2 Samueli 20:1-26

  • Sheba anaukira Davide; Yowabu anapha Amasa (1-13)

  • Anthu anasakasaka Sheba ndipo anadulidwa mutu (14-22)

  • Ulamuliro wa Davide (23-26)

20  Ndiyeno panali munthu wina wosokoneza dzina lake Sheba,+ mwana wamwamuna wa Bikiri,+ wafuko la Benjamini. Iye analiza lipenga la nyanga ya nkhosa nʼkunena kuti: “Ife Davide tilibe naye ntchito ndipo sitingapatsidwe cholowa kuchokera kwa mwana wa Jese.+ Aisiraeli inu, aliyense apite kwa milungu* yake!”+  Zitatero, anthu onse a Isiraeli anachoka kwa Davide nʼkuyamba kutsatira Sheba mwana wa Bikiri.+ Koma anthu a ku Yuda, kuyambira ku Yorodano mpaka ku Yerusalemu, anakhalabe ndi mfumu yawo.+  Mfumu Davide atafika kunyumba yake* ku Yerusalemu,+ anatenga akazi ake aangʼono 10, amene anawasiya kuti azisamalira nyumba yake aja+ nʼkuwatsekera mʼnyumba ina ndipo anaikapo alonda. Iye ankawapatsa chakudya koma sanagone nawo.+ Iwo anapitiriza kukhala mʼnyumbamo mpaka tsiku limene anamwalira. Ankakhala ngati akazi amasiye ngakhale kuti mwamuna wawo anali moyo.  Mfumu inauza Amasa kuti:+ “Uitane amuna onse mu Yuda kuti asonkhane kuno pasanathe masiku atatu, ndipo iwenso ubwere.”  Choncho Amasa anapita kukaitana anthu a mu Yuda, koma anabwera mochedwa osati pa nthawi imene anauzidwa.  Ndiyeno Davide anauza Abisai kuti:+ “Sheba+ mwana wamwamuna wa Bikiri ativutitsa kwambiri kuposa Abisalomu.+ Ndiye utenge atumiki a mbuye wako ndipo mukamusake kuti asapeze mizinda ya mipanda yolimba kwambiri nʼkubisala.”  Choncho asilikali a Yowabu,+ Akereti, Apeleti+ ndi amuna onse amphamvu anayamba kumusakasaka. Iwo anachoka ku Yerusalemu nʼkupita kukafunafuna Sheba mwana wa Bikiri.  Atatsala pangʼono kufika pamwala waukulu umene uli ku Gibiyoni,+ Amasa+ anabwera kudzakumana nawo. Yowabu anali atavala zovala zankhondo ndipo anaika lupanga mʼchimake nʼkulikoleka mʼchiuno mwake. Atayandikira Amasa, lupangalo linagwa.  Ndiyeno Yowabu anafunsa Amasa kuti: “Uli bwanji mʼbale wanga?” Kenako Yowabu anagwira ndevu za Amasa ndi dzanja lake lamanja ngati akufuna kumukisa. 10  Koma Amasa sanali tcheru ndi lupanga limene linali mʼmanja mwa Yowabu. Choncho Yowabuyo anamubaya nalo mʼmimba+ ndipo matumbo ake anakhuthukira pansi. Anangomubaya kamodzi nʼkuferatu, sanachite kumubaya kawiri. Kenako Yowabu ndi mchimwene wake Abisai anapitiriza kusaka Sheba mwana wa Bikiri. 11  Mnyamata wina wa Yowabu anaima pafupi ndi Amasa ndipo ankanena kuti: “Aliyense amene ali kumbali ya Yowabu komanso ya Davide, atsatire Yowabu!” 12  Pa nthawiyi nʼkuti mtembo wa Amasa uli kwala pamagazi ake, pakati pa msewu. Mnyamata uja ataona kuti anthu onse akumaima pamalopo, anachotsa mtembo wa Amasa nʼkuuika patchire. Kenako anauphimba ndi chovala chifukwa anaona kuti aliyense akafika pamalowo, ankaima. 13  Atangomuchotsa pamsewupo, aliyense ankangodutsa kutsatira Yowabu pokasaka Sheba+ mwana wa Bikiri. 14  Tsopano Sheba anadutsa mafuko onse a Isiraeli nʼkukafika kumzinda wa Abele wa ku Beti-maaka.+ Nawonso Abikiri onse anasonkhana nʼkuyamba kumutsatira. 15  Yowabu ndi asilikali ake* anafika nʼkuzungulira mzinda wa Abele wa ku Beti-maaka womwe unazunguliridwa ndi malo okwera amene anthu amumzindawo anamanga. Yowabu ndi asilikali ake anamanganso malo okwera omenyerapo nkhondo. Anthu onse amene anali ndi Yowabu ankakumba pansi pa mpandawo kuti augwetse. 16  Ndiyeno mayi wina wanzeru wamumzindawo anafuula kuti: “Tamverani amuna inu, tamverani! Chonde tamuuzeni Yowabu abwere pafupipa kuti ndilankhule naye.” 17  Choncho Yowabu anayandikira ndipo mayiyo anati: “Kodi ndinu a Yowabu?” Yowabu anayankha kuti: “Inde, ndine.” Ndiyeno mayiyo anati: “Tamverani zimene ine kapolo wanu ndikufuna kukuuzani.” Yowabu anayankha kuti: “Ndikumvetsera.” 18  Ndiyeno mayiyo anati: “Kale anthu ankanena kuti, ‘Ngati anthu akufuna kuti nkhani yawo ithe, akafunsire nzeru kumzinda wa Abele.’ 19  Ine ndikuimira anthu okonda mtendere ndi okhulupirika a mu Isiraeli. Inu mukufuna kupha mzinda umene uli ngati mayi mu Isiraeli. Nʼchifukwa chiyani mukufuna kuwononga cholowa cha Yehova?”+ 20  Yowabu anayankha kuti: “Ine sindingawononge mzindawu, nʼzosatheka zimenezo. 21  Nkhani siili choncho. Koma munthu wochokera kudera lamapiri la Efuraimu,+ dzina lake Sheba+ mwana wa Bikiri, waukira Mfumu Davide. Inu mukangotipatsa munthu ameneyu, ine ndiusiya mzindawu.” Mayiyo anauza Yowabu kuti: “Tikuponyerani mutu wake kuchokera pamwamba pa mpanda!” 22  Nthawi yomweyo, mayi wanzeruyo anapita nʼkukalankhula ndi anthu onse, ndipo anthuwo anadula mutu wa Sheba mwana wa Bikiri nʼkuuponya kwa Yowabu. Zitatero, Yowabu analiza lipenga la nyanga ya nkhosa ndipo anthu onse anachoka kumzindawo nʼkupita kwawo.+ Yowabu nayenso anabwerera ku Yerusalemu kwa mfumu. 23  Yowabu anali mtsogoleri wa gulu lonse lankhondo la Isiraeli+ ndipo Benaya+ mwana wa Yehoyada+ ankatsogolera Akereti ndi Apeleti.+ 24  Adoramu+ ankatsogolera anthu olembedwa ntchito yokakamiza ndipo Yehosafati+ mwana wa Ahiludi ankalemba zimene zachitika. 25  Seva anali mlembi ndipo Zadoki+ ndi Abiyatara+ anali ansembe. 26  Ira mbadwa ya Yairi anakhala nduna yaikulu* ya Davide.

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “kutenti.”
Kapena kuti, “kunyumba yake yachifumu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Iwo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wansembe.”