2 Samueli 17:1-29

  • Husai anasokoneza malangizo a Ahitofeli (1-14)

  • Davide anachenjezedwa ndipo anathawa Abisalomu (15-29)

    • Barizilai ndi anthu ena anapereka zakudya (27-29)

17  Ndiyeno Ahitofeli anauza Abisalomu kuti: “Bwanji ndisankhe amuna 12,000 kuti usiku uno ndikasakesake Davide?  Ndikamupeza atatopa komanso alibe mphamvu*+ ndipo ndikamupanikiza. Zikakatero, anthu onse amene ali naye akathawa ndipo ine ndikapha mfumu yokhayo.+  Ndiyeno ndibweretsa anthu onse kwa inu. Zimene zingachitikire munthu amene mukumusakasakayu, ndi zomwe zingachititse kuti anthu onse abwerere. Kenako anthu onse adzakhala mwamtendere.”  Maganizo amenewa anasangalatsa Abisalomu ndi akulu onse a Isiraeli.  Komabe Abisalomu anati: “Tumani munthu akaitane Husai+ mbadwa ya Areki kuti timvenso maganizo ake.”  Choncho Husai anabwera kwa Abisalomu. Ndiyeno Abisalomu anamuuza kuti: “Ahitofeli wapereka malangizo amenewa. Kodi tichite zimene wanenazi? Ngati ayi, iweyo tiuze zochita.”  Husai anauza Abisalomu kuti: “Malangizo amene Ahitofeli wapereka ulendo uno, si abwino.”+  Husai ananenanso kuti: “Inu mukudziwa bwino kuti bambo anu ndi amuna amene ali nawo, onse ndi amphamvu+ ndipo mitima ikuwapweteka ngati chimbalangondo chimene ana ake asowa mʼtchire.+ Komanso bambo anu ndi munthu wodziwa nkhondo+ ndipo sangagone kumene kuli anthu.  Panopa akubisala mʼphanga kapena mʼmalo ena.+ Ngati iwowo angakhale oyamba kuukira gulu lanu, nkhani idzafala kuti, ‘Anthu amene akutsatira Abisalomu agonjetsedwa.’ 10  Zikatero, ngakhale mwamuna wolimba mtima ngati mkango+ adzachita mantha kwambiri. Chifukwa Aisiraeli onse akudziwa kuti bambo anu ndi munthu wamphamvu+ ndipo amuna amene ali nawo ndi olimba mtima. 11  Malangizo anga ndi akuti: Musonkhanitse Aisiraeli onse kuyambira ku Dani mpaka ku Beere-seba.+ Akhale ambiri ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja+ ndipo inuyo muwatsogolere kunkhondo. 12  Tikawaukira kulikonse kumene ali, ndipo tikafika ngati mmene mame amagwera pansi. Sipakakhala opulumuka, kaya bambo anuwo kapena anthu onse amene ali nawo. 13  Ngati angathawire mumzinda uliwonse, ife tidzapita ndi Aisiraeli onse nʼkukaukokera kuchigwa ndi zingwe. Mumzindawo simudzatsala ngakhale mwala wa nkhulungo.” 14  Kenako Abisalomu ndi amuna onse a Isiraeli anati: “Malangizo a Husai mbadwa ya Areki ndi abwino+ kusiyana ndi a Ahitofeli.”+ Yehova anaonetsetsa kuti anthuwo asatsatire malangizo a Ahitofeli ngakhale kuti anali abwino. Yehova anachita zimenezi kuti abweretsere Abisalomu tsoka.+ 15  Kenako Husai anauza Zadoki ndi Abiyatara+ ansembe kuti: “Ahitofeli wapereka malangizo akutiakuti kwa Abisalomu ndi akulu a Isiraeli koma ine ndapereka malangizo akutiakuti. 16  Ndiye tumizani uthenga mwamsanga kwa Davide wakuti, ‘Usiku uno musakhale pamalo owolokera kuchipululu. Koma muwoloke ndithu chifukwa mukapanda kutero inu mfumu ndi anthu onse amene muli nawo, muphedwa.’”+ 17  Yonatani+ ndi Ahimazi+ ankakhala ku Eni-rogeli+ ndipo wantchito wamkazi anapita kukawauza uthengawu. Choncho iwo ananyamuka kuti akauze Mfumu Davide. Iwo sanafune kuti anthu awaone akulowa mumzinda. 18  Komabe mnyamata wina anawaona ndipo anapita kukauza Abisalomu. Choncho anthu awiriwo anachoka mofulumira nʼkupita kunyumba kwa munthu wina amene anali ndi chitsime pakhomo pake ku Bahurimu,+ ndipo analowa mʼchitsimemo. 19  Ndiyeno mkazi wa munthuyo anatenga chinsalu nʼkuchiyala pamwamba pa chitsimepo, kenako anaunjikapo tirigu wosinja, ndipo palibe amene anadziwa chilichonse. 20  Atumiki a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo nʼkufunsa kuti: “Kodi Ahimazi ndi Yonatani ali kuti?” Mkaziyo anayankha kuti: “Adutsa pano kulowera kumtsinje.”+ Zitatero anthuwo anawafunafuna koma sanawapeze, choncho anabwerera ku Yerusalemu. 21  Anthuwo atachoka, Ahimazi ndi Yonatani anatuluka mʼchitsimemo nʼkupita kukauza Mfumu Davide kuti: “Nyamukani mwamsanga ndipo muwoloke mtsinje.” Kenako anawauza malangizo amene Ahitofeli anapereka.+ 22  Nthawi yomweyo Davide ananyamuka pamodzi ndi anthu onse amene anali naye, ndipo anawoloka Yorodano. Pofika mʼbandakucha, aliyense anali atawoloka Yorodano. 23  Ahitofeli ataona kuti malangizo ake sanatsatiridwe, anakwera bulu nʼkupita kunyumba yake mʼtauni yakwawo.+ Kenako anapereka malangizo kwa anthu amʼbanja lake+ ndipo atatero anadzimangirira.+ Iye anafa ndipo anaikidwa mʼmanda a makolo ake. 24  Davide anapita ku Mahanaimu+ ndipo Abisalomu anawoloka Yorodano pamodzi ndi amuna onse a Isiraeli. 25  Ndiyeno Abisalomu anasankha Amasa+ kukhala mtsogoleri wa asilikali mʼmalo mwa Yowabu.+ Amasa anali mwana wa munthu wina wa Chiisiraeli dzina lake Itara yemwe anagona ndi Abigayeli+ mwana wamkazi wa Nahasi, mchemwali wake wa Zeruya, mayi ake a Yowabu. 26  Aisiraeli ndi Abisalomu anamanga msasa ku Giliyadi.+ 27  Davide atangofika ku Mahanaimu, Sobi mwana wamwamuna wa Nahasi wochokera ku Raba+ mzinda wa Aamoni, Makiri+ mwana wa Amiyeli wochokera ku Lo-debara komanso Barizilai+ wa ku Giliyadi wochokera ku Rogelimu, 28  anabweretsa mabedi, mabeseni, miphika, tirigu, balere, ufa, nyemba zikuluzikulu, mphodza, mbewu zina zokazinga, 29  uchi, nkhosa, bata ndiponso tchizi.* Anabweretsa zinthu zimenezi kuti Davide ndi anthu onse amene anali naye adye.+ Iwo ankati: “Anthuwa ali mʼchipululu ndipo ali ndi njala, ali ndi ludzu komanso atopa.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Ndikamupeza manja ake onse atafooka.”
Bata komanso tchizi ndi zakudya zopangidwa kuchokera ku mkaka.