2 Samueli 19:1-43

  • Davide analira Abisalomu (1-4)

  • Yowabu anadzudzula Davide (5-8a)

  • Davide anabwerera ku Yerusalemu (8b-15)

  • Simeyi anapempha kuti amukhululukire (16-23)

  • Mefiboseti anasonyeza kuti anali wosalakwa (24-30)

  • Barizilai analemekezedwa (31-40)

  • Mkangano pakati pa mafuko (41-43)

19  Anthu ena anakauza Yowabu kuti: “Mfumu ikulira Abisalomu.”+  Choncho pa tsikuli anthu onse anali pa chisoni mʼmalo mosangalala kuti apambana kunkhondo chifukwa anamva kuti: “Mfumu ikulira maliro a mwana wake.”  Tsiku limenelo anthu analowa mumzinda mwakachetechete+ ngati anthu amene akuchita manyazi chifukwa choti athawa kunkhondo.  Ndiyeno mfumu inaphimba nkhope yake ndipo inkalirabe mokweza kuti: “Mwana wanga Abisalomu! Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!”+  Kenako Yowabu anapita kunyumba ya mfumu nʼkuiuza kuti: “Lero mwachititsa manyazi atumiki anu onse amene apulumutsa moyo wanu, wa ana anu aamuna,+ ana anu aakazi,+ akazi anu komanso akazi anu aangʼono.*+  Mumakonda anthu amene amadana nanu ndipo mumadana ndi amene amakukondani. Lero mwasonyeza kuti atumiki anu ndi atsogoleri mulibe nawo ntchito ndipo sindikukayikira kuti Abisalomu akanakhala moyo koma ena tonsefe nʼkufa, simukanadandaula.  Ndiye nyamukani, mupite mukalimbikitse atumiki anu, chifukwa ngati simupita, ndithu ndikulumbira mʼdzina la Yehova, palibe munthu amene atsale ndi inu usiku uno. Zimenezi zikhala zoipa kwambiri kwa inu kuposa zoipa zonse zimene mwakumana nazo kuyambira muli mnyamata.”  Choncho mfumu inanyamuka nʼkukakhala pageti. Kenako anthu onse anauzidwa kuti: “Mfumu yakhala pageti.” Ndiyeno anthu anabwera pamene panali mfumuyo. Koma Aisiraeli anali atathawira kunyumba zawo.+  Anthu a mʼmafuko onse a Isiraeli anayamba kukangana ndipo ankati: “Mfumuyi ndi imene inatipulumutsa kwa adani athu+ komanso kwa Afilisiti. Koma panopa yathawa mʼdziko lino chifukwa cha Abisalomu.+ 10  Ndiye Abisalomu amene tinamudzoza kuti akhale mtsogoleri wathu+ wafa kunkhondo.+ Nanga nʼchifukwa chiyani simukuchita chilichonse kuti mfumu ibwerere?” 11  Mfumu Davide inatumiza uthenga kwa Zadoki+ ndi Abiyatara+ ansembe wakuti: “Muwafunse akulu a Yuda+ kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani inu nokha simukuchita chilichonse kuti mfumu ibwerere kunyumba yake, pamene Aisiraeli onse atumiza uthenga kwa mfumu? 12  Inu ndinu abale anga ndipo ndife magazi amodzi.* Ndiye nʼchifukwa chiyani inu nokha simukuchita chilichonse kuti mfumu ibwerere?’ 13  Amasa mumuuze kuti,+ ‘Iwe ndi ine ndife magazi amodzi. Mulungu andilange mowirikiza ngati sindikuika kukhala mtsogoleri wa gulu langa lankhondo mʼmalo mwa Yowabu.’”+ 14  Choncho amuna onse a Yuda anakopeka ndipo anamvana chimodzi, moti anatumiza uthenga kwa mfumu wakuti: “Bwererani pamodzi ndi atumiki anu onse.” 15  Ndiyeno mfumu inayamba kubwerera kwawo ndipo inafika ku Yorodano. Anthu a ku Yuda anabwera ku Giligala+ kudzakumana ndi mfumu komanso kuti aiperekeze powoloka mtsinje wa Yorodano. 16  Kenako Simeyi+ mwana wa Gera wa ku Bahurimu, wa fuko la Benjamini, anathamangira amuna a ku Yuda nʼkupita nawo kukakumana ndi Mfumu Davide. 17  Iye anali ndi amuna 1,000 a ku Benjamini. Nayenso Ziba,+ mtumiki wa nyumba ya Sauli, ndi ana ake 15 komanso atumiki ake 20 anayenda mofulumira nʼkukafika ku Yorodano mfumu isanafike. 18  Iye* atafika, anawolokera tsidya lina kuti akawolotse anthu a mʼbanja la mfumu komanso kuchita zilizonse zimene mfumuyo ingafune. Koma mfumu itatsala pangʼono kuwoloka Yorodano, Simeyi mwana wa Gera, anagwada pamaso pake. 19  Ndiyeno anauza mfumu kuti: “Mbuyanga, mundikhululukire zimene ndinalakwitsa. Musakumbukire zoipa zimene ine mtumiki wanu+ ndinachita tsiku limene inu mbuyanga mfumu munkachoka ku Yerusalemu. Musasunge zimenezi mumtima mwanu mfumu. 20  Ine mtumiki wanu ndikudziwa kuti ndinachimwa, nʼchifukwa chake lero ndakhala woyamba mʼnyumba yonse ya Yosefe kubwera kuno kudzakumana nanu mbuyanga mfumu.” 21  Nthawi yomweyo Abisai+ mwana wa Zeruya anati:+ “Pa zimene wanenazi, kodi Simeyi sakuyenera kuphedwa chifukwa choti anatemberera wodzozedwa wa Yehova?”+ 22  Koma Davide anati: “Chikukukhudzani nʼchiyani inu ana a Zeruya+ kuti lero muzitsutsana ndi ine? Kodi mu Isiraeli muyenera kuphedwa munthu lero? Kodi ine sindikudziwa kuti lero ndine mfumu ya Isiraeli?” 23  Kenako mfumu inauza Simeyi kuti: “Suufa.” Ndipo mfumu inamulumbirira.+ 24  Nayenso Mefiboseti,+ mdzukulu wa Sauli, anabwera kudzaonana ndi mfumu. Kuchokera tsiku limene mfumu inachoka mpaka tsiku lomwe inabwerera mwamtendere, iye sanasambe mapazi ake, sanamete ndevu zapamulomo ndiponso sanachape zovala zake. 25  Atafika* ku Yerusalemu kukakumana ndi mfumu, mfumuyo inamufunsa kuti: “Mefiboseti, nʼchifukwa chiyani sunapite nane?” 26  Iye anayankha kuti: “Mbuyanga mfumu, mtumiki wanga+ ndi amene anandipusitsa. Ine mtumiki wanu ndinamuuza kuti, ‘Ndiikireni chishalo pabulu ndikwerepo kuti ndipite limodzi ndi mfumu,’ chifukwa ine mtumiki wanu ndine wolumala.+ 27  Koma mtumiki wangayo anakuuzani inu mbuyanga mfumu+ zinthu zabodza zokhudza ine mtumiki wanu. Komabe inu mbuyanga muli ngati mngelo wa Mulungu woona, choncho chitani zilizonse zomwe mukuona kuti nʼzabwino. 28  Inu mbuyanga mfumu, mukanatha kupha anthu onse a mʼnyumba ya bambo anga. Koma munaika ine mtumiki wanu mʼgulu la anthu amene amadya patebulo lanu.+ Choncho ndilibe chifukwa chomveka kuti ndipitirize kudandaula kwa inu mfumu.” 29  Koma mfumu inamuuza kuti: “Usavutike ndi kulankhula zonsezo. Ine ndikulamula kuti iwe ndi Ziba mugawane malo aja.”+ 30  Mefiboseti anayankha mfumu kuti: “Musiyeni atenge malo onsewo, kwa ine zili bwino chifukwa inu mbuyanga mfumu mwabwerera kunyumba yanu mwamtendere.” 31  Ndiyeno Barizilai+ wa ku Giliyadi anabwera kudera la Yorodano kuchokera ku Rogelimu kuti adzaperekeze mfumu mpaka kuwoloka mtsinje wa Yorodano. 32  Barizilai anali ndi zaka 80 ndipo anali wokalamba kwambiri. Pamene Mfumu Davide anali ku Mahanaimu,+ Barizilai ankamupatsa chakudya popeza anali wolemera kwambiri. 33  Ndiyeno mfumu inauza Barizilai kuti: “Tiyeni tiwoloke limodzi tipite ku Yerusalemu ndipo ndizikakupatsani chakudya.”+ 34  Koma Barizilai anauza mfumu kuti: “Kodi masiku a moyo wanga atsala angati kuti ndipite ku Yerusalemu pamodzi ndi mfumu? 35  Panopa ndili ndi zaka 80.+ Kodi ndingasiyanitse chabwino ndi choipa? Kodi ine mtumiki wanu ndingamve kukoma kwa zakudya ndi zakumwa? Nanga ndingathenso kumvetsera nyimbo za amuna ndi akazi oimba?+ Ndiye ine mtumiki wanu ndikulemetseni chifukwa chiyani mbuyanga mfumu? 36  Zili bwino kuti ine mtumiki wanu ndakuperekezani kudzafika ku Yorodano kuno. Ndiye nʼchifukwa chiyani inu mfumu mukufuna kundipatsa mphoto imeneyi? 37  Ndiloleni ine mtumiki wanu ndibwerere ndikafere mumzinda wakwathu pafupi ndi manda a bambo ndi mayi anga.+ Koma mukhoza kuwoloka ndi mtumiki wanu Chimamu+ kuti mupite naye limodzi mbuyanga mfumu, ndipo mukamuchitire zilizonse zimene mukuona kuti nʼzabwino.” 38  Mfumu inati: “Chimamu ndipita naye limodzi, ndipo ine ndikamuchitira zimene mukuona kuti nʼzabwino. Chilichonse chimene mudzapemphe kuti ndikuchitireni, ndidzakuchitirani.” 39  Kenako anthu onse anayamba kuwoloka Yorodano, ndipo mfumu itawoloka, inakisa Barizilai+ nʼkumudalitsa. Zitatero, Barizilai anabwerera kwawo. 40  Pamene mfumu inkawoloka kupita ku Giligala,+ Chimamu anapita nawo. Ayuda onse komanso hafu ya anthu a ku Isiraeli anaperekeza mfumu.+ 41  Kenako anthu ena a ku Isiraeli anabwera kwa mfumu nʼkunena kuti: “Nʼchifukwa chiyani abale athu a ku Yuda akubweretsani mozemba inu mfumu, pamodzi ndi banja lanu komanso anthu onse amene munali nawo kutsidya la Yorodano?”+ 42  Anthu a ku Yuda anayankha anthu a ku Isiraeli kuti: “Chifukwa chakuti mfumuyi ndi wachibale wathu.+ Ndiye inu mwakwiya nazo chifukwa chiyani? Kodi ife tadya zinthu zilizonse za mfumu kapena kulandira mphatso?” 43  Koma anthu a ku Isiraeli anayankha anthu a ku Yuda kuti: “Ifetu tili ndi mafuko 10 mu ufumu wa Davide, choncho tili ndi mphamvu zambiri kuposa inuyo. Ndiye nʼchifukwa chiyani mwatinyoza chonchi? Kodi ife sitinayenera kukhala patsogolo pobweretsa mfumu yathu?” Koma anthu a ku Isiraeliwo anagonja chifukwa cha zimene anthu a ku Yuda ananena.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “adzakazi.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo ndine fupa lanu ndi mnofu wanu.”
Mabaibulo ena amati, “Iwo.”
Mabaibulo ena amati, “Atachokera.”