2 Mbiri 34:1-33

  • Yosiya, mfumu ya Yuda (1, 2)

  • Zinthu zomwe Yosiya anasintha (3-13)

  • Anapeza buku la Chilamulo (14-21)

  • Hulida analosera za tsoka (22-28)

  • Yosiya anawerengera anthu buku (29-33)

34  Yosiya+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 8 ndipo analamulira zaka 31 ku Yerusalemu.+  Iye anachita zoyenera pamaso pa Yehova ndipo anayenda mʼnjira za Davide kholo lake. Sanapatukire kumanja kapena kumanzere.  Mʼchaka cha 8 cha ulamuliro wake, akadali mnyamata, Yosiya anayamba kufunafuna Mulungu wa Davide kholo lake.+ Mʼchaka cha 12 anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu+ pochotsa malo okwezeka,+ mizati yopatulika,* zifaniziro zogoba+ ndiponso zifaniziro zachitsulo.  Kuwonjezera pamenepo, anthu anagwetsa maguwa ansembe a Abaala pamaso pake, ndipo iye anagumula zofukizira zimene zinali pamwamba pa maguwawo. Mizati yopatulika,* zifaniziro zogoba ndi zifaniziro zachitsulo, anaziphwanya nʼkuziperapera. Fumbi lake analiwaza pamanda a anthu amene ankapereka nsembe kwa zinthu zimenezi.+  Mafupa a ansembe anawatentha pamaguwa awo ansembe.+ Choncho Yosiya anayeretsa Yuda ndi Yerusalemu.  Komanso mʼmizinda ya Manase, Efuraimu,+ Simiyoni, mpaka Nafitali ndi mʼmabwinja onse ozungulira mizindayi,  Yosiya anagwetsamo maguwa ansembe. Anaphwanya mizati yopatulika* ndi zifaniziro zogoba+ nʼkuziperapera ndipo anagumula zofukizira zonse mʼdziko lonse la Isiraeli.+ Atatero anabwerera ku Yerusalemu.  Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wake, atayeretsa dzikolo ndiponso kachisi,* iye anatuma Safani+ mwana wa Azaliya, Maaseya mkulu wa mzinda ndi Yowa mwana wa Yowahazi wolemba zochitika, kuti akakonze nyumba ya Yehova Mulungu wake.+  Iwo anapita kwa Hilikiya mkulu wa ansembe nʼkumupatsa ndalama zimene anthu ankabweretsa kunyumba ya Mulungu, zimene Alevi omwe anali alonda apakhomo, anatolera kwa anthu a fuko la Manase, la Efuraimu, kwa Aisiraeli onse,+ kwa Ayuda onse, anthu a fuko la Benjamini ndiponso kwa anthu onse okhala ku Yerusalemu. 10  Kenako ndalamazo anazipereka kwa anthu amene anasankhidwa kuti aziyangʼanira ntchito panyumba ya Yehova. Ndiyeno anthu amene ankagwira ntchito panyumba ya Yehova anagwiritsa ntchito ndalamazo pokonza nyumbayo. 11  Anthu ogwira ntchitowa anapereka ndalamazo kwa amisiri ndi kwa omanga nyumba kuti agulire miyala yosema komanso matabwa olimbitsira nyumba ndiponso kuti akhome mitanda ya nyumba zimene mafumu a Yuda anazilekerera kuti ziwonongeke.+ 12  Anthuwo anagwira ntchitoyo mokhulupirika.+ Amene ankawayangʼanira anali Yahati ndi Obadiya, Alevi omwe anali mbadwa za Merari+ ndiponso Zekariya ndi Mesulamu mbadwa za Kohati.+ Aliyense wa Aleviwo, anali katswiri woimba+ 13  ndipo ankayangʼanira anthu onyamula katundu ndi anthu onse ogwira ntchito zosiyanasiyana. Panalinso Alevi amene anali alembi, akapitawo ndi alonda apageti.+ 14  Pamene ankatulutsa ndalama zimene zinabwera kunyumba ya Yehova,+ wansembe Hilikiya anapeza buku la Chilamulo cha Yehova+ loperekedwa kudzera mwa Mose.+ 15  Choncho Hilikiya anauza Safani mlembi kuti: “Ndapeza buku la Chilamulo mʼnyumba ya Yehova!” Atatero Hilikiya anapereka bukulo kwa Safani. 16  Ndiyeno Safani anapititsa bukulo kwa mfumu nʼkunena kuti: “Atumiki anu akugwira ntchito yonse imene apatsidwa. 17  Iwo akhuthula ndalama zimene azipeza mʼnyumba ya Yehova nʼkuzipereka kwa amuna osankhidwa ndiponso kwa anthu amene akugwira ntchito.” 18  Kenako Safani mlembi anauza mfumuyo kuti: “Wansembe Hilikiya wandipatsa buku linalake.”+ Ndiyeno Safani anayamba kuwerengera mfumu bukulo.+ 19  Mfumuyo itangomva mawu a Chilamulowo, inangʼamba zovala zake.+ 20  Kenako mfumuyo inalamula Hilikiya, Ahikamu+ mwana wa Safani, Abidoni mwana wa Mika, Safani mlembi ndi Asaya mtumiki wa mfumu, kuti: 21  “Pitani mukafunsire kwa Yehova mʼmalo mwa ineyo ndiponso mʼmalo mwa anthu amene atsala mu Isiraeli ndi mu Yuda. Mukafunse zokhudza mawu amʼbuku limene lapezekali, chifukwa mkwiyo umene Yehova adzatisonyeze ndi waukulu, popeza makolo athu sanasunge mawu a Yehova moti sanatsatire zonse zimene zinalembedwa mʼbukuli.”+ 22  Choncho Hilikiya ndi anthu amene mfumu inawatuma anapita kukalankhula ndi Hulida mneneri wamkazi.+ Hulida anali mkazi wa Salumu yemwe ankayangʼanira mosungira zovala, mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi. Hulidayo ankakhala Kumbali Yatsopano ya mzinda wa Yerusalemu.+ 23  Iye anawauza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Munthu amene wakutumaniyo mukamuuze kuti: 24  “Yehova wanena kuti, ‘Ndibweretsa tsoka pamalo ano ndiponso kwa anthu ake,+ pokwaniritsa matemberero onse amene analembedwa mʼbuku+ limene anawerenga pamaso pa mfumu ya Yuda, 25  chifukwa chakuti andisiya+ nʼkumakapereka nsembe zautsi kwa milungu ina kuti andikwiyitse+ ndi ntchito zonse za manja awo, ndibweretsa mkwiyo wanga pamalo ano ndipo suzimitsidwa.’”+ 26  Koma kwa mfumu ya Yuda imene yakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova, mukanene kuti, “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ponena za mawu amene wamvawo,+ 27  chifukwa chakuti mtima wako unali womvera* ndipo unadzichepetsa pamaso pa Mulungu utamva mawu ake okhudza malo ano ndi anthu ake komanso unadzichepetsa pamaso panga nʼkungʼamba zovala zako ndi kulira pamaso panga, inenso ndamva,+ watero Yehova. 28  Nʼchifukwa chake ndidzakuika mʼmanda a makolo ako ndipo udzaikidwa mʼmanda ako mwamtendere. Maso ako sadzaona tsoka lonse lomwe ndidzabweretse pamalo ano ndi anthu ake.’”’”+ Kenako iwo anakauza mfumuyo zimenezi. 29  Choncho mfumuyo inatumiza uthenga kwa akulu onse a Yuda ndi Yerusalemu ndipo inawasonkhanitsa pamodzi.+ 30  Zitatero, mfumuyo inapita kunyumba ya Yehova limodzi ndi amuna onse a ku Yuda, anthu okhala ku Yerusalemu, ansembe, Alevi ndi anthu onse, ana ndi akulu omwe. Mfumuyo inawawerengera mawu onse amʼbuku la pangano limene linapezeka mʼnyumba ya Yehova.+ 31  Mfumuyo inaimirira pamalo ake ndipo inachita* pangano+ pamaso pa Yehova, kuti idzatsatira Yehova ndi kusunga malamulo ake ndiponso zikumbutso zake. Inanena kuti idzachita zimenezi ndi mtima wake wonse+ ndi moyo wake wonse potsatira mawu a pangano olembedwa mʼbukulo.+ 32  Komanso mfumuyo inachititsa kuti anthu onse amene anali ku Yerusalemu ndi ku Benjamini avomereze panganolo. Ndipo anthu okhala ku Yerusalemuwo anachita mogwirizana ndi pangano la Mulungu, Mulungu wa makolo awo.+ 33  Kenako Yosiya anachotsa zonyansa* zonse mʼmadera onse a Aisiraeli+ ndipo anachititsa kuti anthu onse a ku Isiraeli azitumikira Yehova Mulungu wawo. Pa nthawi yonse ya moyo wa Yosiya, iwo sanasiye kutsatira Yehova Mulungu wa makolo awo.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “nyumba.”
Kapena kuti, “chifukwa chakuti unafewetsa mtima wako.”
Kapena kuti, “inabwereza.”
Kapena kuti, “mafano.”