2 Mbiri 6:1-42

  • Solomo analankhula ndi anthu (1-11)

  • Pemphero la Solomo lotsegulira kachisi (12-42)

6  Pa nthawiyo Solomo ananena kuti: “Yehova anati adzakhala mumdima wandiweyani.+  Tsopano ndakumangirani nyumba yapamwamba yomwe ndi malo okhazikika oti muzikhalamo mpaka kalekale.”+  Kenako mfumu inatembenuka nʼkuyamba kudalitsa gulu lonse la Aisiraeli. Apa nʼkuti Aisiraeli onsewo ataimirira.+  Mfumuyo inati: “Atamandike Yehova Mulungu wa Isiraeli, amene ndi pakamwa pake analonjeza bambo anga Davide ndipo ndi manja ake wakwaniritsa zimene ananena zakuti,  ‘Kuyambira tsiku limene ndinatulutsa anthu anga mʼdziko la Iguputo, sindinasankhe mzinda mʼmafuko onse a Isiraeli womangako nyumba ya dzina langa kuti likhale kumeneko.+ Ndipo sindinasankhe munthu woti alamulire anthu anga Aisiraeli.  Koma ndasankha Yerusalemu+ kuti dzina langa likhale kumeneko ndiponso ndasankha Davide kuti alamulire anthu anga Aisiraeli.’+  Ndipo bambo anga Davide ankafunitsitsa kumanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.+  Koma Yehova anauza Davide bambo anga kuti, ‘Unkafunitsitsa kumanga nyumba ya dzina langa ndipo unachita bwino kulakalaka utachita zimenezi.  Koma iweyo sumanga nyumbayi, mʼmalomwake mwana wamwamuna amene udzabereke* ndi amene adzamange nyumba ya dzina langa.’+ 10  Yehova wakwaniritsa zimene analonjeza, chifukwa ndalowa mʼmalo mwa bambo anga Davide ndipo ndakhala pampando wachifumu wa Isiraeli,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analonjeza.+ Komanso ndamanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli. 11  Ndipo mʼnyumbamo ndaikamo Likasa, lomwe muli pangano+ limene Yehova anapangana ndi Aisiraeli.” 12  Kenako Solomo anaimirira pafupi ndi guwa lansembe la Yehova kutsogolo kwa Aisiraeli onse ndipo anakweza manja ake mʼmwamba.+ 13  (Solomo anapanga nsanja yakopa* nʼkuiika pakati pa bwalo lamkati.+ Nsanjayo inali yaikulu mikono* 5 mulitali, mikono 5 mulifupi ndiponso mikono itatu kupita mʼmwamba. Iye anakwera pansanjayo.) Ndiyeno anagwada patsogolo pa Aisiraeli onse nʼkukweza manja ake mʼmwamba.+ 14  Atatero anati: “Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli, palibe Mulungu wina wofanana ndi inu kumwambako kapena pansi pano. Mumasunga pangano komanso mumasonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu amene amakutumikirani ndi mtima wawo wonse.+ 15  Mwakwaniritsa lonjezo limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga.+ Munalonjeza ndi pakamwa panu ndipo lero mwakwaniritsa ndi dzanja lanu.+ 16  Tsopano inu Yehova Mulungu wa Isiraeli, mukwaniritse lonjezo limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga lakuti, ‘Anthu a mʼbanja lako sadzasiya kukhala pampando wachifumu wa Isiraeli. Chofunika nʼchakuti ana ako asamale mayendedwe awo poyenda mokhulupirika mʼnjira zanga+ ngati mmene iwe wachitira.’+ 17  Ndiye inu Yehova Mulungu wa Isiraeli, zimene munalonjeza mtumiki wanu Davide zikwaniritsidwe. 18  Koma kodi Mulungu angakhaledi limodzi ndi anthu padziko lapansi?+ Kumwamba, ngakhalenso kumwamba kwa kumwamba, simungakwaneko.+ Kuli bwanji nyumba imene ndamangayi?+ 19  Inu Yehova Mulungu wanga, mumvetsere pemphero la mtumiki wanu ndi pempho lake lopempha chifundo. Imvani kulira kwanga kopempha thandizo komanso pemphero limene ine mtumiki wanu ndikupemphera kwa inu. 20  Maso anu akhale akuyangʼana nyumba ino masana komanso usiku. Akhale akuyangʼana malo amene munanena kuti dzina lanu lidzakhala kumeneko,+ kuti mumvetsere pemphero limene mtumiki wanu angapemphere atayangʼana kumalo ano. 21  Mumve pemphero la mtumiki wanu lopempha thandizo komanso la anthu anu Aisiraeli, limene angapemphere atayangʼana malo ano.+ Inuyo mumve muli kumalo anu okhala, kumwamba,+ mumve nʼkukhululuka.+ 22  Munthu akachimwira mnzake, wochimwiridwayo nʼkulumbiritsa* wochimwayo pofuna kutsimikiza kuti sanachimwedi, ndiyeno wochimwayo akabwera patsogolo pa guwa lansembe mʼnyumba muno,+ 23  inu mumve muli kumwamba ndipo muchitepo kanthu posonyeza amene ali wolakwa pobwezera wolakwayo mogwirizana ndi zochita zake+ komanso musonyeze amene ali wosalakwa nʼkumupatsa mphoto mogwirizana ndi chilungamo chake.+ 24  Anthu anu Aisiraeli akagonjetsedwa ndi adani awo chifukwa choti ankakuchimwirani,+ ndiyeno abwerera kwa inu nʼkutamanda dzina lanu+ mʼnyumbayi, kupemphera+ ndiponso kupempha kuti muwachitire chifundo,+ 25  inuyo mumve muli kumwambako+ ndipo mukhululuke tchimo la anthu anu Aisiraeli nʼkuwabwezeretsa kudziko limene munapatsa iwowo ndiponso makolo awo.+ 26  Kumwamba kukatsekeka, mvula nʼkumakanika kugwa+ chifukwa choti akhala akukuchimwirani,+ ndiyeno iwo nʼkupemphera atayangʼana malo ano, kutamanda dzina lanu ndiponso kusiya machimo awo chifukwa choti mwawapatsa chilango,+ 27  inuyo mumve muli kumwambako ndipo anthu anu Aisiraeli, omwenso ndi atumiki anu, muwakhululukire machimo awo popeza mudzawaphunzitsa njira yabwino yoti aziyendamo.+ Mubweretse mvula+ mʼdziko lanu limene munapatsa anthu anu monga cholowa. 28  Mʼdzikomo mukagwa njala,+ mliri,+ mphepo yotentha yowononga mbewu, matenda ambewu a chuku,+ dzombe,+ ziwala zowononga, mliri wamtundu uliwonse, nthenda yamtundu uliwonse komanso adani awo akawaukira+ mʼmizinda yawo,+ 29  ndiyeno munthu aliyense kapena anthu anu onse Aisiraeli akapereka pemphero lililonse,+ akapempha kuti muwachitire chifundo+ (chifukwa aliyense akudziwa mliri wake ndi ululu wake),+ ndiponso akakweza manja awo atayangʼana kunyumbayi,+ 30  inuyo mumve muli kumwambako, komwe mumakhala+ ndipo mukhululuke+ ndi kuchitapo kanthu. Mupereke mphoto kwa aliyense mogwirizana ndi njira zake zonse, chifukwa mukudziwa mtima wake (inu nokha mumadziwa bwino mtima wa munthu aliyense).+ 31  Muchite zimenezi kuti iwo azikuopani poyenda mʼnjira zanu masiku onse amene angakhale ndi moyo mʼdziko limene munapatsa makolo athu. 32  Komanso mlendo amene si mmodzi wa anthu anu Aisiraeli, amene wabwera kuchokera kudziko lakutali chifukwa cha dzina* lanu lalikulu,+ dzanja lanu lamphamvu ndiponso mkono wanu wokonzeka kuthandiza,* ndipo wabwera nʼkupemphera atayangʼana nyumbayi,+ 33  inuyo mumve muli kumwambako, kumene mumakhala, ndipo muchite zonse zimene mlendoyo wakupemphani. Muchite zimenezi kuti anthu a mitundu yonse yapadziko lapansi adziwe dzina lanu+ ndiponso akuopeni ngati mmene anthu anu Aisiraeli amachitira, komanso adziwe kuti dzina lanu lili panyumba imene ndamangayi. 34  Anthu anu akapita kunkhondo kukamenyana ndi adani awo mmene mwawatumizira,+ ndipo akapemphera+ kwa inu atayangʼana kumzinda umene mwasankha ndi kunyumba ya dzina lanu imene ndamanga,+ 35  inuyo mumve muli kumwambako pemphero lawo ndi pempho lawo lopempha chifundo, ndipo muonetsetse kuti chilungamo chachitika kwa iwo.+ 36  Anthu anu akakuchimwirani (popeza palibe munthu amene sachimwa)+ inu nʼkuwakwiyira kwambiri ndiponso kuwapereka kwa adani, adani awowo nʼkuwatenga kupita nawo kudziko lakutali kapena lapafupi,+ 37  ndiyeno iwo nʼkuzindikira kulakwa kwawo mʼdziko limene anawatengeralo nʼkulapa, ndiponso akapempha chifundo kwa inu mʼdziko la adani awowo nʼkunena kuti, ‘Tachimwa, talakwitsa ndiponso tachita zinthu zoipa,’+ 38  nʼkubwerera kwa inu ndi mtima wawo wonse+ ndi moyo wawo wonse, mʼdziko limene anapita nawo atawagwira,+ ndiponso akapemphera kwa inu atayangʼana kudziko lawo limene munapatsa makolo awo, mzinda umene mwasankha+ komanso nyumba ya dzina lanu imene ndamanga, 39  inuyo, kumwamba kumene mumakhalako, mumve pemphero lawo ndi pempho lawo lopempha chifundo ndipo muonetsetse kuti chilungamo chachitika kwa iwo.+ Mukhululukire anthu anu amene anakuchimwirani. 40  Tsopano Mulungu wanga, chonde, maso anu aone ndipo makutu anu akhale tcheru kumvetsera pemphero loperekedwa pamalo ano.+ 41  Inu Yehova Mulungu nyamukani mulowe mʼmalo oti mupumeko,+ inuyo komanso Likasa limene mumasonyezera mphamvu zanu. Ansembe anu, inu Yehova Mulungu, avale chipulumutso ndipo okhulupirika anu asangalale chifukwa cha ubwino wanu.+ 42  Inu Yehova Mulungu, musakane wodzozedwa wanu.+ Kumbukirani chikondi chanu chokhulupirika chimene munasonyeza Davide mtumiki wanu.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “wotuluka mʼchiuno mwako.”
Kapena kuti, “yamkuwa.”
Mkono umodzi unali wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “nʼkumutemberera.” Limeneli ndi lumbiro limene linkachititsa kuti munthu atembereredwe ngati walumbira monama kapena ngati sanakwaniritse zomwe walumbirazo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkono wanu wotambasula.”
Kapena kuti, “mbiri yanu.”