2 Mbiri 32:1-33

  • Senakeribu anaopseza Yerusalemu (1-8)

  • Senakeribu ananyoza Yehova (9-19)

  • Mngelo anapha asilikali a Asiriya (20-23)

  • Hezekiya anadwala kenako anadzikuza (24-26)

  • Zimene Hezekiya anachita; imfa ya Hezekiya (27-33)

32  Pambuyo pa zimenezi ndiponso pambuyo pa zinthu zokhulupirika+ zimene Hezekiya anachitazi, Senakeribu mfumu ya Asuri anabwera kuti adzaukire Yuda. Iye anamanga misasa pafupi ndi mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri nʼcholinga choti alowe nʼkulanda mizindayo.+  Hezekiya ataona kuti Senakeribu wabwera kuti adzamenyane ndi anthu a ku Yerusalemu,  anakambirana ndi akalonga ndi asilikali ake ndipo anaganiza zotseka akasupe a madzi amene anali kunja kwa mzindawo,+ moti iwo anamuthandiza.  Anthu ambiri anasonkhana ndipo anatseka akasupe onse ndiponso mtsinje umene unkadutsa kumeneko. Iwo anati: “Sitikufuna kuti mafumu a Asuri akabwera adzakhale ndi madzi ambiri.”  Kuwonjezera pamenepo, iye anachita zinthu mwakhama ndipo anamanga mpanda umene unagumuka. Anamanganso nsanja mʼmalo osiyanasiyana pamwamba pa mpandawo ndipo kunja kwake anamangako mpanda wina. Anakonzanso Chimulu cha Dothi*+ cha mu Mzinda wa Davide ndipo anapanga zishango ndi zida zina zambiri.  Kenako anasankha akuluakulu a asilikali kuti aziyangʼanira anthu, ndipo anawasonkhanitsa pabwalo lapageti la mzindawo. Kumeneko iye anawalimbikitsa kuti:  “Limbani mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu. Musachite mantha kapena kuopa mfumu ya Asuri+ ndi gulu lalikulu limene ali nalo, chifukwa ife tili ndi ambiri kuposa amene ali ndi mfumuyo.+  Iye akudalira mphamvu za anthu, koma ife tili ndi Yehova Mulungu wathu kuti atithandize ndi kutimenyera nkhondo zathu.”+ Anthuwo analimbikitsidwa kwambiri ndi mawu amene Hezekiya mfumu ya Yuda inanenawa.+  Kenako Senakeribu mfumu ya Asuri ali ku Lakisi+ pamodzi ndi asilikali ake onse, anatuma anthu ku Yerusalemu kwa Hezekiya mfumu ya Yuda ndi kwa anthu onse a ku Yudeya omwe anali ku Yerusalemu.+ Anawatuma kukanena kuti: 10  “Senakeribu mfumu ya Asuri yanena kuti, ‘Kodi mukudalira chiyani kuti muzingokhalabe mu Yerusalemu, mzindawu utazunguliridwa?+ 11  Hezekiyatu akukupusitsani pokuuzani kuti: “Yehova Mulungu wathu atipulumutsa mʼmanja mwa mfumu ya Asuri,”+ ndipo mufa ndi njala ndiponso ludzu. 12  Kodi si Hezekiya yemweyo amene anachotsa malo okwezeka+ a Mulungu wanu ndi maguwa ake ansembe+ kenako nʼkuuza anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu kuti: “Muziwerama pamaso pa guwa lansembe limodzi lokha ndipo nsembe zanu muzipereka pamenepo”?+ 13  Kodi simukudziwa zimene ineyo ndi makolo anga akale tinachita kwa anthu onse a mayiko ena?+ Kodi milungu ya anthu a mitundu inayo inatha kupulumutsa mayiko awo mʼmanja mwanga?+ 14  Pa milungu ya mitundu yomwe makolo anga anaiwonongayi, ndi mulungu uti amene anatha kupulumutsa anthu ake mʼmanja mwanga, kuti Mulungu wanu athe kukupulumutsani mʼmanja mwanga?+ 15  Musalole kuti Hezekiya akupusitseni kapena kukusocheretsani chonchi.+ Musamukhulupirire, chifukwa palibe mulungu wa ufumu uliwonse kapena wa mtundu uliwonse amene anatha kupulumutsa anthu ake mʼmanja mwanga ndiponso mʼmanja mwa makolo anga akale. Ndiye mukuganiza kuti Mulungu wanu angakupulumutseni mʼmanja mwanga?’”+ 16  Atumiki a Senakeribuwo analankhula zinthu zinanso zonyoza Yehova Mulungu woona ndi Hezekiya mtumiki wake. 17  lye analembanso makalata+ onyoza Yehova Mulungu wa Isiraeli+ komanso omunenera zachipongwe kuti: “Mofanana ndi milungu ya anthu amʼmayiko ena, imene sinapulumutse anthu ake mʼmanja mwanga,+ Mulungu wa Hezekiya sapulumutsa anthu ake mʼmanja mwanga.” 18  Iwo anapitiriza kulankhula mokuwa mʼchilankhulo cha Ayuda, kwa anthu a ku Yerusalemu amene anali pamwamba pa mpanda, kuti awaopseze komanso kuwachititsa mantha nʼcholinga choti alande mzindawo.+ 19  Ananyoza Mulungu wa anthu a ku Yerusalemu ngati mmene ananyozera milungu ya anthu apadziko lapansi, yomwe ndi yopangidwa ndi manja a anthu. 20  Koma Mfumu Hezekiya ndi mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi, ankapempherera nkhani imeneyi ndiponso kufuulira Mulungu kumwamba kuti awathandize.+ 21  Ndiyeno Yehova anatumiza mngelo yemwe anapha msilikali aliyense wamphamvu,+ mtsogoleri ndiponso mkulu wa asilikali aliyense mumsasa wa mfumu ya Asuri, moti mfumuyo inabwerera kwawo mwamanyazi. Kenako inalowa mʼkachisi wa mulungu wake ndipo ena mwa ana ake anaipha ndi lupanga mʼkachisimo.+ 22  Choncho Yehova anapulumutsa Hezekiya ndi anthu a ku Yerusalemu mʼmanja mwa Senakeribu mfumu ya Asuri komanso mʼmanja mwa ena onse, ndipo anawapatsa mpumulo mʼdziko lonselo. 23  Zimenezi zitachitika, anthu ambiri ankabweretsa mphatso kwa Yehova ku Yerusalemu ndi zinthu zabwino kwambiri kwa Hezekiya mfumu ya Yuda,+ moti iye ankalemekezedwa ndi anthu a mitundu yonse. 24  Mʼmasiku amenewo, Hezekiya anadwala mpaka kutsala pangʼono kufa. Iye anapemphera kwa Yehova+ ndipo anamuyankha komanso anamupatsa chizindikiro.+ 25  Koma Hezekiya sanasonyeze kuyamikira zabwino zimene anamuchitira, moti mtima wake unayamba kudzikuza ndipo zimenezi zinachititsa kuti Mulungu amukwiyire iyeyo, Yuda ndiponso Yerusalemu. 26  Komabe, Hezekiya anadzichepetsa nʼkusintha mtima wake wodzikuza.+ Anadzichepetsa limodzi ndi anthu a ku Yerusalemu ndipo Yehova sanawasonyeze mkwiyo wake mʼmasiku a Hezekiya.+ 27  Hezekiya anakhala ndi chuma chambiri ndiponso ulemerero.+ Anamanga nyumba zake zosungiramo+ siliva, golide, miyala yamtengo wapatali, mafuta a basamu, zishango ndiponso zinthu zonse zabwino kwambiri. 28  Anamanganso mosungira zokolola, vinyo watsopano ndi mafuta, komanso makola a ziweto zosiyanasiyana. 29  Analinso ndi mizinda ndiponso ziweto zosiyanasiyana monga nkhosa ndi ngʼombe zambiri, chifukwa Mulungu anamʼpatsa katundu wambiri. 30  Hezekiya ndi amene anatseka kasupe wakumtunda wa madzi+ a ku Gihoni+ ndipo anawapatutsira kumunsi, chakumadzulo, ku Mzinda wa Davide.+ Ntchito iliyonse imene Hezekiya ankagwira inkamuyendera bwino. 31  Koma akalonga a ku Babulo atatumiza anthu kuti akamufunse za chizindikiro+ chimene chinachitika mʼdzikolo,+ Mulungu woona anamusiya kuti amuyese+ nʼcholinga choti adziwe zonse zimene zinali mumtima mwake.+ 32  Nkhani zina zokhudza Hezekiya ndiponso mmene anasonyezera chikondi chokhulupirika,+ zinalembedwa mʼmasomphenya a mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi omwe ali mʼBuku la Mafumu a Yuda ndi Isiraeli.+ 33  Kenako Hezekiya, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda pachitunda chopita kumanda a ana a Davide.+ Ndipo Ayuda onse ndi anthu a ku Yerusalemu anamulemekeza kwambiri pa maliro ake. Ndiyeno mwana wake Manase anakhala mfumu mʼmalo mwake.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Milo.” Amenewa ndi mawu a Chiheberi otanthauza “kudzaza.”