2 Mbiri 8:1-18

  • Zinthu zina zimene Solomo anamanga (1-11)

  • Anakonza dongosolo lolambirira pakachisi (12-16)

  • Zombo za Solomo (17, 18)

8  Kumapeto kwa zaka 20 zimene Solomo anamanga nyumba ya Yehova ndiponso nyumba* yake,+  iye anamanganso mizinda imene Hiramu+ anamʼpatsa nʼkuipereka kwa Aisiraeli* kuti azikhalamo.  Kuwonjezera pamenepo, Solomo anapita ku Hamati-zoba nʼkukagonjetsa anthu akumeneko.  Kenako anamanganso mzinda wa Tadimori mʼchipululu komanso mizinda yonse yosungiramo zinthu+ imene anamanga ku Hamati.+  Anamanganso mzinda wa Beti-horoni+ Wakumtunda ndi Beti-horoni Wakumunsi.+ Imeneyi inali mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, mageti ndi mipiringidzo.  Anamanganso Baalati+ ndi mizinda yonse yosungirako zinthu ya Solomo, mizinda yonse yosungirako magaleta,+ mizinda ya amuna okwera pamahatchi ndiponso zilizonse zimene iye anafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi mʼmadera onse amene ankalamulira.  Panalinso Ahiti onse otsala, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi+ amene sanali Aisiraeli,+  komanso mbadwa zawo zimene zinatsala mʼdzikomo, zomwe Aisiraeli analephera kuzipha.+ Anthu onsewa Solomo ankawagwiritsa ntchito yaukapolo ndipo akugwirabe ntchitoyi mpaka lero.+  Koma palibe Aisiraeli amene Solomo anawasandutsa akapolo ogwira ntchito yake,+ chifukwa iwo anali asilikali ake, atsogoleri a asilikali ake othandiza pamagaleta ndiponso atsogoleri a asilikali ake oyendetsa magaleta ndi amuna okwera pamahatchi.+ 10  Panali akuluakulu oyangʼanira nduna okwana 250 a Mfumu Solomo omwe ankayangʼanira anthu ogwira ntchito.+ 11  Solomo anatulutsa mwana wamkazi+ wa Farao mu Mzinda wa Davide nʼkukamuika mʼnyumba imene anamʼmangira+ chifukwa iye anati: “Ngakhale kuti ndi mkazi wanga, sakuyenera kumakhala mʼnyumba ya Davide mfumu ya Isiraeli, poti malo alionse amene Likasa la Yehova likukhala ndi oyera.”+ 12  Kenako Solomo anapereka nsembe zopsereza+ kwa Yehova paguwa lansembe+ la Yehova limene iye anamanga patsogolo pa khonde.+ 13  Anatsatira dongosolo la tsiku ndi tsiku loperekera nsembe mogwirizana ndi lamulo la Mose. Nsembezo zinali za pa Masabata,+ za pa masiku amene mwezi watsopano waoneka+ ndi za pa zikondwerero zomwe zinkachitika katatu pa chaka.+ Zikondwererozo zinali Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa,+ Chikondwerero cha Masabata+ ndi Chikondwerero cha Misasa.+ 14  Kuwonjezera pamenepo, Solomo anasankha magulu a ansembe+ kuti azitumikira mogwirizana ndi lamulo la Davide bambo ake. Anasankhanso Alevi kuti azikhala pamalo awo a ntchito nʼkumatamanda+ ndi kutumikira pamaso pa ansembe mogwirizana ndi dongosolo la tsiku ndi tsiku. Komanso anasankha alonda apageti mʼmagulu awo kuti akhale mʼmageti osiyanasiyana+ chifukwa limeneli linali lamulo la Davide munthu wa Mulungu woona. 15  Iwo sanasiye kutsatira lamulo limene mfumu inapereka kwa ansembe ndi Alevi lokhudza nkhani ina iliyonse kapena nyumba zosungiramo zinthu. 16  Choncho ntchito yonse ya Solomo inkayenda bwino, kuyambira tsiku limene anayala maziko a nyumba ya Yehova+ mpaka pamene inatha. Choncho nyumba ya Yehova inatha kumangidwa.+ 17  Pa nthawi imeneyi mʼpamene Solomo anapita ku Ezioni-geberi+ ndi ku Eloti,+ mʼmbali mwa nyanja, mʼdziko la Edomu.+ 18  Hiramu,+ kudzera mwa antchito ake, ankatumizira Solomo zombo ndi antchito odziwa zapanyanja. Ulendo uliwonse umene iwo limodzi ndi antchito a Solomo apita ku Ofiri,+ ankabweretsera Mfumu Solomo+ golide wokwana matalente* 450.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana a Isiraeli.”
Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.