2 Mbiri 24:1-27

  • Ulamuliro wa Yehoasi (1-3)

  • Yehoasi anakonza kachisi (4-14)

  • Yehoasi anayamba kulambira mafano (15-22)

  • Yehoasi anaphedwa (23-27)

24  Yehoasi anayamba kulamulira ali ndi zaka 7.+ Iye analamulira zaka 40 ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Beere-seba ndipo dzina lawo linali Zibiya.+  Yehoasi anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova masiku onse a wansembe Yehoyada.+  Yehoyada anapezera Yehoasi akazi awiri ndipo iye anabereka ana aamuna ndi aakazi.  Kenako Yehoasi anafunitsitsa kukonzanso nyumba ya Yehova.+  Choncho anasonkhanitsa ansembe ndi Alevi nʼkuwauza kuti: “Pitani mʼmizinda ya Yuda mukatolere ndalama kwa Aisiraeli onse kuti muzikonzera nyumba ya Mulungu wanu+ chaka ndi chaka. Muchite zimenezi mwachangu.” Koma Aleviwo sanachite zimenezo mwachangu.+  Ndiyeno mfumuyo inaitana mtsogoleri wawo Yehoyada nʼkumufunsa kuti:+ “Bwanji simunauze Alevi kuti abweretse msonkho wopatulika kuchokera kwa anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu? Si paja anayenera kubweretsa msonkho wopatulika wochokera kwa Aisiraeli wogwiritsa ntchito pachihema cha Umboni+ womwe Mose+ mtumiki wa Yehova analamula?  Pajatu ana a Ataliya+ mkazi woipa uja anathyola nyumba ya Mulungu woona,+ ndipo anagwiritsa ntchito zinthu zonse zopatulika zamʼnyumba ya Yehovayo potumikira Abaala.”  Kenako mfumuyo inalamula kuti apange bokosi+ nʼkuliika panja, pageti la nyumba ya Yehova.+  Atatero anauza anthu onse a ku Yuda ndi ku Yerusalemu kuti abweretse kwa Yehova msonkho wopatulika+ umene Mose mtumiki wa Mulungu woona analamula Aisiraeli mʼchipululu. 10  Akalonga onse ndi anthu onse anasangalala,+ ndipo ankabweretsa ndalama za msonkhowo nʼkumaziponya mʼbokosi lija mpaka linadzaza.* 11  Alevi akanyamula bokosilo nʼkupita nalo kwa mfumu ndipo akaona kuti muli ndalama zambiri, mlembi wa mfumu ndi mtumiki wa wansembe wamkulu ankabwera nʼkukhuthula ndalamazo.+ Kenako ankabwezeretsa bokosilo pamalo ake. Ankachita zimenezi tsiku ndi tsiku moti anasonkhetsa ndalama zambiri. 12  Mfumuyo ndi Yehoyada ankapereka ndalamazo kwa anthu amene ankayangʼanira ntchito yokonza nyumba ya Yehova. Anthuwo ankalemba ntchito osema miyala ndi amisiri okonza nyumba ya Yehova+ komanso amisiri a kopa* ndi a zitsulo oti akonze nyumba ya Yehova. 13  Oyangʼanira ntchitowo anayamba ntchito yawo ndipo ntchito yokonza nyumbayo inkayenda bwino moti anakonza nyumba ya Mulungu woona mpaka inakhalanso bwino ndipo anailimbitsa. 14  Atangomaliza ntchitoyo anabweretsa ndalama zimene zinatsala kwa mfumu ndi Yehoyada. Ndalamazo anazigwiritsa ntchito popanga ziwiya zamʼnyumba ya Yehova, ziwiya zogwiritsa ntchito pa utumiki ndi popereka zopereka komanso popanga makapu ndi ziwiya zagolide ndi zasiliva.+ Ndipo ankapereka nsembe zopsereza+ nthawi zonse panyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada. 15  Kenako Yehoyada anamwalira atakalamba komanso atakhutira ndi moyo wake wa zaka zambiri. Iye anamwalira ali ndi zaka 130. 16  Choncho anamuika mʼmanda a mafumu mu Mzinda wa Davide,+ chifukwa anachita zinthu zabwino mu Isiraeli+ zokhudza Mulungu woona ndi nyumba ya Mulungu woonayo. 17  Yehoyada atamwalira, akalonga a Yuda anabwera nʼkudzagwada pamaso pa mfumu ndipo mfumuyo inawamvera. 18  Iwo anasiya nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo awo nʼkuyamba kutumikira mizati yopatulika* ndiponso mafano. Choncho Mulungu anakwiyira kwambiri Yuda ndi Yerusalemu chifukwa cha kulakwa kwawoko. 19  Yehova anapitiriza kuwatumizira aneneri kuti awathandize kubwerera kwa iye. Aneneriwo anapitiriza kuwachenjeza, koma sanamvere.+ 20  Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, Zekariya mwana wa wansembe Yehoyada+ anaimirira pamalo okwera nʼkuyamba kuuza anthuwo kuti: “Mulungu woona wanena kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mukuphwanya malamulo a Yehova? Zinthutu sizikukuyenderani bwino. Poti mwamusiya Yehova, iyenso akusiyani.’”+ 21  Koma anthuwo anamʼkonzera chiwembu+ ndipo anamʼponya miyala pabwalo la nyumba ya Yehova, atalamulidwa ndi mfumu.+ 22  Choncho Mfumu Yehoasi sanakumbukire chikondi chokhulupirika chimene Yehoyada bambo a Zekariya anamusonyeza ndipo anapha mwana wawo, yemwe pakufa ananena kuti: “Yehova aone zimene mwachitazi nʼkukubwezerani.”+ 23  Kumayambiriro kwa chaka chotsatira, asilikali a ku Siriya anabwera kudzamenyana ndi Yehoasi, ndipo analowa mu Yuda ndi Yerusalemu.+ Asilikaliwo anapha akalonga onse+ ndipo zinthu zonse zimene anatenga kumeneko anazitumiza kwa mfumu ya ku Damasiko. 24  Ngakhale kuti asilikali a Siriya amene anabwera anali ochepa, Yehova anapereka mʼmanja mwawo gulu lalikulu kwambiri la asilikali+ chifukwa iwo anasiya Yehova Mulungu wa makolo awo. Choncho Asiriyawo anapereka chiweruzo kwa Yehoasi. 25  Asilikaliwo atachoka (nʼkumusiya atavulala kwambiri), atumiki ake anamʼkonzera chiwembu chifukwa anapha ana* a wansembe Yehoyada.+ Iwo anamuphera pabedi lake.+ Kenako anamuika mʼmanda mu Mzinda wa Davide+ koma sanamuike mʼmanda a mafumu.+ 26  Anthu amene anamʼkonzera chiwembuwo+ ndi awa: Zabadi yemwe mayi ake anali Simeyati, mbadwa ya Amoni, ndiponso Yehozabadi yemwe mayi ake anali Simiriti, wa ku Mowabu. 27  Nkhani zokhudza ana ake, mauthenga ochuluka omutsutsa+ ndiponso ntchito yokonza* nyumba ya Mulungu woona,+ zinalembedwa mʼBuku la Mafumu. Kenako Amaziya mwana wake anakhala mfumu mʼmalo mwake.

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “mpaka aliyense anapereka.”
Kapena kuti, “a mkuwa.”
Kapena kuti, “mwana.” Mwina ananena kuti “ana” polemekeza.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ntchito yokonzanso maziko.”