2 Mbiri 30:1-27

  • Hezekiya anachita Pasika (1-27)

30  Hezekiya anatumiza uthenga kwa Aisiraeli+ ndi Ayuda onse ndipo analembera makalata anthu a ku Efuraimu ndi ku Manase+ kuti abwere kunyumba ya Yehova ku Yerusalemu kudzachitira Pasika Yehova Mulungu wa Isiraeli.+  Koma mfumuyo, akalonga ake ndi gulu lonse la anthu ku Yerusalemu anagwirizana zoti achite Pasikayo mwezi wachiwiri.+  Iwo sanathe kuchita Pasikayo pa nthawi imene ankayenera kuchita+ chifukwa ansembe amene anadziyeretsa+ anali osakwanira komanso anthu anali asanasonkhane ku Yerusalemu.  Zimenezi zinasangalatsa mfumu komanso gulu lonselo.  Choncho anagwirizana kuti alengeze zimenezi mu Isiraeli monse kuyambira ku Beere-seba mpaka ku Dani+ kuti anthu abwere ku Yerusalemu adzachitire Pasika Yehova Mulungu wa Isiraeli, chifukwa anthuwo anali asanasonkhanepo kuti achite Pasika mogwirizana ndi zimene zinalembedwa.+  Ndiyeno asilikali othamanga amene anatenga makalata ochokera kwa mfumu ndi kwa akalonga ake, anapita mu Isiraeli ndi mu Yuda monse chifukwa mfumu inalamula kuti: “Inu Aisiraeli, bwererani kwa Yehova Mulungu wa Abulahamu, Isaki ndi Isiraeli, kuti iye abwerere kwa anthu amene anatsala, omwe anapulumuka mʼmanja mwa mafumu a Asuri.+  Musakhale ngati makolo anu ndi abale anu amene anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wa makolo awo, moti anawachititsa kukhala chinthu chodabwitsa ngati mmene mukuoneramu.+  Ndiye musakhale ankhutukumve ngati makolo anu.+ Gonjerani Yehova ndipo mupite kunyumba yake yopatulika+ imene waiyeretsa mpaka kalekale. Tumikirani Yehova Mulungu wanu kuti asiye kukukwiyirani kwambiri.+  Mukabwerera kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzachitiridwa chifundo ndi anthu amene anawagwira+ ndipo adzawalola kubwerera mʼdzikoli.+ Chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi wachisomo komanso wachifundo+ ndipo sadzayangʼana kumbali mukabwerera kwa iye.”+ 10  Choncho asilikali othamangawo anapita mʼmizinda yonse mʼdera la Efuraimu ndi Manase+ mpaka ku Zebuloni. Koma anthuwo ankangowanyoza ndiponso kuwaseka.+ 11  Komabe anthu ena ochokera ku Aseri, ku Manase ndi ku Zebuloni anadzichepetsa nʼkubwera ku Yerusalemu.+ 12  Komanso dzanja la Mulungu woona linathandiza anthu a ku Yuda kukhala ogwirizana, kuti amvere zimene mfumu ndi akalonga anawalamula motsatira mawu a Yehova. 13  Anthu ambirimbiri anasonkhana ku Yerusalemu kuti achite Chikondwerero cha Mkate Wopanda Zofufumitsa+ mʼmwezi wachiwiri+ ndipo linali gulu lalikulu kwambiri. 14  Kenako iwo anakachotsa maguwa ansembe amene anali mu Yerusalemu.+ Anachotsanso maguwa onse a nsembe zofukiza+ nʼkukawataya kuchigwa cha Kidironi. 15  Atatero anapha nyama ya Pasika pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Ansembe ndi Alevi anachita manyazi moti anadziyeretsa nʼkubweretsa nsembe zopsereza kunyumba ya Yehova. 16  Iwo anaimirira mʼmalo mwawo mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose munthu wa Mulungu woona. Kenako ansembe anawaza paguwa lansembe magazi+ amene analandira kwa Alevi. 17  Pagululo panali anthu ambiri amene sanadziyeretse. Choncho Alevi ndi amene ankapha nyama za Pasika za anthu onse amene sanali oyera,+ kuti awayeretse kwa Yehova. 18  Anthu ambiri makamaka ochokera ku Efuraimu, ku Manase,+ ku Isakara ndi ku Zebuloni sanadziyeretse koma anadyabe Pasikayo, zomwe zinali zosagwirizana ndi zimene zinalembedwa. Ndiyeno Hezekiya anawapempherera kuti: “Inu Yehova, ndinu wabwino,+ musakwiyire 19  aliyense amene wakonza mtima wake kuti afunefune inu Mulungu woona+ Yehova, Mulungu wa makolo ake, ngakhale kuti sanadziyeretse mogwirizana ndi malamulo okhudza kudziyeretsa.”+ 20  Yehova anamvera Hezekiya ndipo anakhululukira anthuwo. 21  Choncho Aisiraeli amene anali ku Yerusalemu anachita Chikondwerero cha Mkate Wopanda Zofufumitsa+ mosangalala kwambiri kwa masiku 7.+ Alevi ndi ansembe ankatamanda Yehova tsiku ndi tsiku nʼkumaimbira Yehova mokweza ndi zipangizo zawo.+ 22  Kuwonjezera pamenepo, Hezekiya analankhula ndi Alevi onse amene ankachita zinthu mwanzeru potumikira Yehova ndiponso anawalimbikitsa. Anthuwo anachita phwando kwa masiku 7.+ Ankapereka nsembe zamgwirizano+ komanso kuthokoza Yehova Mulungu wa makolo awo. 23  Ndiyeno gulu lonse la anthulo linagwirizana kuti lichitenso phwando masiku ena 7. Choncho anachita phwandolo mosangalala masiku enanso 7.+ 24  Hezekiya mfumu ya Yuda anapereka ku mpingowo ngʼombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa 7,000. Akalonganso anapereka ku mpingowo ngʼombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa 10,000+ ndipo ansembe ambiri ankadziyeretsa.+ 25  Gulu lonse la Ayuda, ansembe, Alevi, gulu lonse la anthu amene anachokera ku Isiraeli+ komanso alendo+ amene anachokera mʼdziko la Isiraeli ndiponso amene ankakhala mʼdziko la Yuda, anapitiriza kusangalala. 26  Choncho anthu anasangalala kwambiri ku Yerusalemu, chifukwa kuyambira mʼmasiku a Solomo mwana wa Davide mfumu ya Isiraeli, zinthu ngati zimenezi zinali zisanachitike ku Yerusalemu.+ 27  Pomaliza, Alevi omwe anali ansembe anaimirira nʼkudalitsa anthuwo.+ Mulungu anamva mawu awo ndipo pemphero lawo linafika kumwamba, kumalo oyera omwe iye amakhala.

Mawu a M'munsi