2 Samueli 21:1-22

  • Agibiyoni anabwezera anthu a mʼbanja la Sauli (1-14)

  • Nkhondo yolimbana ndi Afilisiti (15-22)

21  Ndiyeno mʼmasiku a Davide kunagwa njala+ kwa zaka zitatu zotsatizana. Choncho Davide anafunsa Yehova ndipo Yehova anamuuza kuti: “Sauli ndi anthu amʼnyumba yake ali ndi mlandu wa magazi chifukwa Sauli anapha Agibiyoni.”+  Choncho mfumu inaitana Agibiyoni+ ndi kulankhula nawo. (Agibiyoni sanali Aisiraeli koma Aamori+ omwe anatsala. Aisiraeli analumbirira Agibiyoni kuti sawapha,+ koma Sauli ankafuna kuwapha onse chifukwa cha mtima wofunitsitsa kuthandiza Aisiraeli ndi Ayuda.)  Davide anafunsa Agibiyoni kuti: “Ndikuchitireni chiyani ndipo ndipereke chiyani kuti ndiphimbe tchimo limeneli, kuti inu mudalitse cholowa cha Yehova?”  Agibiyoni anayankha kuti: “Sitikufuna siliva kapena golide+ pa nkhani ya Sauli ndi anthu amʼnyumba yake, komanso sitingaphe munthu aliyense mu Isiraeli.” Ndiyeno Davide anati: “Chilichonse chimene mungafune ndikuchitirani.”  Iwo anauza mfumu kuti: “Tikufuna kuti munthu amene anapha anthu a mtundu wathu ndiponso kutikonzera chiwembu choti tisapezekenso mʼmadera onse a Isiraeli,+  mutipatse ana ake aamuna 7. Tipachika* mitembo yawo+ kuti Yehova aione.+ Tiipachika ku Gibeya, kwawo kwa Sauli, munthu amene Yehova anamusankha.”+ Ndiyeno mfumu inati: “Ndikupatsani.”  Koma mfumu inamvera chisoni Mefiboseti+ mwana wamwamuna wa Yonatani, mwana wa Sauli, chifukwa cha lumbiro limene Davideyo ndi Yonatani+ mwana wa Sauli anapanga pamaso pa Yehova.  Choncho mfumu inatenga Arimoni ndi Mefiboseti, amene anali ana awiri aamuna a Rizipa,+ mwana wamkazi wa Aya, amene Rizipayo anaberekera Sauli. Anatenganso ana aamuna 5 a Mikala,*+ mwana wamkazi wa Sauli, amene anaberekera Adiriyeli,+ mwana wa Barizilai wa ku Mehola.*  Iye anawapereka kwa Agibiyoni ndipo Agibiyoniwo anapachika mitembo yawo paphiri kuti Yehova+ aone moti onse 7 anafera limodzi. Iwo anaphedwa mʼmasiku oyambirira a nthawi yokolola, kumayambiriro kwa nthawi yokolola balere. 10  Kenako Rizipa+ mwana wamkazi wa Aya anatenga chiguduli nʼkuchiyala pamwala kuti azikhalapo, kuyambira kumayambiriro kwa nthawi yokolola mpaka pamene mvula inagwera pamitemboyo. Iye sanalole mbalame zamumlengalenga kutera pamitemboyo masana, ndipo usiku sanalole zilombo zakutchire kuyandikirapo. 11  Davide anauzidwa zimene Rizipa mwana wa Aya, mkazi wamngʼono* wa Sauli anachita. 12  Choncho Davide anapita kukatenga mafupa a Sauli ndi mafupa a Yonatani mwana wake kwa atsogoleri* a ku Yabesi-giliyadi.+ Atsogoleriwo anakatenga mobisa mtembo wa Sauli ndi wa Yonatani mʼbwalo la mzinda wa Beti-sani, kumene Afilisiti anaipachika, tsiku limene anapha Sauli paphiri la Giliboa.+ 13  Iye anabweretsa mafupa a Sauli ndi a mwana wake Yonatani. Atatero anasonkhanitsanso mafupa a anthu amene anaphedwa* aja.+ 14  Kenako anthu anaika mafupa a Sauli ndi a mwana wake Yonatani mʼdera la Benjamini ku Zela+ mʼmanda a Kisi+ bambo ake. Atachita zonse zimene mfumu inalamula, Mulungu anamvetsera madandaulo awo okhudza dzikolo.+ 15  Ndiyeno panayambikanso nkhondo pakati pa Afilisiti ndi Aisiraeli.+ Choncho Davide ndi atumiki ake anapita kukamenyana ndi Afilisiti, koma Davide anatopa kwambiri. 16  Zitatero, Isibi-benobi, mbadwa ya Arefai+ amene anali ndi mkondo wakopa wolemera makilogalamu pafupifupi atatu ndi hafu*+ komanso lupanga latsopano, ankafuna kupha Davide. 17  Nthawi yomweyo Abisai+ mwana wa Zeruya anathandiza+ Davide ndipo anapha Mfilisitiyo. Zitatero asilikali a Davide anamulumbirira kuti: “Musamapitenso ndi ife kunkhondo.+ Musazimitse nyale ya Isiraeli.”+ 18  Nkhondo imeneyi itatha, panayambikanso nkhondo ina yomenyana ndi Afilisiti+ ku Gobu. Pa nthawi imeneyo Sibekai+ wa ku Husa* anapha Safi, mbadwa ya Arefai.+ 19  Kenako panayambikanso nkhondo ina ndi Afilisiti+ ku Gobu, ndipo Elihanani mwana wa Yaare-oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliyati wa ku Gati, amene mtengo wa mkondo wake unali waukulu ngati mtengo wogwiritsa ntchito powomba nsalu.+ 20  Kenako panayambikanso nkhondo ina ku Gati ndipo kunali munthu wamkulu modabwitsa. Iye anali ndi zala 6 kudzanja lililonse ndiponso zala 6 kuphazi lililonse, moti anali ndi zala 24. Nayenso anali mbadwa ya Arefai.+ 21  Iye ankanyoza kwambiri Aisiraeli.+ Choncho Yonatani mwana wa Simeyi,+ mchimwene wake wa Davide, anamupha. 22  Anthu 4 amenewa anali mbadwa za Arefai ku Gati ndipo anaphedwa ndi Davide ndi atumiki ake.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Tionetsa,” kutanthauza atawathyola manja ndi miyendo.
Mabaibulo ena amati, “Merabu.”
Nʼkutheka kuti kunali ku Abele-mehola.
Kapena kuti, “mdzakazi.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mabaibulo ena amati, “nzika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anaonetsedwa.”
Kapena kuti, “wolemera masekeli 300.” Onani Zakumapeto B14.
Mabaibulo ena amati, “Sibekai mbadwa ya Husa.”