2 Samueli 10:1-19

  • Anagonjetsa Aamoni ndi Asiriya (1-19)

10  Kenako mfumu ya Aamoni+ inamwalira, ndipo mwana wake Hanuni anayamba kulamulira mʼmalo mwake.+ 2  Zitatero, Davide anati: “Ndimusonyeza Hanuni mwana wa Nahasi chikondi chokhulupirika ngati mmene bambo ake anandisonyezera chikondi chokhulupirika.” Choncho Davide anatumiza atumiki ake kuti akamutonthoze chifukwa cha imfa ya bambo ake. Koma atumiki a Davidewo atangofika mʼdziko la Aamoni, 3  akalonga a Aamoni anauza Hanuni mbuye wawo kuti: “Kodi mukuganiza kuti Davide watumiza anthu odzakutonthozani chifukwa cholemekeza bambo anu? Kodi iye sanatumize atumiki akewa kuti adzafufuze zokhudza mzindawu nʼcholinga choti adzaulande?” 4  Choncho Hanuni anatenga atumiki a Davide aja nʼkuwameta ndevu mbali imodzi,+ kenako anadula zovala zawo pakati moti zinalekeza mʼmatako nʼkuwauza kuti azipita. 5  Davide atamva zimenezi, nthawi yomweyo anatumiza anthu kuti akakumane nawo chifukwa atumiki akewo anali atachititsidwa manyazi kwambiri. Choncho mfumu inawauza kuti: “Mukhalebe ku Yeriko+ mpaka ndevu zanu zitakula, kenako mudzabwere.” 6  Patapita nthawi, Aamoni anaona kuti akhala ngati chinthu chonunkha kwa Davide. Choncho anatumiza anthu kuti akalembe ganyu Asiriya a ku Beti-rehobu+ ndi Asiriya a ku Zoba+ ndipo onse pamodzi analipo asilikali 20,000 oyenda pansi. Anapitanso kwa mfumu ya ku Maaka+ nʼkulemba ganyu amuna 1,000 komanso ku Isitobu amuna 12,000.+ 7  Davide atamva zimenezi anatumiza Yowabu ndi gulu lonse lankhondo, limodzinso ndi asilikali ake amphamvu.+ 8  Ndiyeno Aamoni anapita kukaima pageti la mzinda atakonzekera kumenya nkhondo. Pomwe Asiriya a ku Zoba, a ku Rehobu, a ku Isitobu ndi a ku Maaka anakayalana kwaokha kutchire. 9  Yowabu ataona kuti adani ake akubwera kuchokera kutsogolo ndi kumbuyo, anasankha ena mwa magulu a asilikali amphamvu mu Isiraeli nʼkuwakonzekeretsa kuti amenyane ndi Asiriya.+ 10  Anthu ena onse anawapereka kwa mchimwene wake Abisai+ kuti awatsogolere pokamenyana ndi Aamoni.+ 11  Ndiyeno anamuuza kuti: “Ukaona kuti Asiriya akundigonjetsa, ubwere udzandipulumutse. Koma Aamoni akayamba kukugonjetsa, ineyo ndibwera kudzakupulumutsa. 12  Tikuyenera kuchita zinthu mwamphamvu komanso molimba mtima+ chifukwa cha anthu athu ndiponso chifukwa cha mizinda ya Mulungu wathu. Yehova adzachita zimene akuona kuti nʼzabwino kwa iye.”+ 13  Kenako Yowabu ndi amuna amene anali naye anapita kukamenyana ndi Asiriya ndipo Asiriyawo anayamba kuthawa.+ 14  Aamoni ataona kuti Asiriya athawa, nawonso anathawa Abisai nʼkupita mumzinda. Yowabu atamaliza kumenyana ndi Aamoni anabwerera ku Yerusalemu. 15  Asiriya ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisiraeli, anasonkhananso pamodzi.+ 16  Choncho Hadadezeri+ anatuma anthu kuti akatenge Asiriya amene anali mʼdera la ku Mtsinje.*+ Atatero anabwera ku Helamu ndipo Sobaki mkulu wa asilikali a Hadadezeri ndi amene ankawatsogolera. 17  Davide atamva zimenezi, nthawi yomweyo anasonkhanitsa Aisiraeli onse nʼkuwoloka Yorodano kupita ku Helamu. Ndiyeno Asiriya anayalana kuti akumane ndi Davide ndipo anayamba kumenyana naye.+ 18  Koma Asiriyawo anayamba kuthawa Isiraeli ndipo Davide anapha asilikali a Siriya 700 okwera magaleta komanso asilikali 40,000 okwera pamahatchi. Iye anaphanso Sobaki, mtsogoleri wa gulu lankhondo la Siriya.+ 19  Mafumu onse amene anali atumiki a Hadadezeri ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisiraeli, nthawi yomweyo anakhazikitsa mtendere ndi Aisiraeli nʼkuyamba kuwatumikira.+ Asiriya anachita mantha kwambiri moti sanayesenso kuthandiza Aamoni.

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.