2 Mbiri 35:1-27

  • Yosiya anakonza zoti achite pasika (1-19)

  • Yosiya anaphedwa ndi Farao Neko (20-27)

35  Yosiya anachitira Yehova Pasika+ ku Yerusalemu ndipo iwo anapha nyama ya nsembe+ ya Pasika pa tsiku la 14 la mwezi woyamba.+  Iye anapatsa ansembe ntchito zawo ndipo anawalimbikitsa kuti azichita utumiki wawo wa panyumba ya Yehova.+  Ndiyeno anauza Alevi, alangizi a Aisiraeli onse,+ omwe anali oyera kwa Yehova, kuti: “Ikani Likasa lopatulika mʼnyumba imene Solomo mwana wa Davide mfumu ya Isiraeli anamanga.+ Musamalinyamulenso pamapewa anu.+ Tsopano tumikirani Yehova Mulungu wanu ndi anthu ake Aisiraeli.  Konzekani mogwirizana ndi nyumba za makolo anu komanso magulu anu, potsatira zimene analemba Davide+ mfumu ya Isiraeli ndiponso mwana wake Solomo.+  Muime mʼmalo oyera mogwirizana ndi gulu limene muli, ndipo muime mʼnjira yoti banja lililonse likhale ndi banja la Alevi lowathandiza.  Muphe nyama ya nsembe ya Pasika+ nʼkudziyeretsa ndipo muwakonzere abale anu nyama kuti mutsatire mawu a Yehova kudzera mwa Mose.”  Yosiya anapereka ziweto zokwana 30,000 kwa anthu kuti zikhale nsembe ya Pasika ya anthu onse amene analipo. Anapereka ana a nkhosa amphongo ndi ana a mbuzi amphongo ndiponso ngʼombe 3,000. Zonsezi zinachokera pa katundu wa mfumu.+  Akalonga ake anaperekanso nsembe yaufulu kwa anthuwo, kwa ansembe ndi kwa Alevi. Hilikiya,+ Zekariya ndi Yehiela monga atsogoleri a nyumba ya Mulungu woona, anapereka kwa ansembe nkhosa ndi mbuzi zokwana 2,600 ndiponso ngʼombe 300 kuti zikhale nsembe za Pasika.  Konaniya limodzi ndi abale ake, Semaya ndi Netaneli, komanso Hasabiya, Yeyeli ndi Yozabadi, amene anali atsogoleri a Alevi, anapereka kwa Alevi nkhosa ndi mbuzi 5,000 ndiponso ngʼombe 500 kuti zikhale nsembe za Pasika. 10  Iwo atamaliza kukonzekera, ansembe anaimirira mʼmalo awo, komanso Alevi anali mʼmagulu awo+ mogwirizana ndi zimene mfumu inalamula. 11  Atatero anapha nyama ya Pasika+ ndipo ansembe anawaza paguwa lansembe magazi amene anapatsidwa.+ Pa nthawiyi nʼkuti Alevi akusenda nyamazo.+ 12  Kenako, anakonza nsembe zopsereza kuti azipereke kwa anthuwo potsatira nyumba za makolo awo kuti ziperekedwe kwa Yehova mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la Mose. Anachitanso chimodzimodzi ndi ngʼombe. 13  Zitatero anaphika* nsembe ya Pasika pamoto malinga ndi mwambo wawo.+ Nsembe zopatulika anaziphikira mʼmiphika ingʼonoingʼono, mʼmiphika ikuluikulu ndi mʼmapani. Atamaliza kuphika anapititsa nyamayo mofulumira kwa anthu ena onse. 14  Pambuyo pake anakonza nyama yawo ndi ya ansembe chifukwa ansembe, mbadwa za Aroni, ankapereka nsembe zopsereza ndiponso nsembe za mafuta mpaka kunja kunada. Choncho Alevi anakonza nyama yawo ndi ya ansembe, mbadwa za Aroni. 15  Oimba, ana a Asafu,+ anali pa ntchito yawo mogwirizana ndi lamulo la Davide,+ la Asafu,+ la Hemani ndi la Yedutuni+ yemwe anali wamasomphenya wa mfumu. Alonda apageti anali pamageti osiyanasiyana.+ Iwo sankafunika kusiya ntchito yawo chifukwa Alevi abale awo anawakonzera nyama yawo. 16  Iwo anamaliza kukonza zonse zofunikira pochita Pasika+ wa Yehova tsiku limenelo komanso popereka nsembe zopsereza paguwa lansembe la Yehova, mogwirizana ndi lamulo la Mfumu Yosiya.+ 17  Pa nthawi imeneyo, Aisiraeli amene analipo anachita Pasika komanso Chikondwerero cha Mkate Wopanda Zofufumitsa kwa masiku 7.+ 18  Pasika ngati ameneyu anali asanachitikepo mu Isiraeli kuchokera mu nthawi ya mneneri Samueli. Mafumu ena onse a Isiraeli anali asanachitepo Pasika ngati amene anachita Yosiya,+ ansembe, Alevi, Ayuda ndi Aisiraeli onse amene analipo ndiponso anthu a ku Yerusalemu. 19  Pasika ameneyu anachitika mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yosiya. 20  Pambuyo pa zonsezi, Yosiya atakonza kachisi, Neko+ mfumu ya Iguputo anabwera kudzamenya nkhondo ku Karikemisi pafupi ndi mtsinje wa Firate, ndipo Yosiya anapita kukamenyana naye.+ 21  Choncho Neko anatumiza anthu kuti akamuuze kuti: “Kodi chikukukhudza nʼchiyani iwe mfumu ya Yuda? Ulendo uno sindinabwere kudzamenyana ndi iwe. Ndabwera kudzamenyana ndi mtundu wina ndipo Mulungu wanena kuti ndisachedwe. Ngati ukufuna kuti zinthu zikuyendere bwino, usachite zimenezi. Usatsutsane ndi Mulungu amene ali ndi ine chifukwa akhoza kukuwononga.” 22  Koma Yosiya anadzisintha+ nʼkupitabe kukamenyana naye. Iye sanamvere mawu a Neko omwe anali ochokera kwa Mulungu. Choncho anapita kukamenyana naye mʼchigwa cha Megido.+ 23  Kenako asilikali oponya mivi analasa Mfumu Yosiya. Choncho mfumuyo inauza atumiki ake kuti: “Ndichotseni malo ano chifukwa ndavulala kwambiri.” 24  Atumiki akewo anamutsitsa mʼgaletalo nʼkumukweza mʼgaleta lake lina lankhondo ndipo anabwerera naye ku Yerusalemu. Iye anafa ndipo anamuika mʼmanda a makolo ake.+ Ayuda onse ndi anthu onse a ku Yerusalemu analira maliro a Yosiya. 25  Yeremiya+ anaimba nyimbo ya maliro a Yosiya. Oimba onse aamuna ndi aakazi+ amaimba zokhudza Yosiya akamaimba nyimbo za maliro mpaka lero. Panakhazikitsidwa lamulo loti nyimbo zimenezi ziziimbidwa mu Isiraeli ndipo zinaikidwa mʼgulu la nyimbo zoimba pamaliro. 26  Nkhani zina zokhudza Yosiya komanso mmene anasonyezera chikondi chokhulupirika potsatira zomwe zinalembedwa mʼChilamulo cha Yehova, 27  ndiponso zimene anachita, kuyambira pachiyambi mpaka pamapeto, zinalembedwa mʼBuku la Mafumu a Isiraeli ndi Yuda.+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “anawotcha.”