2 Samueli 24:1-25

  • Davide anachimwa powerenga anthu (1-14)

  • Mliri unapha anthu 70,000 (15-17)

  • Davide anamanga guwa (18-25)

    • Sanapereke nsembe popanda kulipira (24)

24  Yehova anakwiyiranso kwambiri Aisiraeli+ pamene winawake anaukira Aisiraeli nʼkuuza Davide kuti: “Pitani mukawerenge+ anthu a Isiraeli ndi Yuda.”+  Choncho mfumu inauza Yowabu+ mkulu wa magulu ankhondo amene anali naye kuti: “Upite mʼmafuko onse a Isiraeli kuyambira ku Dani mpaka ku Beere-seba+ ndipo ukawerenge anthu kuti ndidziwe chiwerengero chawo.”  Koma Yowabu anauza mfumu kuti: “Yehova Mulungu wanu awonjezere anthu kuwirikiza ka 100 ndipo inu mbuyanga mfumu muone zimenezi zikuchitika. Koma nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchita zimenezi mbuyanga mfumu?”  Koma mfumu inakana kumvera zimene Yowabu ndi atsogoleri a asilikali ananena. Choncho Yowabu ndi atsogoleri a asilikaliwo anapita kukawerenga Aisiraeli.+  Anawoloka Yorodano nʼkukamanga msasa ku Aroweli,+ kumanja* kwa mzinda umene unali pakati pa chigwa.* Atatero anapita kufupi ndi dera la fuko la Gadi ndipo kenako anapita ku Yazeri.+  Atachoka kumeneko anafika ku Giliyadi+ ndi ku Tatimu-hodisi, ndipo anapitirira mpaka ku Dani-jaana nʼkuzungulira kukafika ku Sidoni.+  Atachoka kumeneko anafika mumzinda wa mpanda wolimba wa Turo+ ndiponso mʼmizinda yonse ya Ahivi+ ndi Akanani.+ Kenako anafika ku Beere-seba+ ku Negebu, mʼdziko la Yuda.  Choncho anazungulira mʼdziko lonse ndipo anabwerera ku Yerusalemu patatha miyezi 9 ndi masiku 20.  Yowabu anapereka kwa mfumu chiwerengero cha anthu onse. Aisiraeli anali ndi asilikali 800,000 amphamvu okhala ndi lupanga, ndipo Ayuda anali ndi asilikali 500,000.+ 10  Koma Davide atawerenga anthuwo, anayamba kuvutika mumtima mwake.*+ Choncho Davide anauza Yehova kuti: “Ndachimwa+ kwambiri pochita zimenezi. Chonde Yehova, ndikhululukireni tchimo langa ine mtumiki wanu,+ chifukwa ndachita zopusa kwambiri.”+ 11  Davide atadzuka mʼmawa, Yehova anauza mneneri Gadi,+ wamasomphenya wa Davide, kuti: 12  “Pita, ukamuuze Davide kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Pali zilango zitatu zimene ndingakupatse ndipo iwe usankhepo chimodzi.”’”+ 13  Choncho Gadi anapita kwa Davide nʼkumuuza kuti: “Kodi mʼdziko lanu mugwe njala zaka 7?+ Kapena muzithawa adani anu kwa miyezi itatu?+ Kapena mʼdziko lanu mugwe mliri masiku atatu?+ Ganizirani mofatsa zoti ndikayankhe kwa amene wandituma.” 14  Davide atamva zimenezo, anauza Gadi kuti: “Zimenezi zikundisowetsa mtendere kwambiri. Kuli bwino ndilangidwe ndi Yehova,+ chifukwa chifundo chake nʼchachikulu,+ koma ndisalangidwe ndi munthu.”+ 15  Kenako Yehova anagwetsa mliri+ mu Isiraeli kuyambira mʼmawa mpaka nthawi yomwe anakonza, moti anthu 70,000 anafa,+ kuyambira ku Dani mpaka ku Beere-seba.+ 16  Mngelo atatambasula dzanja lake kuti awononge Yerusalemu, Yehova anamva chisoni chifukwa cha mliriwo,+ choncho anauza mngelo amene ankapha anthuyo kuti: “Basi! Bweza dzanja lako.” Pa nthawiyi, mngelo wa Yehovayo anali pafupi ndi malo opunthira mbewu a Arauna+ wa Chiyebusi.+ 17  Davide ataona mngelo amene ankapha anthuyo anauza Yehova kuti: “Ine ndi amene ndachimwa, ndipo ine ndi amene ndalakwitsa, nanga nkhosazi+ zalakwa chiyani? Bwanji mulange ineyo ndi anthu amʼnyumba ya bambo anga?”+ 18  Kenako Gadi anapita kwa Davide tsiku lomwelo nʼkukamuuza kuti: “Pitani mukamangire Yehova guwa lansembe pamalo opunthira mbewu a Arauna wa Chiyebusi.”+ 19  Choncho Davide anapitadi mogwirizana ndi mawu a Gadi komanso mogwirizana ndi zimene Yehova analamula. 20  Arauna atasuzumira panja anaona mfumu ndi atumiki ake akubwera. Nthawi yomweyo Arauna anatuluka nʼkugwada pamaso pa mfumu ndipo anawerama mpaka nkhope yake kufika pansi. 21  Arauna anafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani inu mbuyanga mfumu mwabwera kwa ine mtumiki wanu?” Davide anayankha kuti: “Ndabwera kudzagula malo ako opunthira mbewu. Ndikufuna kumangira Yehova guwa lansembe, kuti mliri umene uli pakati pa anthuwu uthe.”+ 22  Koma Arauna anauza Davide kuti: “Mbuyanga mfumu, tengani malowo ndipo mupereke chilichonse chimene mukuona kuti nʼchabwino. Ngʼombe iyi ikhale nsembe yopsereza ndipo chopunthira ndi zipangizo zinazi zikhale nkhuni. 23  Ine Arauna ndikukupatsani zonsezi mfumu.” Kenako Arauna anauza mfumu kuti: “Yehova Mulungu wanu asonyeze kuti akusangalala nanu.” 24  Koma mfumu inauza Arauna kuti: “Ayi, ndikuyenera kugula zimenezi. Sindingapereke nsembe zopsereza kwa Yehova Mulungu wanga popanda kulipira chilichonse.” Choncho Davide anagula malo opunthira mbewu ndi ngʼombe ndipo analipira ndalama zokwana masekeli* 50 asiliva.+ 25  Zitatero, Davide anamangira Yehova guwa lansembe+ pamalowo ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamgwirizano. Choncho Yehova anamva kuchonderera kwawo,+ moti mliri umene unagwa mu Isiraeliwo, unatha.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kumʼmwera.”
Kapena kuti, “chikumbumtima chake chinayamba kumuvutitsa.”
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.