2 Samueli 16:1-23

  • Ziba ananamizira Mefiboseti (1-4)

  • Simeyi ananyoza Davide (5-14)

  • Abisalomu anamulandira Husai (15-19)

  • Malangizo a Ahitofeli (20-23)

16  Davide atamaliza kukwera phiri lija,+ anapeza Ziba+ mtumiki wa Mefiboseti+ akumudikira kuti akumane naye. Iye anali ndi abulu awiri okhala ndi zishalo atanyamula mikate 200, makeke 100 a mphesa, makeke 100 a zipatso zamʼchilimwe* ndiponso mtsuko waukulu wa vinyo.+  Ndiyeno mfumu inafunsa Ziba kuti: “Nʼchifukwa chiyani wabweretsa zinthu zimenezi?” Ziba anayankha kuti: “Abuluwa ndatengera anthu amʼnyumba ya mfumu kuti azikwerapo, mikate ndi makeke a zipatso zamʼchilimwezi ndatengera anyamata kuti adye ndipo vinyoyu ndatenga kuti anthu amene atopa mʼchipululu, azimwa.”+  Kenako mfumu inafunsa kuti: “Nanga mwana* wa mbuye wako ali kuti?”+ Ziba anauza mfumu kuti: “Watsala ku Yerusalemu ndipo wanena kuti, ‘Lero nyumba ya Isiraeli indibwezera ufumu wa bambo anga.’”+  Kenako mfumu inauza Ziba kuti: “Zinthu zonse zimene zinali za Mefiboseti zikhale zako.”+ Ziba anati: “Ulemu wanu mfumu. Pitirizani kundikomera mtima mbuyanga mfumu.”+  Mfumu Davide itafika ku Bahurimu, mwamuna wina wa mʼbanja la Sauli, dzina lake Simeyi,+ mwana wa Gera anatulukira akulankhula mawu onyoza.+  Iye anayamba kugenda Davide, atumiki onse a Mfumu Davide, anthu onse komanso amuna onse amphamvu amene anali kumanja ndi kumanzere kwa mfumu.  Simeyi ankanena kuti: “Choka! Choka! Munthu wa mlandu wa magazi ndiponso wopanda pake iwe!  Yehova wakubwezera mlandu wa magazi a nyumba ya Mfumu Sauli amene iwe unamulowa mʼmalo. Yehova wapereka ufumu mʼmanja mwa Abisalomu mwana wako. Ndipo tsoka lakugwera chifukwa uli ndi mlandu wa magazi!”+  Kenako Abisai mwana wa Zeruya+ anauza mfumu kuti: “Nʼchifukwa chiyani galu wakufayu+ akukunyozani mbuyanga mfumu?+ Bwanji ndipite ndikamʼdule mutu?”+ 10  Koma mfumu inati: “Ndili nanu chiyani inu ana a Zeruya?+ Musiyeni anyoze+ chifukwa Yehova wamuuza kuti,+ ‘Munyoze Davide!’ Ndiye ndi ndani angamufunse kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukuchita zimenezi?’” 11  Kenako Davide anauza Abisai ndi atumiki ake onse kuti: “Ngati mwana wanga weniweni, wobereka ndekha akufunafuna moyo wanga,+ kuli bwanji munthu wa fuko la Benjaminiyu?+ Musiyeni anyoze, chifukwa Yehova ndi amene wamuuza. 12  Mwina Yehova aona mavuto anga,+ ndipo Yehova adzabwezeretsa zabwino kwa ine mʼmalo mwa zimene Simeyi akunena lero pondinyoza.”+ 13  Choncho Davide ndi amuna amene anali naye anapitiriza ulendo wawo. Simeyi ankayenda mʼmbali mwa phiri pafupi ndi Davide, uku akulankhula mawu onyoza,+ kugenda ndi miyala ndiponso kuwaza fumbi lambiri. 14  Patapita nthawi, mfumu ndi anthu onse amene anali naye anafika kumene ankapita atatopa kwambiri ndipo anayamba kupuma. 15  Abisalomu ndi amuna onse a Isiraeli, anafika ku Yerusalemu ndipo Ahitofeli+ anali naye limodzi. 16  Husai+ mbadwa ya Areki,+ mnzake wa Davide, atafika kwa Abisalomu anauza Abisalomu kuti: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!+ Mfumu ikhale ndi moyo wautali!” 17  Zitatero Abisalomu anafunsa Husai kuti: “Kodi zimene wachitazi wamusonyeza mnzako chikondi chokhulupirika? Nʼchifukwa chiyani sunapite naye limodzi mnzakoyo?” 18  Husai anayankha Abisalomu kuti: “Ayi, ine ndili kumbali ya munthu amene wasankhidwa ndi Yehova komanso amene wasankhidwa ndi anthu awa ndiponso amuna onse a mu Isiraeli. Ine ndidzakhala ndi ameneyo. 19  Ndibwereze kunena kuti, ndingatumikirenso ndani? Ndiyenera kutumikira mwana wake. Ine ndikutumikirani inuyo ngati mmene ndinkachitira ndi bambo anu.”+ 20  Kenako Abisalomu anauza Ahitofeli kuti: “Ndipatseni malangizo.+ Tichite chiyani?” 21  Ahitofeli anauza Abisalomu kuti: “Ugone ndi akazi aangʼono* a bambo ako+ amene awasiya kuti azisamalira nyumba.*+ Ukatero Aisiraeli onse adzamva kuti wadzinunkhitsa pamaso pa bambo ako, ndipo udzapatsa mphamvu anthu amene ali kumbali yako.” 22  Choncho anamangira Abisalomu tenti padenga,+ ndipo Abisalomu anayamba kugona ndi akazi aangʼono a bambo ake,+ Aisiraeli onse akuona.+ 23  Pa nthawiyo, malangizo a Ahitofeli+ ankaonedwa ngati mawu ochokera kwa Mulungu woona. Umu ndi mmene Davide ndi Abisalomu ankaonera malangizo onse a Ahitofeli.

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “zipatso zamʼchilimwe” makamaka akutanthauza nkhuyu, koma angatanthauzenso zipatso za kanjedza.
Kapena kuti, “mdzukulu.”
Kapena kuti, “adzakazi.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”