2 Mbiri 9:1-31

  • Mfumukazi ya ku Sheba inapita kwa Solomo (1-12)

  • Chuma cha Solomo (13-28)

  • Imfa ya Solomo (29-31)

9  Mfumukazi ya ku Sheba+ inamva za Solomo. Choncho inabwera ku Yerusalemu kuti idzamuyese pomufunsa mafunso ovuta. Mfumukaziyo inapita ndi anthu ambiri oiperekeza. Inapita ndi ngamila zitanyamula mafuta a basamu, golide wambiri+ ndi miyala yamtengo wapatali. Inafika kwa Solomo nʼkuyamba kulankhula naye zonse zimene zinali mumtima mwake.+  Solomo anayankha mafunso ake onse. Panalibe chimene Solomo analephera kumufotokozera.  Mfumukazi ya ku Sheba itaona nzeru za Solomo,+ nyumba imene anamanga,+  chakudya chapatebulo pake,+ operekera zakumwa, mmene atumiki ake ankakhalira pa nthawi ya chakudya, mmene operekera zakudya ankachitira komanso zovala zawo ndiponso nsembe zopsereza zimene ankapereka panyumba ya Yehova nthawi zonse,+ inasowa chonena.  Choncho inauza mfumuyo kuti: “Nkhani zimene ndinamva kudziko langa zokhudza zimene mwakwanitsa kuchita komanso nzeru zanu ndi zoona.  Koma sindinakhulupirire zimene ndinauzidwa mpaka pamene ndabwera nʼkuona ndi maso anga.+ Panopa ndaona kuti zimene ndinauzidwa zinali hafu chabe ya nzeru zanu zambiri.+ Mwaposa kwambiri zimene ndinamva.+  Anthu anu komanso atumiki anu amene amatumikira pamaso panu nthawi zonse nʼkumamva nzeru zanu, ndi osangalala.  Atamandike Yehova Mulungu wanu, amene wasangalala nanu nʼkukuikani pampando wake wachifumu mʼmalo mwa Yehova Mulungu wanu. Chifukwa Mulungu wanu amakonda Isiraeli+ ndipo amafuna kuti akhalepo mpaka kalekale, wakuikani kuti mukhale mfumu kuti muziweruza anthu ndi kuchita chilungamo.”  Kenako mfumukaziyo inapatsa mfumuyo golide wokwana matalente* 120,+ mafuta a basamu ochuluka kwambiri ndiponso miyala yamtengo wapatali. Mafuta a basamu amene mfumukazi ya ku Sheba inapatsa Mfumu Solomo, anali ambiri moti sipanakhalenso mafuta ochuluka choncho.+ 10  Kuwonjezera pamenepo, atumiki a Hiramu ndi atumiki a Solomo amene anabwera ndi golide kuchokera ku Ofiri,+ anabweretsanso matabwa a mtengo wa mʼbawa ndi miyala yamtengo wapatali.+ 11  Mfumuyo inagwiritsa ntchito matabwa a mʼbawawo popanga masitepe a nyumba ya Yehova+ komanso a nyumba ya mfumu.+ Inagwiritsanso ntchito matabwawo kupanga azeze ndi zoimbira za zingwe za oimba.+ Matabwa a mʼbawa otere, sanaonekeponso mʼdziko la Yuda. 12  Nayonso Mfumu Solomo inapatsa mfumukazi ya ku Sheba chilichonse chimene inkafuna komanso chimene inapempha. Inapatsa mfumukaziyo zoposa zimene inabweretsa. Kenako mfumukaziyo inanyamuka nʼkumapita kwawo limodzi ndi antchito ake.+ 13  Golide amene ankabwera kwa Solomo pa chaka, anali wolemera matalente 666,+ 14  osawerengera golide wochokera kwa amalonda oyendayenda ndi amalonda ena, komanso wochokera kwa mafumu onse a Aluya ndi kwa abwanamkubwa amʼdzikolo, amene ankabweretsa golide ndi siliva kwa Solomo.+ 15  Mfumu Solomo anapanga zishango 200 zikuluzikulu za golide wosakaniza ndi zitsulo zina.+ (Chishango chilichonse anachikuta ndi golide wolemera masekeli* 600.)+ 16  Anapanganso zishango 300 zingʼonozingʼono* za golide wosakaniza ndi zitsulo zina. (Chishango chilichonse anachikuta ndi golide wolemera ma mina* atatu.) Kenako mfumuyo inaika zishangozi mʼnyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.+ 17  Mfumuyo inapanganso mpando wachifumu waukulu waminyanga ya njovu nʼkuukuta ndi golide woyenga bwino.+ 18  Panali masitepe 6 okafika kumpando wachifumuwo. Mpando wachifumuwo unali ndi chopondapo mapazi chagolide cholumikiza kumpandowo. Mpandowo unali ndi moika manja mbali zonse ziwiri. Mʼmbali mwake munali zifaniziro ziwiri za mikango+ itaimirira. 19  Pamasitepe 6 aja, panali zifaniziro 12 za mikango+ itaimirira. Kumapeto kwa sitepe iliyonse kunali mkango umodzi. Panalibenso ufumu womwe unali ndi mpando wachifumu ngati umenewo. 20  Makapu onse a Mfumu Solomo anali agolide, ndipo ziwiya zonse zamʼnyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide yekhayekha. Panalibe chiwiya chasiliva chifukwa siliva sankaoneka ngati kanthu mʼmasiku a Solomo.+ 21  Zinali choncho chifukwa zombo za mfumu zinkapita ku Tarisi+ limodzi ndi atumiki a Hiramu.+ Kamodzi pa zaka zitatu zilizonse, zombozo zinkabweretsa golide, siliva, minyanga ya njovu,+ anyani ndi mbalame zotchedwa pikoko. 22  Choncho Mfumu Solomo anali wolemera kwambiri ndiponso wanzeru kuposa mafumu ena onse a padziko lapansi.+ 23  Mafumu onse apadziko lapansi ankafuna kuonana ndi Solomo kuti amve nzeru zake zimene Mulungu woona anaika mumtima mwake.+ 24  Anthuwo ankabweretsa mphatso monga zinthu zasiliva, zinthu zagolide, zovala,+ zida zankhondo, mafuta a basamu, mahatchi komanso nyulu* ndipo zimenezi zinkachitika chaka chilichonse. 25  Solomo anali ndi makola 4,000 a mahatchi ndi magaleta komanso mahatchi* okwana 12,000.+ Zonsezi ankazisunga mʼmizinda yosungiramo magaleta ndiponso pafupi ndi mfumuyo ku Yerusalemu.+ 26  Solomo ankalamulira mafumu onse kuyambira ku Mtsinje* mpaka kudziko la Afilisiti nʼkukafika kumalire ndi Iguputo.+ 27  Mfumuyo inachititsa kuti ku Yerusalemu kukhale siliva wambiri ngati miyala ndiponso kuti matabwa a mkungudza akhale ambiri ngati mitengo ya mkuyu ya ku Sefela.+ 28  Anthu ankamubweretsera Solomo mahatchi kuchokera ku Iguputo+ ndi kumayiko ena onse. 29  Nkhani zina zokhudza Solomo,+ kuyambira zoyamba mpaka zomaliza, zikupezeka mʼzinthu zimene mneneri Natani+ analemba, mu ulosi wa Ahiya+ wa ku Silo ndiponso mʼbuku la masomphenya a mneneri* Ido,+ lonena za Yerobowamu+ mwana wa Nebati. 30  Solomo analamulira Isiraeli yense ku Yerusalemu kwa zaka 40. 31  Kenako Solomo, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide bambo ake.+ Ndiyeno mwana wake Rehobowamu, anakhala mfumu mʼmalo mwake.+

Mawu a M'munsi

Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
“Mina” yotchulidwa mʼMalemba a Chiheberi inkalemera magalamu 570. Onani Zakumapeto B14.
Nthawi zambiri amene ankanyamula zishango zimenezi anali oponya mivi.
“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.
Kapena kuti, “amuna okwera pamahatchi.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Kapena kuti, “wamasomphenya.”