2 Samueli 1:1-27

  • Davide anamva za imfa ya Sauli (1-16)

  • Davide anaimba nyimbo yolira Sauli ndi Yonatani (17-27)

1  Sauli atamwalira, ndiponso Davide atabwera kuchokera kokagonjetsa* Aamaleki, Davideyo anakhala ku Zikilaga+ masiku awiri.  Tsiku lachitatu, munthu wina anabwera kuchokera kumsasa wa Sauli. Iye anali atangʼamba zovala zake komanso atadzithira dothi kumutu. Atafika kwa Davide, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake kufika pansi, kenako anagona pansi.  Davide anamufunsa kuti: “Wachokera kuti?” Iye anayankha kuti: “Ndathawa kumsasa wa Isiraeli.”  Ndiyeno Davide anamufunsa kuti: “Zayenda bwanji kumeneko? Chonde, ndiuze.” Iye anayankha kuti: “Anthu athawa kunkhondo komanso anthu ambiri aphedwa. Nayenso Sauli ndi mwana wake Yonatani afa.”+  Davide anafunsa mnyamatayo kuti: “Iwe wadziwa bwanji kuti Sauli ndi mwana wake Yonatani afa?”  Mnyamatayo anayankha kuti: “Zinangochitika kuti ineyo ndinali paphiri la Giliboa,+ ndipo ndinaona Sauli atatsamira mkondo wake. Asilikali oyenda mʼmagaleta ndi asilikali okwera pamahatchi anali atamupeza.+  Sauliyo atatembenuka nʼkundiona, anandiitana ndipo ine ndinayankha kuti, ‘Ine mbuyanga!’  Ndiyeno anandifunsa kuti, ‘Ndiwe ndani?’ Ndinamuyankha kuti, ‘Ndine Mwamaleki.’+  Ndiyeno anandiuza kuti, ‘Chonde bwera undiphe, chifukwa ndikumva ululu woopsa koma ndidakali moyo.’ 10  Choncho ndinapita nʼkukamupha+ chifukwa ndinadziwa kuti sakhalanso ndi moyo popeza anali atagwa komanso atavulala kwambiri. Kenako ndinatenga chipewa chachifumu chimene chinali kumutu kwake ndi khoza lomwe anavala pamkono ndipo ndabwera nazo kwa inu mbuyanga.” 11  Davide atamva zimenezi anagwira zovala zake nʼkuzingʼamba. Nawonso amuna onse amene anali naye anangʼamba zovala zawo. 12  Atatero, anayamba kulira ndi kusala kudya+ mpaka madzulo. Iwo ankalira maliro a Sauli, mwana wake Yonatani, anthu a Yehova ndiponso nyumba ya Isiraeli+ chifukwa anali ataphedwa ndi lupanga. 13  Ndiyeno Davide anafunsa mnyamata amene anabweretsa uthengawo kuti: “Kodi kwanu nʼkuti?” Iye anayankha kuti: “Ndine mwana wa Mwamaleki, amene anabwera kudzakhala ndi Aisiraeli.” 14  Davide anamufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani sunaope kupha wodzozedwa wa Yehova?”+ 15  Atatero, Davide anaitana mmodzi mwa anyamata ake nʼkumuuza kuti: “Bwera kuno udzamuphe.” Choncho iye anamuphadi.+ 16  Davide anamuuza kuti: “Mlandu wa magazi ako ukhale pamutu pako, chifukwa wadzichitira wekha umboni ponena kuti, ‘Ineyo ndapha wodzozedwa wa Yehova.’”+ 17  Ndiyeno Davide anayamba kuimba nyimbo yamaliro iyi polirira Sauli komanso mwana wake Yonatani.+ 18  Iye ananenanso kuti anthu a ku Yuda aphunzitsidwe nyimboyi, yotchedwa “Uta.” Nyimbo imeneyi inalembedwa mʼbuku la Yasari:+ 19  “Isiraeli iwe, anthu ako aulemerero aphedwa pamalo ako okwezeka.+ Anthu amphamvu agwa! 20  Musanene zimenezi ku Gati;+Musazilengeze mʼmisewu ya Asikeloni,Chifukwa ana aakazi a Afilisiti akhoza kusangalala,Ana aakazi a anthu osadulidwa akhoza kukondwera. 21  Inu mapiri a Giliboa,+Mame kapena mvula zisagwe pa inu.Komanso minda yakumeneko isatulutse zopereka zopatulika.+Chifukwa chishango cha amuna amphamvu chinadetsedwa kumeneko,Chishango cha Sauli sichikupakidwanso mafuta. 22  Uta wa Yonatani sunkalephera kupha adani ndi kukhetsa magazi awo,Sunkalephera kubaya mafuta a anthu amphamvu.+Lupanga la Sauli silinkabwerera osakwaniritsa ntchito yake.+ 23  Sauli ndi Yonatani+ anali okondedwa ndi osangalatsa pa moyo wawo,Ngakhale pa imfa yawo sanasiyane.+ Anali aliwiro kuposa chiwombankhanga,+Amphamvu kuposa mikango.+ 24  Inu ana aakazi a Isiraeli, mulirireni Sauli,Amene anakuvekani zovala zamtengo wapatali, zofiira komanso zokhala ndi zokongoletsa,Amene anaika zokongoletsa zagolide pazovala zanu. 25  Isiraeli iwe, anthu amphamvu agwa pankhondo! Yonatani waphedwa pamalo ako okwezeka!+ 26  Mtima wanga ukuwawa chifukwa cha iwe mchimwene wanga Yonatani;Ndinkakukonda kwambiri.+ Chikondi chimene unali nacho pa ine chinkaposa chikondi cha akazi.+ 27  Anthu amphamvu agwa,Ndipo zida zankhondo zawonongeka.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kokapha.”