2 Samueli 3:1-39

  • Davide anakhala wamphamvu (1)

  • Ana a Davide (2-5)

  • Abineri anakhala mbali ya Davide (6-21)

  • Yowabu anapha Abineri (22-30)

  • Davide analira maliro a Abineri (31-39)

3  Nkhondo ya pakati pa anthu a nyumba ya Sauli ndi a nyumba ya Davide inapitirirabe. Davide anapitiriza kukhala wamphamvu+ koma anthu a nyumba ya Sauli ankachepa mphamvu.+  Pa nthawiyi, Davide anabereka ana aamuna ku Heburoni.+ Mwana wake woyamba anali Aminoni+ ndipo mayi ake anali Ahinowamu+ wa ku Yezereeli.  Mwana wake wachiwiri anali Kileyabu ndipo mayi ake anali Abigayeli+ yemwe anali mkazi wa Nabala wa ku Karimeli. Wachitatu anali Abisalomu+ ndipo mayi ake anali Maaka, mwana wa Talimai+ mfumu ya ku Gesuri.  Wa 4 anali Adoniya+ ndipo mayi ake anali Hagiti. Wa 5 anali Sefatiya yemwe mayi ake anali Abitali.  Wa 6 anali Itireamu ndipo mayi ake anali Egila, mkazi wa Davide. Amenewa ndi ana amene Davide anabereka ali ku Heburoni.  Pamene nkhondo ya pakati pa anthu a nyumba ya Sauli ndi a nyumba ya Davide inkapitirira, Abineri+ anaonetsetsa kuti akupitiriza kukhala ndi mphamvu mʼnyumba ya Sauli.  Sauli anali ndi mkazi wamngʼono, dzina lake Rizipa,+ mwana wa Aya. Patapita nthawi, Isi-boseti+ anafunsa Abineri kuti: “Nʼchifukwa chiyani unagona ndi mkazi wamngʼono wa bambo anga?”+  Abineri atamva mawu a Isi-bosetiwa anakwiya kwambiri ndipo anati: “Kodi ndine galu wopanda pake wa Yuda? Ineyo ndakhala ndikusonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu a nyumba ya Sauli bambo ako, azichimwene ake komanso anzake ndipo sindinakupereke mʼmanja mwa Davide. Koma lero ukundiimba mlandu pa zimene ndinalakwitsa zokhudza mkazi.  Mulungu alange ine Abineri mowirikiza ngati sindidzachitira Davide mogwirizana ndi zimene Yehova analumbira kwa iye,+ 10  kusamutsa ufumu kuuchotsa mʼnyumba ya Sauli nʼkukhazikitsa mpando wachifumu wa Davide mu Isiraeli ndi mu Yuda, kuchokera ku Dani mpaka ku Beere-seba.”+ 11  Isi-boseti sanayankhe chilichonse pa zimene Abineri ananena chifukwa ankamuopa.+ 12  Nthawi yomweyo, Abineri anatumiza anthu kwa Davide kukamuuza kuti: “Kodi dzikoli ndi la ndani?” Anawonjezera kuti: “Chitani nane pangano, ndipo ineyo ndidzayesetsa kuti Aisiraeli onse akhale kumbali yanu.”+ 13  Davide anayankha kuti: “Chabwino! Ndichitadi nawe pangano. Koma ndikukupempha chinthu chimodzi: Usadzabwere kuno kudzaonana nane pokhapokha udzabwere ndi Mikala,+ mwana wamkazi wa Sauli.” 14  Kenako Davide anatumiza uthenga kwa Isi-boseti+ mwana wa Sauli wakuti: “Ndipatse mkazi wanga Mikala, amene ndinamuperekera malowolo a makungu okwana 100 a Afilisiti, amene amachotsa pochita mdulidwe.”+ 15  Choncho Isi-boseti anatuma anthu kuti akatenge Mikala kwa mwamuna wake Palitiyeli,*+ mwana wa Laisi. 16  Koma mwamuna wake ankamutsatira, kwinaku akulira mpaka kukafika ku Bahurimu.+ Kenako Abineri anamuuza kuti: “Bwerera!” Atatero anabwerera. 17  Pa nthawiyi, Abineri anatumiza uthenga kwa akulu a Isiraeli wakuti: “Paja mwakhala mukufuna kuti Davide akhale mfumu yanu. 18  Ndiye dziwani zochita chifukwa Yehova anauza Davide kuti:+ ‘Ndidzapulumutsa anthu anga Aisiraeli kwa Afilisiti ndiponso kwa adani awo onse pogwiritsa ntchito dzanja la Davide mtumiki wanga.’” 19  Kenako Abineri analankhula ndi anthu a fuko la Benjamini.+ Anapitanso kukalankhula ndi Davide pa awiri ku Heburoni ndipo anamuuza zimene Aisiraeli komanso anthu onse a nyumba ya Benjamini anagwirizana. 20  Abineri atafika kwa Davide ku Heburoni pamodzi ndi amuna 20, Davide anawakonzera phwando. 21  Kenako Abineri anauza Davide kuti: “Ine ndimati ndinyamuke ndikasonkhanitse Aisiraeli onse kuti akhale mbali ya mbuyanga mfumu, kuti achite nanu pangano ndipo mudzakhala mfumu ya anthu onse amene mumafuna kuwalamulira.” Choncho Davide analola Abineri kuti apite mwamtendere. 22  Pasanapite nthawi, Yowabu ndi atumiki a Davide anafika kuchokera kunkhondo, atatengako zinthu zambiri. Pa nthawiyi Abineri sanali ndi Davide ku Heburoni chifukwa anali atamulola kupita mwamtendere. 23  Yowabu+ atafika pamodzi ndi gulu lonse lankhondo lomwe anali nalo, anthu anamuuza kuti: “Abineri+ mwana wa Nera+ anabwera kwa mfumu, ndipo mfumu yamulola kupita mwamtendere.” 24  Zitatero Yowabu anapita kwa mfumu nʼkunena kuti: “Nʼchiyani mwachitachi? Abineri anabwera kwa inu. Ndiye zoona mungamusiye kuti azipita mwamtendere? 25  Kodi Abineri mwana wa Nera simukumudziwa? Iye anabwera kuno kudzakupusitsani kuti adziwe zonse zokhudza inuyo ndiponso chilichonse chimene mukuchita.” 26  Ndiyeno Yowabu anachoka nʼkumusiya Davide ndipo anatuma anthu kuti akamubweze Abineri. Anthuwo anamupeza Abineri pachitsime cha Sira, koma Davide sanadziwe chilichonse. 27  Abineri atabwerera ku Heburoni,+ Yowabu anamʼtengera pambali kugeti kuti alankhulane naye pa awiri. Koma kumeneko anamubaya pamimba moti anafa.+ Anamupha chifukwa choti anapha Asaheli, mchimwene wake wa Yowabuyo.+ 28  Davide atamva zimenezi, ananena kuti: “Yehova akudziwa kuti ineyo ndi ufumu wanga tilibe mlandu wa magazi+ a Abineri mwana wa Nera mpaka kalekale. 29  Mlandu umenewu ubwerere pamutu pa Yowabu+ ndi anthu onse a nyumba ya bambo ake. Mʼnyumba ya Yowabu musadzasowe mwamuna wa nthenda yakukha kumaliseche,+ wakhate,+ wogwira ntchito yowomba nsalu,* wophedwa ndi lupanga kapena wosowa chakudya!”+ 30  Choncho Yowabu ndi mchimwene wake Abisai+ anapha Abineri+ chifukwa chakuti iye anapha Asaheli mchimwene wawo pa nkhondo+ ku Gibiyoni. 31  Kenako Davide anauza Yowabu ndi anthu onse amene anali naye kuti: “Ngʼambani zovala zanu nʼkuvala ziguduli ndipo mumulire Abineri.” Mfumu Davide ankayenda pambuyo pa chithatha cha maliro a Abineri. 32  Abineri anaikidwa mʼmanda ku Heburoni. Kumandako, mfumu inayamba kulira mokweza ndipo anthu onse anayambanso kulira. 33  Mfumuyo inayamba kuimba nyimbo yolira Abineri kuti: “Zoona Abineri afe ngati munthu wopanda nzeru? 34  Manja ako anali osamangidwa,Ndipo mapazi ako sanaikidwe mʼmatangadza a kopa. Wafa ngati waphedwa ndi zigawenga.”*+ Zitatero anthu onse analiranso. 35  Kenako anthu onse anabwera kwa Davide tsiku lomwelo masana kudzamʼpatsa chakudya kuti amutonthoze. Koma Davide analumbira kuti: “Mulungu andilange mowirikiza ngati ndingadye chakudya chilichonse dzuwa lisanalowe!”+ 36  Anthu onse anaona zimene mfumu inkachitazi, ndipo anaona kuti zili bwino. Ankaona kuti zili bwino mofanana ndi zina zonse zimene mfumuyo inkachita. 37  Anthu onse komanso Aisiraeli onse anadziwa tsiku limenelo kuti mfumu inalibe mlandu pa imfa ya Abineri mwana wa Nera.+ 38  Kenako mfumu inauza atumiki ake kuti: “Kodi simukudziwa kuti amene wafa leroyu ndi kalonga komanso munthu wamphamvu mu Isiraeli?+ 39  Ine lero ndafooka ngakhale kuti ndinadzozedwa kukhala mfumu.+ Ndikuona kuti amuna awa, ana a Zeruya,+ achita nkhanza kwambiri.+ Yehova abwezere munthu aliyense wochita zoipa mogwirizana ndi kuipa kwake.”+

Mawu a M'munsi

Pa 1Sa 25:44 akutchedwa Paliti.
Mwina akunena za mwamuna wolumala wogwira ntchito za azimayi.
Kapena kuti, “anthu osalungama.”