2 Samueli 11:1-27

  • Davide anachita chigololo ndi Bati-seba (1-13)

  • Davide anakonza zoti Uriya aphedwe (14-25)

  • Davide anakwatira Bati-seba (26, 27)

11  Kumayambiriro kwa chaka, pa nthawi imene mafumu ankapita kukamenya nkhondo, Davide anatumiza Yowabu ndi atumiki ake komanso asilikali onse Aisiraeli kuti akaphe Aamoni ndipo iwo anazungulira mzinda wa Raba.+ Koma Davide anatsala ku Yerusalemu.+  Tsiku lina madzulo, Davide anadzuka pabedi lake nʼkupita kukayendayenda padenga la nyumba yake yachifumu. Ali pamenepo anaona mkazi akusamba, ndipo mkaziyo anali wokongola kwambiri.  Kenako Davide anatuma munthu kukafufuza za mkaziyo. Ndiyeno munthuyo anati: “Ndi Bati-seba+ mwana wa Eliyamu,+ mkazi wa Uriya+ Muhiti.”+  Davide anatuma anthu kuti akamutenge.+ Choncho mkaziyo anabweradi ndipo Davide anagona naye.+ (Zimenezi zinachitika pa nthawi imene mkaziyo ankadziyeretsa.*)+ Kenako mkaziyo anabwerera kunyumba kwake.  Mkaziyo anakhala ndi pakati ndipo anatumiza uthenga kwa Davide wakuti: “Ndili ndi pakati.”  Zitatero, Davide anatumiza uthenga kwa Yowabu wakuti: “Umuuze Uriya Muhiti abwere.” Choncho Yowabu anauza Uriya kuti apite kwa Davide.  Uriya atafika, Davide anamufunsa za moyo wa Yowabu ndi asilikali onse komanso mmene nkhondo ikuyendera.  Kenako Davide anauza Uriya kuti: “Pita kunyumba kwako ukapume.”* Uriya atachoka mʼnyumba ya mfumu, mfumuyo inamutumizira mphatso.*  Koma Uriya anagona pakhomo la nyumba ya mfumu pamodzi ndi atumiki ena a mbuye wake, moti sanapite kunyumba kwake. 10  Choncho anthu anauza Davide kuti: “Uriya sanapite kunyumba kwake.” Davide atamva zimenezi, anauza Uriya kuti: “Iweyo wayenda ulendo wautali, ndiye bwanji sunapite kunyumba kwako?” 11  Uriya anauza Davide kuti: “Likasa+ komanso asilikali a Isiraeli ndi Yuda akukhala mʼmisasa, ndipo mbuyanga Yowabu pamodzi ndi atumiki anu mbuyanga ali mumsasa kutchire. Ndiye ine ndikalowe mʼnyumba yanga kukadya chakudya, kumwa ndi kugona ndi mkazi wanga?+ Ndithu ndikulumbira mʼdzina lanu mfumu muli apa, sindingachite zimenezo!” 12  Ndiyeno Davide anauza Uriya kuti: “Leronso usanyamuke, upita mawa.” Choncho Uriya anakhalabe ku Yerusalemu tsiku limenelo ndiponso lotsatira. 13  Kenako Davide anamuitana kuti adzadye ndi kumwa naye limodzi ndipo anamuledzeretsa. Koma madzulo Uriya anapita kukagona pabedi limodzi ndi atumiki a mbuye wake, ndipo sanapite kunyumba kwake. 14  Mʼmawa mwake, Davide analembera kalata Yowabu ndipo anapatsira Uriya. 15  Mʼkalatayo analembamo kuti: “Muike Uriya kutsogolo kumene nkhondo yakula, ndipo inu mubwerere mʼmbuyo kuti amuphe.”+ 16  Yowabu anali atafufuza zokhudza mzinda wa Raba ndipo anaika Uriya pamalo amene ankadziwa kuti akumana ndi asilikali amphamvu. 17  Amuna amumzindawo atatuluka kudzamenyana ndi Yowabu, atumiki ena a Davide anaphedwa ndipo Uriya Muhiti nayenso anafa.+ 18  Kenako Yowabu anatumiza munthu kuti akauze Davide zonse zimene zachitika kunkhondo. 19  Yowabu anauza munthuyo kuti: “Ukakamaliza kufotokozera mfumu zonse zokhudza nkhondoyi, 20  mwina mfumu ikakwiya ndipo ikakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mumamenya nkhondo moyandikira mzindawo kwambiri choncho? Simumadziwa kuti akuponyerani mivi kuchokera pamwamba pa mpanda? 21  Ndi ndani anapha Abimeleki+ mwana wa Yerubeseti+ ku Tebezi? Kodi si mkazi amene anali pamwamba pa mpanda yemwe anaponya mwala wa mphero? Nʼchifukwa chiyani munauyandikira kwambiri mpandawo?’ Iwe ukanene kuti, ‘Nayenso mtumiki wanu Uriya Muhiti, wafa.’” 22  Choncho munthuyo anapita, ndipo atafika kwa Davide anafotokoza zonse zimene Yowabu anamutuma. 23  Ndiyeno munthuyo anauza Davide kuti: “Asilikali awo anali amphamvu kuposa ife, ndipo anabwera kudzamenyana nafe kutchire, koma tinayesetsa kulimbana nawo mpaka anabwerera kugeti la mzinda. 24  Koma asilikali ena amaponya mivi kuchokera pamwamba pa mpanda nʼkumabaya atumiki anu, moti atumiki anu ena a mfumu, afa. Nayenso mtumiki wanu Uriya Muhiti, wafa.”+ 25  Davide atamva zimenezi anauza munthuyo kuti: “Ukamuuze Yowabu kuti, ‘Usade nkhawa ndi zimenezi, aliyense akhoza kuphedwa ndi lupanga. Inuyo menyanani ndi anthu amumzindawo mwamphamvu ndipo muwagonjetse.’+ Komanso ukamulimbikitse.” 26  Mkazi wa Uriya atamva kuti mwamuna wake wafa, anayamba kumulira. 27  Nthawi yolira maliro itatha, Davide anatumiza anthu kuti akatenge Bati-seba nʼkubwera naye kunyumba kwake kuti akhale mkazi wake+ ndipo anamuberekera mwana wamwamuna. Koma zimene Davide anachitazi zinamunyansa kwambiri Yehova.+

Mawu a M'munsi

Nʼkutheka kuti ankadziyeretsa atamaliza kusamba kwake kwa pamwezi.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ukasambe mapazi ako.”
Imeneyi inali mphatso imene mfumu inkapereka kwa mlendo wolemekezeka.