2 Mbiri 23:1-21

  • Yehoyada anathandiza kuti Yehoasi akhale mfumu (1-11)

  • Ataliya anaphedwa (12-15)

  • Zinthu zomwe Yehoyada anasintha (16-21)

23  Mʼchaka cha 7, Yehoyada anachita zinthu molimba mtima ndipo anachita pangano ndi atsogoleri a magulu a asilikali 100.+ Atsogoleriwo anali Azariya mwana wa Yerohamu, Isimaeli mwana wa Yehohanani, Azariya mwana wa Obedi, Maaseya mwana wa Adaya ndi Elisafati mwana wa Zikiri. 2  Kenako iwo anazungulira mʼdziko lonse la Yuda ndipo anasonkhanitsa Alevi+ kuchokera mʼmizinda yonse ya Yuda ndi atsogoleri a nyumba za makolo a Isiraeli. Atafika ku Yerusalemu, 3  anthu onsewo anachita pangano+ ndi mfumu mʼnyumba ya Mulungu woona. Ndiyeno Yehoyada anawauza kuti: “Mwana wa mfumu ayenera kulamulira, mogwirizana ndi zimene Yehova analonjeza zokhudza ana a Davide.+ 4  Choncho muchite izi: Mukhale mʼmagulu atatu ofanana a ansembe ndi Alevi, amene adzabwere kudzagwira ntchito+ pa Sabata, ndipo gulu limodzi lidzakhale alonda apamakomo.+ 5  Gulu lina lidzakhale panyumba ya mfumu,+ ndipo gulu lachitatu lidzakhale pageti lotchedwa Maziko. Anthu onse adzakhale pamabwalo a nyumba ya Yehova.+ 6  Musadzalole kuti aliyense alowe mʼnyumba ya Yehova kupatulapo ansembe ndi Alevi amene azidzatumikira.+ Amenewa akhoza kudzalowa chifukwa ndi gulu loyera ndipo anthu onse adzakwaniritsa udindo wawo kwa Yehova pokhala panja. 7  Alevi adzazungulire mfumuyo kumbali zonse atatenga zida ndipo aliyense wofuna kulowa mʼnyumbayo adzaphedwe. Muzidzateteza mfumuyo kulikonse kumene ingapite.” 8  Alevi ndi Ayuda onse anachitadi zimene wansembe Yehoyada analamula. Choncho, aliyense anatenga asilikali ake amene ankagwira ntchito pa Sabata ndi amene ankafunika kupuma pa Sabata,+ popeza wansembe Yehoyada sanawauze kuti azipita.+ 9  Kenako wansembe Yehoyada anapatsa atsogoleri a magulu a asilikali 100+ aja mikondo, zishango zingʼonozingʼono* ndiponso zishango zozungulira zimene zinali za Mfumu Davide,+ zomwe zinali mʼnyumba ya Mulungu woona.+ 10  Iye anauza anthu onse kuti aimirire, aliyense atanyamula zida zake, kuyambira kumanja kwa nyumbayo mpaka kumanzere kwa nyumbayo, pafupi ndi guwa lansembe ndiponso pafupi ndi nyumbayo. Anazungulira mfumuyo kumbali zonse. 11  Kenako anatulutsa mwana wa mfumu+ uja nʼkumuveka chipewa chachifumu nʼkuika mpukutu wa Chilamulo+ cha Mulungu pamutu pake. Choncho anthuwo anamuveka ufumu ndipo Yehoyada ndi ana ake anamudzoza. Kenako anati: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”+ 12  Ataliya atamva phokoso la anthu akuthamanga komanso kutamanda mfumu, nthawi yomweyo anapita kwa anthu amene anali panyumba ya Yehova.+ 13  Atafika anaona mfumu itaimirira pafupi ndi chipilala* pakhomo. Akalonga+ ndi anthu oimba malipenga anali limodzi ndi mfumuyo ndipo anthu onse amʼdzikolo ankasangalala+ komanso ankaimba malipenga. Panalinso oimba ndi zipangizo zoimbira amene ankatsogolera poimba nyimbo zotamanda. Ataliya ataona zimenezi anangʼamba zovala zake nʼkuyamba kukuwa kuti: “Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!” 14  Koma wansembe Yehoyada anatenga atsogoleri a magulu a asilikali 100, omwe anasankhidwa kuti aziyangʼanira asilikali, ndipo anawauza kuti: “Mʼchotseni pakati pa asilikali ndipo aliyense amene angamutsatire mumuphe ndi lupanga!” Wansembeyo anali atanena kuti: “Musamuphere mʼnyumba ya Yehova.” 15  Choncho anamugwira ndipo atafika pakhomo la Geti la Mahatchi lolowera kunyumba ya mfumu, anamuphera pomwepo. 16  Ndiyeno Yehoyada anachita pangano pakati pa iyeyo, anthu onse ndi mfumu, kuti iwo apitiriza kukhala anthu a Yehova.+ 17  Kenako anthu onse anapita kukachisi wa Baala nʼkukamugwetsa+ ndipo anaphwanyaphwanya maguwa ndi mafano ake.+ Anaphanso wansembe wa Baala+ dzina lake Mateni kutsogolo kwa maguwa ansembewo. 18  Kenako Yehoyada anapereka udindo woyangʼanira ntchito zapanyumba ya Yehova kwa ansembe ndi Alevi amene Davide anawaika mʼmagulu panyumba ya Yehova, kuti azipereka nsembe zopsereza za Yehova+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo cha Mose.+ Anawauza kuti azizipereka mosangalala poimba nyimbo motsatira malangizo amene Davide anapereka. 19  Anaikanso alonda apageti+ pafupi ndi mageti a nyumba ya Yehova kuti aliyense wodetsedwa mwa njira ina iliyonse asalowe. 20  Atatero anatenga atsogoleri a magulu a asilikali 100,+ anthu olemekezeka, atsogoleri a anthuwo ndi anthu onse a mʼdzikolo, ndipo anaperekeza mfumuyo kutsetsereka kuchokera kunyumba ya Yehova. Anthuwo anadzera pageti lakumtunda nʼkukafika kunyumba ya mfumu. Kenako mfumuyo anaikhazika pampando wachifumu+ wa ufumuwo.+ 21  Choncho anthu onse amʼdzikolo anasangalala ndipo mumzindawo munali bata chifukwa Ataliya anali ataphedwa ndi lupanga.

Mawu a M'munsi

Nthawi zambiri amene ankanyamula zishango zimenezi anali oponya mivi.
Mʼchilankhulo choyambirira, “chipilala chake.”