2 Samueli 18:1-33

  • Abisalomu anagonjetsedwa ndipo anafa (1-18)

  • Davide anauzidwa za imfa ya Abisalomu (19-33)

18  Ndiyeno Davide anawerenga amuna amene anali naye nʼkusankha atsogoleri a magulu a anthu 1,000 ndi atsogoleri a magulu a anthu 100.+  Atatero, Davide anagawa anthuwo mʼmagulu atatu. Gulu loyamba analipereka kwa Yowabu,+ gulu lachiwiri analipereka kwa Abisai+ mwana wa Zeruya,+ mchimwene wake wa Yowabu, ndipo gulu lachitatu analipereka kwa Itai+ wa ku Gati. Kenako mfumu inauza anthuwo kuti: “Inenso ndipita nanu.”  Koma anthuwo anati: “Ayi musapite,+ chifukwa ngati tingakathawe, sakalimbana ndi ife. Ndipo ngati hafu ya ife ingakafe, sakakhutira nazo chifukwa inuyo ndinu wofunika kuposa asilikali 10,000.+ Choncho zingakhale bwino kuti muzitithandiza muli mumzinda momʼmuno.”  Mfumu inawauza kuti: “Ndichita zilizonse zimene inu mukuona kuti nʼzabwino.” Choncho mfumu inaima pafupi ndi geti ndipo anthu onsewo anapita kunkhondo mʼmagulu a anthu 100 ndi 1,000.  Ndiyeno mfumu inalamula Yowabu, Abisai ndi Itai kuti: “Musakachitire nkhanza Abisalomu chifukwa mwana ameneyu ndimamukonda.”+ Anthu onse anamva zimene mfumu inalamula atsogoleriwa zokhudza Abisalomu.  Anthu ananyamuka ulendo wawo wopita kukamenyana ndi Aisiraeli ndipo nkhondo inayambika mʼnkhalango ya Efuraimu.+  Aisiraeli+ anagonjetsedwa ndi atumiki a Davide+ ndipo pa tsikuli panaphedwa anthu ambiri moti anakwana 20,000.  Nkhondoyi inafalikira dera lonselo. Komanso pa tsiku limeneli anthu amene anafera mʼnkhalango anali ambiri kuposa amene anaphedwa ndi lupanga.  Kenako Abisalomu anakumana ndi atumiki a Davide. Abisalomu anali atakwera nyulu,* ndipo nyuluyo inadutsa pansi pa ziyangoyango za nthambi za mtengo waukulu kwambiri. Choncho mutu wa Abisalomu unakola muziyangoyangozo koma nyulu imene anakwerapoyo inadutsa moti inamusiya akulendewera. 10  Ndiyeno munthu wina anaona zimenezo nʼkupita kukauza Yowabu kuti:+ “Ndaona Abisalomu ali lende mumtengo waukulu.” 11  Yowabu anafunsa munthuyo kuti: “Ngati wamuona, bwanji sunamuphe nthawi yomweyo? Ukanamupha, ndikanasangalala kwambiri ndipo ndikanakupatsa ndalama 10 zasiliva komanso lamba.” 12  Koma munthuyo anauza Yowabu kuti: “Ngakhale ndikanalandira ndalama 1,000 zasiliva, sindikanapha mwana wa mfumu. Paja tinamva mfumu ikukulamulani inuyo, Abisai ndi Itai kuti, ‘Aliyense asakaphe Abisalomu.’+ 13  Ndikanapanda kumvera nʼkumupha, zikanadziwika kwa mfumu ndipo inuyo simukanandiikira kumbuyo.” 14  Koma Yowabu anati: “Usandichedwetse iwe!” Atatero anatenga zobayira* zitatu ndipo anakabaya Abisalomu pamtima ali moyo pakati pa ziyangoyango za mtengo waukulu. 15  Kenako atumiki 10 onyamula zida za Yowabu anabwera nʼkudzamalizitsa kupha Abisalomu.+ 16  Zitatero, Yowabu analiza lipenga la nyanga ya nkhosa ndipo anthu anasiya kuthamangitsa Aisiraeli. Choncho Yowabu anauza anthuwo kuti asiye kumenya nkhondo. 17  Atatero, anatenga Abisalomu nʼkumuponya mʼdzenje lalikulu mʼnkhalangomo ndipo anaunjikapo mulu waukulu kwambiri wa miyala.+ Koma Aisiraeli onse anathawa nʼkupita kunyumba kwawo. 18  Abisalomu ali moyo, anamanga chipilala chake mʼChigwa cha Mfumu,+ popeza iye anati: “Ine ndilibe mwana wamwamuna woti asunge dzina langa kuti ndizikumbukiridwa.”+ Choncho chipilalacho anachipatsa dzina lake ndipo chikudziwikabe ndi dzina lakuti Chipilala cha Abisalomu mpaka lero. 19  Ndiyeno Ahimazi+ mwana wa Zadoki anati: “Bwanji ndithamange ndikapereke uthengawu kwa mfumu, chifukwa Yehova wachitira mfumu chilungamo poilanditsa mʼmanja mwa adani ake?”+ 20  Koma Yowabu anamuuza kuti: “Iwe sukapereka uthenga lero, udzapereka tsiku lina. Lero sukapereka uthenga chifukwa mwana wa mfumu wafa.”+ 21  Ndiyeno Yowabu anauza munthu wina wa ku Kusi* kuti:+ “Pita ukauze mfumu zimene waona.” Munthuyo anaweramira Yowabu nʼkuyamba kuthamanga. 22  Ahimazi mwana wa Zadoki anauzanso Yowabu kuti: “Kaya chichitike nʼchiyani, koma bwanji inenso ndithamange kutsatira munthu wa ku Kusi uja?” Koma Yowabu anati: “Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani iwenso ukufuna kupita chonsecho palibe uthenga woti ukanene?” 23  Iye anaumirira nʼkunena kuti: “Kaya chichitike nʼchiyani, koma bwanji nanenso ndithamange?” Choncho Yowabu anati: “Thamanga!” Atatero Ahimazi anayamba kuthamanga kudutsa njira yakuchigawo cha Yorodano ndipo anamupitirira munthu wa ku Kusi uja. 24  Davide anali atakhala pakati pa mageti awiri a mzinda+ ndipo mlonda+ anakwera padenga la geti lolumikizana ndi mpanda. Ndiyeno anaona munthu akuthamanga ali yekha. 25  Choncho mlondayo anafuula nʼkuuza mfumu zimenezo. Mfumuyo inati: “Ngati ali yekha, ndiye kuti akudzanena uthenga.” Munthu uja atayandikira, 26  mlondayo anaonanso munthu wina akuthamanga. Ndiyeno mlondayo anafuula nʼkuuza mlonda wapageti kuti: “Munthu winanso akuthamanga, ali yekha.” Mfumu inati: “Ameneyunso akubweretsa uthenga.” 27  Mlondayo anati: “Mmene munthu woyambayo akuthamangira, ndikuona ngati ndi Ahimazi+ mwana wa Zadoki.” Atatero, mfumu inati: “Ahimazi ndi munthu wabwino, ndipo amabwera ndi uthenga wabwino.” 28  Kenako Ahimazi anauza mfumu kuti: “Zonse zili bwino!” Atatero anagwadira mfumuyo nʼkuwerama mpaka nkhope yake kufika pansi. Ndiyeno anati: “Atamandike Yehova Mulungu wanu, amene wapereka anthu amene anakuukirani inu mbuyanga mfumu!”+ 29  Koma mfumu inati: “Kodi mwana wanga Abisalomu ali bwino?” Ahimazi anayankha kuti: “Pamene Yowabu amatuma mtumiki wanu mfumu komanso ineyo, ndinaona chipwirikiti chachikulu, koma sindinadziwe kuti chikuchitika nʼchiyani.”+ 30  Choncho mfumu inati: “Ima pambalipa.” Iye anachoka nʼkuima pambali. 31  Kenako munthu wa ku Kusi uja anafika,+ ndipo ananena kuti: “Ndabweretsa uthenga mbuyanga mfumu. Lero Yehova wakuchitirani chilungamo pokulanditsani mʼmanja mwa anthu onse amene anakuukirani.”+ 32  Koma mfumu inafunsa munthuyo kuti: “Kodi mwana wanga Abisalomu ali bwino?” Iye anayankha kuti: “Adani anu onse mbuyanga mfumu ndiponso anthu onse amene anakuukirani kuti akuchitireni zoipa, akhale ngati iyeyo.”+ 33  Zimenezi zinakhumudwitsa kwambiri mfumu ndipo inapita mʼchipinda chapadenga chapageti nʼkuyamba kulira, uku ikuyendayenda. Mfumu inkanena kuti: “Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga Abisalomu! Zikanakhala bwino ndikanafa ineyo mʼmalo mwa iwe, Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!”+

Mawu a M'munsi

“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.
Mabaibulo ena amati, “mikondo.” Mʼchilankhulo choyambirira, “ndodo.”
Kapena kuti, “Ethiopia.”