2 Mbiri 29:1-36

  • Hezekiya, mfumu ya Yuda (1, 2)

  • Zinthu zimene Hezekiya anasintha (3-11)

  • Kuyeretsa kachisi (12-19)

  • Anayambiranso utumiki wapakachisi (20-36)

29  Hezekiya+ anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 29. Mayi ake dzina lawo linali Abiya mwana wa Zekariya.+  Iye ankachita zoyenera pamaso pa Yehova,+ ngati mmene anachitira Davide kholo lake.+  Mʼchaka choyamba cha ulamuliro wake, mʼmwezi woyamba, iye anatsegula zitseko za nyumba ya Yehova komanso anazikonza.+  Kenako anasonkhanitsa ansembe ndi Alevi pabwalo, mbali yakumʼmawa.  Ndiyeno anawauza kuti: “Tamverani Alevi inu. Dziyeretseni+ ndipo muyeretsenso nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu. Muchotse mʼmalo oyera chinthu chilichonse chodetsedwa.+  Chifukwa makolo athu akhala akuchita zosakhulupirika ndiponso zoipa pamaso pa Yehova Mulungu wathu.+ Iwo anamusiya komanso anasiya chihema chopatulika cha Yehova nʼkumulozetsa nkhongo.+  Anatseka zitseko zapakhonde+ ndiponso anazimitsa nyale.+ Komanso anasiya kupereka nsembe zofukiza+ ndi nsembe zopsereza+ kwa Mulungu wa Isiraeli mʼmalo oyera.  Choncho Yehova anakwiyira kwambiri anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu+ ndipo anawabweretsera tsoka kuti anthu owaona komanso kumva za tsokalo azichita mantha, kudabwa ndiponso kuwaimbira mluzu, ngati mmene mukuonera ndi maso anu.+  Pa chifukwa chimenechi, makolo athu anaphedwa ndi lupanga+ ndipo ana athu aamuna ndi aakazi ndiponso akazi athu anatengedwa kupita ku ukapolo.+ 10  Tsopano ndine wofunitsitsa kuchita pangano ndi Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ kuti mkwiyo wake umene watiyakira uchoke. 11  Ndiyeno inu ana anga, ino ndi nthawi yochita zinthu mwamphamvu, chifukwa Yehova wakusankhani kuti muziima pamaso pake nʼkumamutumikira+ ndiponso kuti muzipereka nsembe zautsi.”+ 12  Zitatero Alevi anaimirira. Alevi ake anali Mahati mwana wa Amasai ndi Yoweli mwana wa Azariya, mbadwa za Kohati.+ Kuchokera kwa mbadwa za Merari,+ panali Kisi mwana wa Abidi ndi Azariya mwana wa Yehaleleli. Kuchokera kwa mbadwa za Gerisoni+ panali Yowa mwana wa Zima ndi Edeni mwana wa Yowa. 13  Kuchokera kwa ana a Elizafana panali Simuri ndi Yeweli. Kuchokera kwa ana a Asafu+ panali Zekariya ndi Mataniya. 14  Kuchokera kwa ana a Hemani+ panali Yehiela ndi Simeyi. Kuchokera kwa ana a Yedutuni+ panali Semaya ndi Uziyeli. 15  Kenako anasonkhanitsa abale awo nʼkudziyeretsa. Ndiyeno anabwera kudzayeretsa nyumba ya Yehova mogwirizana ndi lamulo la mfumu potsatira mawu a Yehova.+ 16  Kenako ansembe analowa mʼnyumba ya Yehova kukayeretsamo, ndipo anatulutsa zonyansa zonse zimene anazipeza mʼkachisi wa Yehova nʼkupita nazo pabwalo+ la nyumba ya Yehova. Ndiyeno Alevi anazitenga nʼkupita nazo kunja kuchigwa cha Kidironi.+ 17  Anayamba kuyeretsa pa tsiku loyamba la mwezi woyamba ndipo pa tsiku la 8 la mweziwo anafika pakhonde la nyumba ya Yehova.+ Anayeretsa nyumba ya Yehovayo masiku 8 ndipo pa tsiku la 16 la mwezi woyamba anamaliza ntchitoyo. 18  Atatero anapita kumene kunali Mfumu Hezekiya nʼkukaiuza kuti: “Tayeretsa nyumba yonse ya Yehova, guwa lansembe zopsereza+ ndi ziwiya zake zonse.+ Tayeretsanso tebulo loikapo mkate wosanjikiza*+ ndi ziwiya zake zonse. 19  Ziwiya zonse zimene Mfumu Ahazi anasiya kuzigwiritsira ntchito mu ulamuliro wake pamene ankachita zosakhulupirika,+ tazikonza nʼkuziyeretsa+ ndipo zili pafupi ndi guwa lansembe la Yehova.” 20  Mfumu Hezekiya anadzuka mʼmawa kwambiri nʼkusonkhanitsa akalonga a mzindawo ndipo anapita kunyumba ya Yehova. 21  Iwo anabweretsa ngʼombe zamphongo 7, nkhosa zamphongo 7, ana a nkhosa amphongo 7 ndi mbuzi zamphongo 7 kuti azipereke nsembe yamachimo ya ufumuwo, ya malo opatulika ndi ya Yuda.+ Choncho Hezekiya anauza mbadwa za Aroni, zomwe zinali ansembe, kuti apereke nsembeyo paguwa lansembe la Yehova. 22  Iwo anapha ngʼombezo+ ndipo ansembe anatenga magazi ake nʼkuwaza paguwa lansembe.+ Kenako anapha nkhosa zamphongo zija nʼkuwaza magazi ake paguwa lansembe. Atatero anapha ana a nkhosa amphongo aja nʼkuwaza magazi ake paguwa lansembe. 23  Kenako anabweretsa mbuzi zamphongo za nsembe yamachimo zija pafupi ndi mfumu ndi gulu lonse la anthu ndipo iwo anaika manja awo pambuzizo. 24  Kenako ansembe anazipha nʼkuzipereka nsembe yamachimo ndipo anaika magazi ake paguwa lansembe kuti aphimbe machimo a Aisiraeli onse, popeza mfumu inanena kuti nsembe yopsereza ndi yamachimoyo ikhale ya Aisiraeli onse. 25  Pa nthawiyi, Hezekiya anaika Alevi panyumba ya Yehova atanyamula zinganga, zoimbira za zingwe ndi azeze.+ Iwo ankatsatira malamulo oimbira a Davide,+ a Gadi+ yemwe anali wamasomphenya wa mfumu, ndiponso a mneneri Natani,+ chifukwa malamulowo anachokera kwa Yehova kudzera mwa aneneri ake. 26  Choncho Aleviwo anaimirira atanyamula zipangizo zoimbira za Davide. Iwo anaimirira pamodzi ndi ansembe omwe ananyamula malipenga.+ 27  Kenako Hezekiya analamula kuti apereke nsembe yopsereza paguwa lansembe.+ Atayamba kupereka nsembeyo, anayamba kuimba nyimbo ya Yehova ndiponso malipenga motsatira zipangizo zoimbira za Davide mfumu ya Isiraeli. 28  Gulu lonse la anthulo linagwada nʼkuwerama pamene nyimboyo inkaimbidwa ndiponso pamene malipenga ankaimbidwa. Ndipo zonsezi zinapitirira mpaka anamaliza kupereka nsembe yopsereza. 29  Atangomaliza kupereka nsembeyo, mfumu ndi anthu onse amene anali nawo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo kufika pansi. 30  Ndiyeno mfumu Hezekiya ndi akalonga anauza Alevi kuti atamande Yehova ndi mawu a Davide+ komanso a wamasomphenya Asafu.+ Choncho iwo anatamanda Mulungu mosangalala ndipo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo kufika pansi. 31  Kenako Hezekiya anati: “Tsopano popeza mwapatulidwa kuti muzitumikira Yehova, bweretsani nsembe zoyamikira ndi nsembe zina kunyumba ya Yehova.” Ndiyeno gulu la anthuwo linayamba kubweretsa nsembe zoyamikira ndi nsembe zina, ndipo aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa anabweretsa nsembe zopsereza.+ 32  Nsembe zopsereza zimene gulu la anthuwo linabweretsa zinalipo ngʼombe 70, nkhosa zamphongo 100 ndi ana a nkhosa amphongo 200. Zonsezi anazipereka kwa Yehova monga nsembe yopsereza.+ 33  Ndipo zopereka zopatulika zimene anabweretsa zinali ngʼombe 600 ndi nkhosa 3,000. 34  Koma ansembe anali ochepa kwambiri moti sakanatha kusenda nyama zonse za nsembe zopsereza. Choncho abale awo Alevi anawathandiza+ mpaka pamene ntchitoyo inatha ndiponso pamene ansembewo anadziyeretsa,+ chifukwa Alevi ankaona kuti kudziyeretsa nʼkofunika kwambiri kuposa mmene ansembe ankaonera. 35  Komanso, panali nsembe zopsereza zambiri+ ndiponso mafuta ambiri a nsembe zamgwirizano.+ Nazonso nsembe zachakumwa zimene zinaperekedwa limodzi ndi nsembe zopserezazo zinali zambiri.+ Choncho utumiki wapanyumba ya Yehova unayambiranso kuchitika. 36  Ndipo Hezekiya ndi anthu onse anasangalala chifukwa cha zimene Mulungu woona anachitira anthuwo+ chifukwa zinthuzo zinachitika mosayembekezereka.

Mawu a M'munsi

Umenewu unali mkate wachionetsero.