2 Mbiri 31:1-21

  • Hezekiya anathetsa kulambira mafano (1)

  • Ansembe ndi Alevi anayamba kuthandizidwa (2-21)

31  Atangomaliza kuchita zonsezi, Aisiraeli onse amene anali pamenepo anapita kumizinda ya Yuda nʼkukaphwanya zipilala zopatulika,+ kugwetsa mizati yopatulika,*+ malo okwezeka+ ndiponso maguwa ansembe+ mʼmadera onse a Yuda, Benjamini, Efuraimu ndi Manase+ mpaka kuzimaliza zonse. Atatero, Aisiraeli anabwerera kumizinda yawo, aliyense kumalo ake.  Kenako Hezekiya anasankha ansembe mogwirizana ndi magulu awo+ komanso Alevi mogwirizana ndi magulu awo.+ Gulu lililonse la ansembe ndiponso la Alevi analiika mogwirizana ndi utumiki wawo+ wokhudza nsembe zopsereza ndi nsembe zamgwirizano. Anawasankha kuti azitumikira Mulungu, kumuyamika ndiponso kumutamanda mʼmageti a kachisi wa Yehova.+  Kuchokera pa katundu wake, mfumuyo inapereka nsembe zopsereza+ zamʼmawa ndi zamadzulo,+ nsembe zopsereza za Masabata,+ za masiku amene mwezi watsopano waoneka+ ndi za pa nthawi yachikondwerero,+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo cha Yehova.  Kuwonjezera pamenepo, Hezekiya anauza anthu a ku Yerusalemu kuti azipereka gawo loyenera kupita kwa ansembe ndi Alevi+ nʼcholinga choti iwo azitsatira mosamala lamulo la Yehova.  Aisiraeli atangomva zimenezi, anapereka zinthu zambiri zoyambirira kukolola monga mbewu, vinyo watsopano, mafuta,+ uchi ndi zokolola zonse zakumunda+ ndipo anapereka mowolowa manja chakhumi cha zinthu zonse.+  Aisiraeli ndi Ayuda amene ankakhala mʼmizinda ya ku Yuda anabweretsanso chakhumi cha ngʼombe, nkhosa ndiponso cha zinthu zopatulika+ zimene anaziyeretsa kuti zikhale za Yehova Mulungu wawo. Anabweretsa zinthu zimenezi zambiri nʼkuziunjika milumilu.  Anayamba kuunjika milu ya zoperekazo mʼmwezi wachitatu+ ndipo anamaliza mʼmwezi wa 7.+  Hezekiya ndi akalonga atabwera nʼkuona miluyo, anatamanda Yehova ndiponso anadalitsa anthu ake Aisiraeli.  Hezekiya anafunsa ansembe ndi Alevi za miluyo. 10  Ndiyeno Azariya, wansembe wamkulu wa nyumba ya Zadoki, anamuyankha kuti: “Kuyambira pamene anthu anayamba kubweretsa zopereka mʼnyumba ya Yehova,+ anthu akhala akudya mpaka kukhuta ndipo pali zotsala zambiri, chifukwa Yehova wadalitsa anthu ake moti zonse mukuzionazi nʼzotsala.”+ 11  Hezekiya atamva zimenezi, anawauza kuti akonze zipinda zosungira katundu+ mʼnyumba ya Yehova ndipo iwo anazikonzadi. 12  Anthuwo anapitiriza kubweretsa zopereka mokhulupirika, chakhumi+ ndi zinthu zopatulika. Konaniya Mlevi anaikidwa kuti akhale woyangʼanira zinthu zonsezi ndipo Simeyi mchimwene wake anali wachiwiri wake. 13  Yehiela, Azaziya, Nahati, Asaheli, Yerimoti, Yozabadi, Elieli, Isimakiya, Mahati ndi Benaya ankathandiza Konaniya ndi Simeyi mchimwene wake motsatira lamulo la Mfumu Hezekiya. Azariya anali mtsogoleri wa nyumba ya Mulungu woona. 14  Kore, mwana wa Imuna mlonda wa fuko la Levi wapageti lakumʼmawa,+ ankayangʼanira zopereka zaufulu+ za Mulungu woona ndiponso ankagawa zinthu zoperekedwa kwa Yehova+ ndi zinthu zopatulika koposa.+ 15  Iye ankayangʼanira Edeni, Miniyamini, Yesuwa, Semaya, Amariya ndi Sekaniya, mʼmizinda ya ansembe+ amene anali pa maudindo chifukwa cha kukhulupirika kwawo. Iwowa ankagawa zinthu kumagulu a abale awo ndipo ankawagawira mofanana,+ kaya akhale wamkulu kapena wamngʼono. 16  Kuwonjezera pamenepo, ankagawiranso amuna oyambira zaka zitatu kupita mʼtsogolo amene anali pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo. Amuna amenewa ankabwera tsiku ndi tsiku kudzatumikira kunyumba ya Yehova komanso kudzagwira ntchito ya magulu awo. 17  Mndandanda wa mayina a ansembe potengera makolo awo unali wotsatira nyumba ya makolo awo+ ngati mmene unalili mndandanda wa mayina a Alevi azaka 20 kupita mʼtsogolo,+ mogwirizana ndi ntchito za magulu awo.+ 18  Mndandandawo unali wa ana awo onse aangʼono, akazi awo ndiponso ana awo aamuna ndi aakazi komanso mbumba yawo yonse, popeza anadziyeretsa kuti achite utumiki wopatulika, pa ntchito imene ankagwira chifukwa cha kukhulupirika kwawo. 19  Panalinso mndandanda wa mayina a ansembe, mbadwa za Aroni, amene ankakhala kumalo odyetserako ziweto ozungulira mizinda yawo.+ Mʼmizinda yonseyo, amuna anasankhidwa pochita kuwatchula mayina, kuti azipereka chakudya kwa mwamuna aliyense pakati pa ansembe ndiponso kwa aliyense amene anali pamndandanda wa mayina a Alevi motsatira makolo awo. 20  Hezekiya anachita zimenezi ku Yuda konse ndipo anapitiriza kuchita zabwino, zoyenera komanso zokhulupirika pamaso pa Yehova Mulungu wake. 21  Anagwira ndi mtima wake wonse ntchito iliyonse imene anaiyamba pofunafuna Mulungu wake, kaya ndi yokhudza utumiki wapanyumba ya Mulungu woona+ kapena Chilamulo, ndipo zinthu zinamuyendera bwino.

Mawu a M'munsi