2 Samueli 9:1-13

  • Davide anasonyeza Mefiboseti chikondi chokhulupirika (1-13)

9  Kenako Davide ananena kuti: “Kodi pali aliyense amene anatsala mʼnyumba ya Sauli amene ndingamusonyeze chikondi chokhulupirika chifukwa cha Yonatani?”+  Ndiyeno panali mtumiki wa nyumba ya Sauli dzina lake Ziba.+ Choncho anaitanidwa kuti apite kwa Davide, ndipo mfumu inamufunsa kuti: “Kodi ndiwe Ziba?” Iye anayankha kuti: “Inde, ndine mtumiki wanu.”  Mfumu inati: “Kodi pali aliyense amene anatsala mʼnyumba ya Sauli amene ndingamusonyeze chikondi chokhulupirika cha Mulungu?” Ziba anauza mfumu kuti: “Alipo mwana wamwamuna wa Yonatani, wolumala mapazi.”+  Kenako mfumu inamufunsa kuti: “Akukhala kuti?” Ziba anayankha mfumu kuti: “Mʼnyumba ya Makiri,+ mwana wamwamuna wa Amiyeli, ku Lo-debara.”  Nthawi yomweyo Mfumu Davide anatumiza anthu kuti akamutenge kunyumba ya Makiri, mwana wa Amiyeli, ku Lo-debara.  Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli, atalowa nʼkuona Davide, nthawi yomweyo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake kufika pansi. Kenako Davide anati: “Mefiboseti!” Iye anayankha kuti: “Ine mtumiki wanu.”  Ndiyeno Davide anamuuza kuti: “Usaope. Ndikusonyeza ndithu chikondi chokhulupirika+ chifukwa cha Yonatani bambo ako. Ndikubwezera malo onse a agogo ako a Sauli ndipo iweyo nthawi zonse uzidya patebulo langa.”+  Mefiboseti atamva zimenezi anawerama mpaka nkhope yake kufika pansi ndipo anati: “Ine mtumiki wanu ndine ndani kuti mundikumbukire, galu wakufa+ ngati ine?”  Ndiyeno mfumu inaitana Ziba, mtumiki wa Sauli, nʼkumuuza kuti: “Chilichonse chimene chinali cha Sauli komanso chimene chinali cha nyumba yake, ndikupereka kwa mdzukulu wa mbuye wako.+ 10  Iweyo, ana ako aamuna ndi antchito ako, muzimulimira minda yake ndiponso kumukololera kuti anthu amʼnyumba ya mdzukulu wa mbuye wako azikhala ndi chakudya. Koma Mefiboseti, mdzukulu wa mbuye wako, azidya patebulo langa nthawi zonse.”+ Ziba anali ndi ana aamuna 15 ndi antchito 20.+ 11  Ziba anayankha mfumu kuti: “Zonse zimene mbuyanga mfumu mwandiuza, ine mtumiki wanu ndichita zomwezo.” Choncho Mefiboseti ankadya patebulo la Davide* ngati mmodzi wa ana a mfumu. 12  Mefiboseti anali ndi mwana wamngʼono wamwamuna dzina lake Mika,+ ndipo anthu onse amʼnyumba ya Ziba anali antchito a Mefiboseti. 13  Choncho Mefiboseti ankakhala ku Yerusalemu ndipo ankadya patebulo la mfumu nthawi zonse.+ Iye anali wolumala mapazi.+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “patebulo langa.”