2 Samueli 5:1-25

  • Davide anakhala mfumu ya Aisiraeli onse (1-5)

  • Yerusalemu analandidwa (6-16)

    • Ziyoni, Mzinda wa Davide (7)

  • Davide anagonjetsa Afilisiti (17-25)

5  Patapita nthawi, mafuko onse a Isiraeli anapita kwa Davide ku Heburoni+ nʼkumuuza kuti: “Ife ndi inu ndife magazi amodzi.*+  Kale, pamene Sauli anali mfumu yathu, inuyo ndi amene munkatsogolera Aisiraeli kunkhondo.*+ Ndipo Yehova anakuuzani kuti, ‘Udzaweta anthu anga Aisiraeli ndipo udzakhala mtsogoleri wa Aisiraeli.’”+  Choncho akulu onse a Isiraeli anabwera kwa mfumu ku Heburoni ndipo Mfumu Davide inachita nawo pangano+ ku Heburoniko pamaso pa Yehova. Kenako iwo anadzoza Davide kuti akhale mfumu ya Isiraeli.+  Davide anakhala mfumu ali ndi zaka 30 ndipo analamulira kwa zaka 40.+  Ku Heburoni anakhala mfumu ya Yuda kwa zaka 7 ndi miyezi 6. Ku Yerusalemu+ analamulira Isiraeli yense ndi Yuda kwa zaka 33.  Ndiyeno mfumu ndi anthu ake anapita ku Yerusalemu kukamenyana ndi Ayebusi+ amene ankakhala kumeneko. Ayebusi anayamba kunyoza Davide kuti: “Sudzalowa mumzinda uno, chifukwa ngakhale anthu osaona ndi olumala adzakuthamangitsa.” Iwo ankaganiza kuti: ‘Davide sadzalowa mumzinda muno.’+  Koma Davide analanda malo amene anali mumpanda wolimba kwambiri mu Ziyoni, umene panopa ndi Mzinda wa Davide.+  Tsiku limenelo, Davide ananena kuti: “Aliyense wokaukira Ayebusi adutse mʼngalande zamadzi nʼkukapha ‘anthu olumala ndi osaona,’ anthu amene ine Davide ndimadana nawo!” Nʼchifukwa chake pali mawu akuti: “Wosaona ndi wolumala sadzalowa mʼnyumba.”  Kenako Davide anayamba kukhala mʼmalo omwe anali mumpanda wolimba kwambiri, ndipo ankadziwika kuti* Mzinda wa Davide. Iye anayamba kumanga malo onsewo kuyambira ku Chimulu cha Dothi*+ mpaka mkati.+ 10  Choncho Davide anapitiriza kukhala wamphamvu+ ndipo Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba anali naye.+ 11  Ndiyeno Hiramu+ mfumu ya Turo anatumiza anthu kwa Davide. Anatumizanso matabwa a mkungudza,+ akalipentala komanso anthu oswa miyala yomangira makoma ndipo anayamba kumanga nyumba* ya Davide.+ 12  Davide anadziwa kuti Yehova wachititsa kuti ufumu wake ukhazikike mu Isiraeli,+ komanso kuti ukhale wamphamvu+ chifukwa cha anthu a Mulungu, Aisiraeli.+ 13  Davide atachoka ku Heburoni nʼkupita ku Yerusalemu anakwatiranso akazi ena komanso anali ndi akazi apambali+ ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.+ 14  Ana amene Davide anabereka ku Yerusalemu ndi awa: Samuwa, Sobabu, Natani,+ Solomo,+ 15  Ibara, Elisua, Nefegi, Yafiya, 16  Elisama, Eliyada ndi Elifeleti. 17  Afilisiti atamva kuti Davide amudzoza kukhala mfumu ya Isiraeli,+ onse anabwera kudzamufunafuna.+ Davide atamva zimenezi, anapita kumalo ovuta kufikako.+ 18  Kenako Afilisitiwo anafika ndipo anamwazikana mʼchigwa cha Arefai.+ 19  Ndiyeno Davide anafunsira kwa Yehova+ kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Afilisitiwa? Kodi muwapereka mʼmanja mwanga?” Yehova anauza Davide kuti: “Pita, Afilisitiwa ndiwapereka ndithu mʼmanja mwako.”+ 20  Choncho Davide anapita ku Baala-perazimu ndipo anapha Afilisiti kumeneko. Atatero anati: “Yehova wayenda patsogolo panga ngati madzi a chigumula nʼkuwononga adani anga.”+ Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Baala-perazimu.*+ 21  Afilisiti anasiya mafano awo kumeneko ndipo Davide ndi anthu ake anawatenga nʼkuwawononga. 22  Patapita nthawi, Afilisiti aja anabweranso nʼkumwazikana mʼchigwa cha Arefai.+ 23  Davide anafunsira kwa Yehova koma anamuyankha kuti: “Usapite kukakumana nawo. Uwazembere kumbuyo nʼkuwaukira kutsogolo kwa zitsamba za baka.* 24  Ukakamva phokoso la kuguba pamwamba pa zitsamba za baka, ukanyamuke mwamsanga, chifukwa Yehova adzakhala atatsogola kukapha asilikali a Afilisiti.” 25  Davide anachitadi zimene Yehova anamulamula, moti anapha Afilisiti+ kuchokera ku Geba+ mpaka kukafika ku Gezeri.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ife ndife fupa lanu ndi mnofu wanu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “polowa ndi potuluka.”
Mabaibulo ena amati, “anawapatsa dzina lakuti.”
Kapena kuti, “Milo.” Amenewa ndi mawu a Chiheberi otanthauza “kudzaza.”
Kapena kuti, “kumanga nyumba yachifumu.”
Kutanthauza, “Ambuye wa Zigumula.”
Dzina lakuti “baka” ndi lochokera ku Chiheberi. Chitsamba chimenechi sichikudziwika kuti chinali chotani.