2 Samueli 12:1-31

  • Natani anadzudzula Davide (1-15a)

  • Mwana wa Bati-seba anamwalira (15b-23)

  • Bati-seba anabereka Solomo (24, 25)

  • Mzinda wa Aamoni wa Raba unalandidwa (26-31)

12  Yehova anatuma Natani+ kwa Davide. Atafika+ anamuuza kuti: “Panali amuna awiri amene ankakhala mumzinda umodzi. Wina anali wolemera ndipo wina anali wosauka.  Munthu wolemerayo anali ndi nkhosa komanso ngʼombe zambiri.+  Koma munthu wosauka uja anali ndi kamwana ka nkhosa kamodzi kokha kakakazi kamene anagula.+ Iye ankasamalira kamwana ka nkhosako ndipo kankakulira limodzi ndi ana ake. Kankhosako kankadya limodzi ndi munthuyo chakudya chochepa chomwe anali nacho komanso kankamwa naye limodzi. Kankagonanso mʼmanja mwake ndipo kankangokhala ngati mwana wake wamkazi.  Ndiyeno kwa munthu wolemera uja kunabwera mlendo. Koma munthu wolemerayo sanatenge nkhosa kapena ngʼombe yake kuti akonzere chakudya mlendoyo. Mʼmalomwake, anatenga kamwana ka nkhosa ka munthu wosauka uja nʼkuphera mlendoyo.”+  Davide atamva zimenezi anamukwiyira kwambiri munthuyo ndipo anauza Natani kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo,+ munthu amene anachita zimenezi ayenera kufa!  Ndiponso ayenera kubweza ana a nkhosa 4+ chifukwa cha zimene anachitazi komanso chifukwa sanasonyeze chifundo.”  Ndiyeno Natani anauza Davide kuti: “Munthu ameneyu ndi iweyo. Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndinakudzoza kuti ukhale mfumu ya Isiraeli+ ndipo ndinakupulumutsa mʼmanja mwa Sauli.+  Ndinakupatsa nyumba ya mbuye wako+ ndiponso ndinaika akazi a mbuye wako+ mʼmanja mwako. Ndinakupatsanso nyumba ya Isiraeli ndi ya Yuda.+ Zinthu zimenezi zikanakhala kuti sizinakukwanire, ndinali wokonzeka kukuwonjezeranso zina.+  Nʼchifukwa chiyani unanyoza mawu a Yehova pochita zoipa pamaso pake? Unapha Uriya Muhiti ndi lupanga.+ Kenako unatenga mkazi wake kuti akhale mkazi wako+ utapha Uriyayo ndi lupanga la Aamoni.+ 10  Choncho lupanga silidzachoka panyumba yako+ chifukwa wandinyoza potenga mkazi wa Uriya Muhiti kukhala mkazi wako.’ 11  Yehova wanena kuti, ‘Ndikugwetsera tsoka kuchokera mʼnyumba yako+ yomwe komanso iwe ukuona. Ndidzatenga akazi ako nʼkuwapereka kwa mwamuna wina,+ ndipo iye adzagona ndi akazi akowo masanasana.+ 12  Iweyo unachita zimenezi mobisa,+ koma ine ndidzazichita masana Aisiraeli onse akuona.’” 13  Zitatero, Davide anauza Natani kuti: “Ndachimwira Yehova.”+ Natani anauza Davide kuti: “Yehova wakukhululukira tchimo lako+ ndipo suufa.+ 14  Koma chifukwa chakuti wanyoza kwambiri Yehova pochita zimenezi, mwana wako wamwamuna amene wangobadwa kumeneyu afa ndithu.” 15  Kenako Natani anapita kunyumba kwake. Ndiyeno Yehova anachititsa kuti mwana amene mkazi wa Uriya anaberekera Davide ayambe kudwala. 16  Zitatero Davide anachonderera Mulungu woona chifukwa cha mwanayo, ndipo anasiyiratu kudya. Davide akalowa mʼnyumba usiku ankagona pansi.+ 17  Ndiyeno akulu amʼnyumba yake ankabwera pamene wagonapo kuti amudzutse. Koma iye ankakana ndipo sankadya nawo chakudya. 18  Pa tsiku la 7, mwanayo anamwalira. Koma atumiki a Davide ankaopa kumuuza kuti mwanayo wamwalira. Iwo ankanena kuti: “Mwanayu ali moyo, tinalankhula naye Davide koma sanatimvere. Ndiye timuuza bwanji kuti mwana uja wamwalira? Tikamuuza akhoza kuchita chinachake choipa.” 19  Davide ataona kuti atumiki ake akunongʼonezana, anazindikira kuti mwana uja wamwalira. Choncho anafunsa atumiki akewo kuti: “Kodi mwana uja wamwalira?” Iwo anamuyankha kuti: “Inde wamwalira.” 20  Davide atamva zimenezi, anadzuka pamene anagona paja ndipo anasamba nʼkudzola mafuta.+ Kenako anasintha zovala zake nʼkukalowa mʼnyumba+ ya Yehova kukalambira. Atachoka kumeneko anakalowa mʼnyumba yake* nʼkupempha kuti amupatse chakudya ndipo anadya. 21  Atumiki ake anamʼfunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwachita zimenezi? Mwanayu ali moyo, mumakana chakudya ndiponso mumalira. Koma atangomwalira, mwadzuka nʼkuyamba kudya.” 22  Iye anayankha kuti: “Mwanayo ali ndi moyo, ndimasala kudya+ ndipo ndimalira chifukwa ndimaganiza kuti, ‘Angadziwe ndani? Mwina Yehova angandichitire chifundo ndipo angalole kuti mwanayu akhale ndi moyo.’+ 23  Ndiye poti wamwalira, ndisalenso kudya chifukwa chiyani? Kodi ndingamuukitse?+ Inenso tsiku lina ndidzamwalira,+ koma iyeyo sangabwerere kwa ine.”+ 24  Ndiyeno Davide anatonthoza mkazi wake Bati-seba.+ Kenako anagona naye ndipo patapita nthawi, anabereka mwana wamwamuna yemwe anamupatsa dzina lakuti Solomo.*+ Yehova anamʼkonda mwana ameneyu,+ 25  ndipo anatuma mneneri Natani+ kuti akamupatse mwanayo dzina lakuti Yedediya,* chifukwa Yehova anamʼkonda.* 26  Yowabu anapitiriza kumenyana ndi anthu amumzinda wa Raba+ wa Aamoni,+ ndipo analanda mzinda wachifumu.+ 27  Choncho Yowabu anatumiza anthu kuti akauze Davide kuti: “Ndamenyana ndi mzinda wa Raba+ ndipo ndalanda mzinda wa madzi.* 28  Tsopano sonkhanitsani asilikali amene atsala kuti mumenyane ndi anthu amumzindawu nʼkuulanda, chifukwa mukapanda kutero ndiulanda ndine, ndipo dzina langa ndi limene litchuke.” 29  Choncho Davide anasonkhanitsa asilikali onse nʼkupita ku Raba ndipo anamenyana ndi anthu amumzindawo nʼkuulanda. 30  Kenako anatenga chipewa chachifumu chimene chinali kumutu kwa Malikamu* ndipo anthu anaveka Davide chipewacho. Kulemera kwake kunali kofanana ndi talente imodzi* ya golide, ndi miyala yamtengo wapatali. Iye anatenganso zinthu zambirimbiri+ mumzindawo.+ 31  Davide anatenga anthu amene anali mumzindawo nʼkuyamba kuwagwiritsa ntchito yocheka miyala, youmba njerwa komanso ntchito zina zogwiritsa ntchito zitsulo zakuthwa ndi nkhwangwa zachitsulo. Zimenezi ndi zimene anachitira anthu onse amʼmizinda ya Aamoni. Kenako Davide ndi asilikali onse anabwerera ku Yerusalemu.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mʼnyumba yachifumu.”
Kuchokera ku mawu a Chiheberi otanthauza, “Mtendere.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chifukwa cha Yehova.”
Kutanthauza, “Wokondedwa ndi Ya.”
Nʼkutheka kuti akutanthauza malo amene madzi amumzindawo ankachokera.
Ameneyu anali mulungu wa Aamoni.
Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.