2 Mbiri 27:1-9

  • Yotamu, mfumu ya Yuda (1-9)

27  Yotamu+ anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Mayi ake dzina lawo linali Yerusa mwana wa Zadoki.+  Yotamu ankachita zoyenera pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira Uziya bambo ake,+ kungoti sanachite makani nʼkukalowa mʼkachisi wa Yehova.+ Koma anthu ankachitabe zoipa.  Iye anamanga geti lakumtunda la nyumba ya Yehova+ ndipo pakhoma la mpanda wa Ofeli anamangapo zinthu zambiri.+  Komanso anamanga mizinda+ mʼdera lamapiri la Yuda+ ndipo mʼdera lankhalango anamangamo nsanja+ ndiponso malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+  Yotamu anamenyana ndi mfumu ya Aamoni+ ndipo patapita nthawi anawagonjetsa. Choncho chaka chimenecho Aamoni anamʼpatsa matalente* a siliva 100, tirigu wokwana miyezo 10,000 ya kori* komanso balere wokwana miyezo 10,000 ya kori. Aamoni anamupatsanso zinthu zimenezi mʼchaka chachiwiri ndi chachitatu.+  Choncho Yotamu anapitiriza kukhala wamphamvu popeza anatsimikiza kuyenda mʼnjira za Yehova Mulungu wake.  Nkhani zina zokhudza Yotamu, zimene anachita komanso nkhondo zonse zomwe anamenya, zinalembedwa mʼBuku la Mafumu a Isiraeli ndi Yuda.+  Iye anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira zaka 16 ku Yerusalemu.+  Kenako Yotamu mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide.+ Ndiyeno mwana wake Ahazi anakhala mfumu mʼmalo mwake.+

Mawu a M'munsi

Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
Muyezo wa kori unali wokwana malita 220. Onani Zakumapeto B14.