2 Samueli 4:1-12

  • Isi-boseti anaphedwa (1-8)

  • Davide anapha anthu amene anapha Isi-boseti (9-12)

4  Isi-boseti,+ mwana wa Sauli, atamva kuti Abineri wafa ku Heburoni,+ anatheratu mphamvu* ndipo Aisiraeli onse anasokonezeka.  Panali amuna awiri, omwe anali atsogoleri a magulu a achifwamba a mwana wa Sauli. Wina dzina lake anali Bana ndipo wina anali Rekabu. Onsewa anali ana a Rimoni wa ku Beeroti wa fuko la Benjamini. (Chifukwa dera la Beeroti+ linkaonedwanso kuti ndi gawo la fuko la Benjamini.  Anthu a ku Beeroti anathawira ku Gitaimu,+ ndipo akhala kumeneko ngati alendo mpaka lero.)  Yonatani mwana wa Sauli+ anali ndi mwana wamwamuna wolumala mapazi.+ Mwanayu anali ndi zaka 5 pamene kunabwera uthenga wochokera ku Yezereeli+ wakuti Sauli ndi Yonatani afa. Uthengawu utafika, mayi amene ankamusamalira anamunyamula nʼkuyamba kuthawa. Pamene ankathawa mwamantha, mayiyo anagwetsa mwanayo ndipo analumala. Mwanayo dzina lake linali Mefiboseti.+  Rekabu ndi Bana, ana aamuna a Rimoni wa ku Beeroti, anapita kunyumba ya Isi-boseti masana kukutentha, ndipo anamupeza atagona kuti apumule.  Iwo analowa mʼnyumbamo ngati akufuna kukatenga tirigu, kenako anabaya Isi-boseti pamimba. Atatero, Rekabu ndi mchimwene wake Bana+ anathawa.  Iwo atalowa mʼnyumbamo, anapeza Isi-boseti atagona pabedi kuchipinda kwake ndipo anamubaya nʼkumupha. Kenako anamudula mutu nʼkuutenga ndipo anayenda usiku wonse mumsewu wopita ku Araba.  Mutu wa Isi-bosetiwo+ anafika nawo kwa Davide ku Heburoni ndipo anauza mfumuyo kuti: “Takubweretserani mutu wa Isi-boseti mwana wa mdani wanu Sauli,+ amene ankafunafuna moyo wanu.+ Lero Yehova wabwezera Sauli ndi mbadwa zake pa zimene anakuchitirani inu mbuyanga mfumu.”  Koma Davide anayankha Rekabu ndi mchimwene wake Bana, ana a Rimoni wa ku Beeroti kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, amene anandipulumutsa mʼmasautso anga onse,+ 10  munthu wina atandibweretsera uthenga wakuti, ‘Sauli wafa,’+ poganiza kuti wabweretsa uthenga wabwino, ine ndinamugwira nʼkumupha+ ku Zikilaga. Malipiro a uthenga umene anabweretsa anali amenewo. 11  Ndiye kuli bwanji pamene anthu oipa apha munthu wolungama pabedi mʼnyumba yake? Kodi sindiyenera kufuna magazi ake mʼmanja mwanu+ ndiponso kukuchotsani padzikoli?” 12  Pamenepo Davide analamula anyamata ake kuti aphe Rekabu ndi Bana.+ Kenako anawadula manja ndi mapazi nʼkuwapachika+ pafupi ndi dziwe la ku Heburoni. Koma anatenga mutu wa Isi-boseti nʼkuuika mʼmanda a Abineri ku Heburoni.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “manja ake analefuka.”