2 Samueli 22:1-51

  • Davide anatamanda Mulungu chifukwa chowapulumutsa (1-51)

    • “Yehova ndi thanthwe langa” (2)

    • Yehova amakhala wokhulupirika kwa okhulupirika (26)

22  Davide analankhula ndi Yehova mawu a nyimbo iyi,+ pa tsiku limene Yehova anamupulumutsa kwa adani ake onse+ ndiponso mʼmanja mwa Sauli.+  Iye anati: “Yehova ndi thanthwe langa, malo anga achitetezo+ ndiponso Wondipulumutsa.+   Mulungu wanga ndi thanthwe langa,+ ine ndimathawira kwa iye,Iye ndi chishango changa,+ nyanga* yanga ya chipulumutso* ndi malo anga achitetezo.*+Komanso ndi malo anga othawirako,+ mpulumutsi wanga+ amene amandipulumutsa kwa anthu achiwawa.   Ndimapempha Yehova, amene ndi woyenera kutamandidwa, kuti andithandize.Ndipo adzandipulumutsa kwa adani anga.   Mafunde a imfa anandizungulira;+Gulu la anthu opanda pake linkandiopseza.+   Zingwe za Manda* zinandizungulira;+Ndinatcheredwa misampha ya imfa.+   Pa nthawi ya mavuto, ndinaitana Yehova,+Ndinapitiriza kuitana Mulungu wanga. Iye anamva mawu anga ali mʼkachisi wake,Makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+   Dziko lapansi linayamba kugwedezeka ndiponso kunjenjemera;+Maziko akumwamba anagwedezeka.+Anagwedezeka chifukwa Mulungu anakwiya.+   Utsi unatuluka mʼmphuno mwake,Ndipo moto wowononga unatuluka mʼkamwa mwake;+Makala oyaka anatuluka mwa iye. 10  Iye anaweramitsa kumwamba pamene ankatsika,+Mdima wandiweyani unali pansi pa mapazi ake.+ 11  Iye anakwera pakerubi+ ndipo anabwera akuuluka. Anaonekera pamapiko a mngelo.*+ 12  Kenako anaika mdima momuzungulira ngati tenti,+Mʼmadzi akuda ndi mʼmitambo yakuda. 13  Mʼkuwala kochokera pamaso pake munatuluka makala oyaka moto. 14  Kenako Yehova ali kumwamba anayamba kugunda ngati mabingu;+Wamʼmwambamwamba anachititsa kuti mawu ake amveke.+ 15  Anaponya mivi yake+ ndipo anawabalalitsa;Anaponya mphezi ndipo anawasokoneza.+ 16  Pansi pa nyanja panaonekera;+Maziko a dziko lapansi anaonekera chifukwa cha kudzudzula kwa Yehova,Chifukwa cha mphamvu ya mpweya wotuluka mʼmphuno mwake.+ 17  Anatambasula dzanja lake kuchokera kumwamba;Anandigwira nʼkundivuula mʼmadzi akuya.+ 18  Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,+Kwa anthu odana nane amene anali amphamvu kuposa ine. 19  Adaniwo anandiukira pa tsiku la tsoka,+Koma Yehova anandithandiza. 20  Ananditenga nʼkundiika pamalo otetezeka;*+Anandipulumutsa chifukwa ankasangalala nane.+ 21  Yehova amandidalitsa mogwirizana ndi chilungamo changa;+Amandipatsa mphoto mogwirizana ndi manja anga osalakwa.*+ 22  Chifukwa ndasunga njira za Yehova,Ndipo sindinachite chinthu choipa kwambiri, chomwe ndi kusiya Mulungu wanga. 23  Ndimakumbukira ziweruzo zake zonse;+Ndipo sindidzasiya kutsatira malamulo ake.+ 24  Ndidzakhalabe wosalakwa+ pamaso pake,Ndipo ndidzayesetsa kupewa cholakwa.+ 25  Yehova andipatse mphoto mogwirizana ndi chilungamo changa,+Komanso chifukwa choti ndine wosalakwa pamaso pake.+ 26  Munthu wokhulupirika, mumamuchitira mokhulupirika.+Munthu wamphamvu komanso wosalakwa, mumamuchitira mwachilungamo.+ 27  Munthu woyera, mumamusonyeza kuti ndinu woyera,+Koma munthu wamaganizo opotoka mumamusonyeza kuti ndinu wochenjera.+ 28  Mumapulumutsa anthu odzichepetsa,+Koma mumanyansidwa ndi anthu odzikweza ndipo mumawatsitsa.+ 29  Inu Yehova ndinu nyale yanga;+Yehova ndi amene amandiunikira mumdima.+ 30  Ndi thandizo lanu ndingalimbane ndi gulu la achifwamba;Ndi mphamvu za Mulungu ndingakwere khoma.+ 31  Njira ya Mulungu woona ndi yangwiro.+Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino.+ Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+ 32  Kodi pali Mulungu winanso woposa Yehova?+ Nanga pali thanthwe linanso kupatula Mulungu wathu?+ 33  Mulungu woona ndi malo anga otetezeka kwambiri,+Ndipo iye adzasalaza njira yanga.+ 34  Amachititsa kuti mapazi anga akhale ngati a mbawala;Amachititsa kuti ndiime pamalo okwera.+ 35  Iye amaphunzitsa manja anga kumenya nkhondo;Manja anga angathe kukunga uta wakopa.* 36  Mumandipatsa chishango chanu chachipulumutso,Ndipo kudzichepetsa kwanu kumandikweza.+ 37  Mumakulitsa njira kuti mapazi anga azidutsamo,Ndipo mapazi anga sadzaterereka.+ 38  Ndidzathamangitsa adani anga nʼkuwapha onse;Ndipo sindidzabwerera mpaka nditawafafaniza. 39  Ndidzawafafaniza ndi kuwaphwanya kuti asadzukenso.+Iwo adzagwera pansi pa mapazi anga. 40  Mudzandipatsa mphamvu kuti ndithe kumenya nkhondo;+Mudzachititsa kuti adani anga agonje.+ 41  Mudzachititsa kuti adani anga athawe pamaso panga;+Ndidzapha* anthu amene amadana nane.+ 42  Amafuula kuti athandizidwe, koma palibe angawapulumutse;Amafika pofuulira Yehova, koma iye samawayankha.+ 43  Ndidzawapera ndipo adzakhala ngati fumbi.Ndidzawapondaponda ngati matope amumsewu. 44  Inu mudzandipulumutsa kwa anthu a mtundu wanga ondipezera zifukwa.+ Mudzanditeteza kuti ndikhale mtsogoleri wa mitundu ya anthu.+Anthu amene sindikuwadziwa adzanditumikira.+ 45  Anthu ochokera mʼdziko lina adzandiweramira mwamantha;+Zimene adzamve zokhudza ine zidzachititsa kuti azindimvera. 46  Anthu ochokera mʼdziko lina adzachita mantha;Iwo adzatuluka mʼmalo awo otetezeka akunjenjemera. 47  Yehova ndi wamoyo! Litamandike Thanthwe langa!+ Mulungu wanga, yemwe ndi thanthwe limene limandipulumutsa, alemekezeke.+ 48  Mulungu woona amabwezera adani anga;+Iye amachititsa kuti mitundu ya anthu izindigonjera;+ 49  Iye amandipulumutsa kwa adani anga. Mumandikweza pamwamba+ pa anthu ondiukira;Mumandipulumutsa kwa munthu wachiwawa.+ 50  Nʼchifukwa chake ndidzakuyamikani inu Yehova pakati pa mitundu ya anthu.+Ndipo ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.+ 51  Iye amachita zazikulu kuti apulumutse mfumu yake;+Amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa wodzozedwa wake,Kwa Davide ndi mbadwa* zake mpaka kalekale.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mpulumutsi wanga wamphamvu.”
Kapena kuti, “malo anga okwezeka achitetezo.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti “pamapiko a mphepo.”
Kapena kuti, “otakasuka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “oyera.”
Kapena kuti, “wamkuwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndidzakhalitsa chete.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”