2 Samueli 6:1-23

  • Likasa analibweretsa ku Yerusalemu (1-23)

    • Uza anagwira Likasa nʼkuphedwa (6-8)

    • Mikala ananyoza Davide (16, 20-23)

6  Davide anasonkhanitsanso asilikali amphamvu mu Isiraeli, okwana 30,000.  Ndiyeno Davide ndi anthu onse amene anali naye ananyamuka nʼkupita ku Baale-yuda kuti akatenge Likasa la Mulungu woona.+ Pa likasa limeneli anthu amaitanirapo dzina la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,+ amene amakhala pamwamba* pa akerubi.+  Koma iwo ananyamulira Likasa la Mulungu woona pangolo yatsopano+ kuti alichotse kunyumba ya Abinadabu+ imene inali paphiri. Uza ndi Ahiyo, ana aamuna a Abinadabu, ndi amene ankatsogolera ngolo yatsopanoyo.  Choncho ananyamula Likasa la Mulungu woona kuchokera kunyumba ya Abinadabu imene inali paphiri ndipo Ahiyo ankayenda patsogolo pa Likasa.  Davide ndi anthu onse a nyumba ya Isiraeli ankasangalala pamaso pa Yehova, akuimba mitundu yonse ya zoimbira za mtengo wofanana ndi mtengo wa mkungudza. Ankaimbanso zeze, zoimbira za zingwe,+ zinganga+ ndi maseche+ osiyanasiyana.  Koma atafika kumalo opunthira mbewu a ku Nakoni, Uza anagwira Likasa la Mulungu woona,+ chifukwa ngʼombe zinatsala pangʼono kuligwetsa.  Zitatero Yehova anakwiyira kwambiri Uza ndipo Mulungu woona anamuphera+ pomwepo chifukwa chochita zinthu mopanda ulemu.+ Moti Uza anafera pompo, pafupi ndi Likasa la Mulungu woona.  Koma Davide anakwiya* chifukwa Yehova anakwiyira kwambiri Uza. Malo amenewa amadziwika ndi dzina lakuti Perezi-uza* mpaka lero.  Choncho Davide anachita mantha kwambiri ndi Yehova+ tsiku limenelo, ndipo anati: “Kodi Likasa la Yehova lidzabwera bwanji kumene ine ndikukhala?”+ 10  Davide sanafunenso kutenga Likasa la Yehova kupita nalo kumene ankakhala, ku Mzinda wa Davide.+ Mʼmalomwake Davide analamula kuti lipite kunyumba ya Obedi-edomu+ wa ku Gati.* 11  Likasa la Yehova linakhala kunyumba ya Obedi-edomu wa ku Gati kwa miyezi itatu, ndipo Yehova ankadalitsa Obedi-edomu ndi banja lake lonse.+ 12  Mfumu Davide inauzidwa kuti: “Yehova wadalitsa nyumba ya Obedi-edomu ndi zinthu zake zonse chifukwa cha Likasa la Mulungu woona.” Choncho Davide anapita kukatenga Likasa la Mulungu woona kunyumba kwa Obedi-edomu nʼkupita nalo ku Mzinda wa Davide, akusangalala.+ 13  Anthu amene ananyamula+ Likasa la Yehova atangoyenda mapazi 6, Davide anapereka nsembe ngʼombe yamphongo ndi chiweto chonenepa. 14  Davide ankavina mozungulira pamaso pa Yehova ndi mphamvu zake zonse. Apa nʼkuti atavala efodi wansalu.+ 15  Davide ndi anthu onse a nyumba ya Isiraeli ankayenda ndi Likasa+ la Yehova akufuula mokondwera+ ndiponso akuliza lipenga la nyanga ya nkhosa.+ 16  Likasa la Yehova litafika mu Mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli+ anasuzumira pawindo ndipo anaona Mfumu Davide akudumphadumpha nʼkumavina mozungulira pamaso pa Yehova. Ndipo Mikala anayamba kumunyoza mumtima mwake.+ 17  Kenako anaika Likasa la Yehova pamalo ake mutenti imene Davide anamanga.+ Ndiyeno Davide anapereka kwa Yehova+ nsembe zopsereza+ ndi nsembe zamgwirizano.+ 18  Davide atamaliza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamgwirizano, anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 19  Komanso anapatsa anthu onse mikate yozungulira yoboola pakati, makeke a zipatso za kanjedza ndi makeke a mphesa. Anapereka zimenezi ku gulu lonse la Isiraeli, mwamuna ndiponso mkazi. Kenako aliyense anapita kunyumba kwake. 20  Davide atabwerera kunyumba kwake kuti akadalitse banja lake, Mikala mwana wamkazi wa Sauli+ anatuluka kukakumana naye. Mikala anati: “Lero mfumu ya Isiraeli yaonetsa ulemerero wake podzivula pamaso pa akapolo aakazi a atumiki ake, ngati mmene munthu wopanda nzeru amadzivulira mopanda manyazi.”+ 21  Davide anauza Mikala kuti: “Inetu pamene paja ndimasangalala pamaso pa Yehova amene anandisankha mʼmalo mwa bambo ako ndi banja lawo lonse kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu a Yehova, Aisiraeli.+ Choncho ndidzasangalala pamaso pa Yehova. 22  Ndipitiriza kudzichepetsa kuposa pamenepa ndipo ndipitiriza kudziona ngati wotsika. Koma akapolo aakazi amene ukunenawo azindilemekeza.” 23  Choncho Mikala mwana wamkazi wa Sauli+ sanakhalepo ndi mwana mpaka tsiku limene anafa.

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “pakati.”
Kapena kuti, “anakhumudwa.”
Kutanthauza “Kukwiyira kwambiri Uza.”
Mawu akuti “Gati” mwina akunena za mzinda wa Gati-rimoni.