Kalata yachiwiri yopita kwa Timoteyo 4:1-22

  • “Uzikwaniritsa mbali zonse za utumiki wako” (1-5)

    • Lalikira mawu modzipereka (2)

  • “Ndamenya nkhondo yabwino” (6-8)

  • Zina zomwe Paulo ananena (9-18)

  • Kupereka moni (19-22)

4  Pamaso pa Mulungu ndi Khristu Yesu, amene adzaweruze+ amoyo ndi akufa,+ akadzaonekera+ ndiponso akadzabwera mu Ufumu wake,+ ndikukulamula mwamphamvu kuti:  Lalikira mawu.+ Uzilalikira modzipereka, pa nthawi yabwino ndi pa nthawi yovuta. Dzudzula,+ tsutsa, dandaulira, ndipo uzichita zimenezi ndi luso la kuphunzitsa+ ndiponso moleza mtima kwambiri.  Chifukwa idzafika nthawi imene anthu sadzafunanso kuphunzitsidwa zolondola,+ koma mogwirizana ndi zimene amalakalaka, adzapeza aphunzitsi oti aziwauza zowakomera mʼkhutu.+  Iwo adzasiya kumvetsera choonadi nʼkumamvetsera nkhani zonama.  Koma iwe ukhalebe woganiza bwino pa zinthu zonse, uzipirira mavuto,+ uzigwira ntchito ya mlaliki* ndiponso uzikwaniritsa mbali zonse za utumiki wako.+  Ndili ngati nsembe yachakumwa imene ikuthiridwa paguwa la nsembe,+ ndipo nthawi yoti ndimasuke+ yatsala pangʼono.  Ndamenya nkhondo yabwino.+ Ndathamanga pa mpikisanowu mpaka pamapeto.+ Ndakhalabe ndi chikhulupiriro.  Panopa andisungira chisoti chachifumu cha olungama.+ Ambuye, woweruza wachilungamo,+ adzandipatsa mphotoyi pa tsikulo.+ Sikuti adzapatsa ine ndekha, koma adzapatsanso onse amene akhala akuyembekezera kuti iye adzaonekere.  Yesetsa kuti ubwere posachedwapa. 10  Kuno Dema+ wandisiya chifukwa chokonda zinthu zamʼdzikoli* ndipo wapita ku Tesalonika. Keresike wapita ku Galatiya ndipo Tito wapita ku Dalimatiya. 11  Luka yekha ndi amene watsala. Ubwerenso ndi Maliko chifukwa amandithandiza pa utumiki wanga. 12  Koma Tukiko+ ndamutuma ku Efeso. 13  Ukamabwera unditengerekonso chovala champhepo chimene ndinachisiya ku Torowa kwa Karipo komanso mipukutu, makamaka yazikopa ija. 14  Alekizanda wosula zinthu zakopa uja, anandichitira zoipa kwambiri. Yehova* adzamubwezera mogwirizana ndi ntchito zake.+ 15  Iwenso uchenjere naye, chifukwa anatsutsa uthenga wathu mwamphamvu. 16  Pamene ndinkadziteteza koyamba pa mlandu wanga palibe anakhala kumbali yanga, moti onse anandisiya. Komabe asakhale ndi mlandu. 17  Koma Ambuye anaima nane pafupi nʼkundipatsa mphamvu. Anachita zimenezi kuti kudzera mwa ine, ntchito yolalikira ichitike mokwanira, ndi kuti mitundu yonse ya anthu imve uthengawo.+ Ndiponso ndinapulumutsidwa mʼkamwa mwa mkango.+ 18  Ambuye adzandipulumutsa ku choipa chilichonse ndipo adzandisunga kuti ndikakhale mu Ufumu wake wakumwamba.+ Iye apatsidwe ulemerero mpaka muyaya. Ame. 19  Undiperekere moni kwa Purisika ndi Akula+ komanso banja la Onesiforo.+ 20  Erasito+ anatsala ku Korinto, koma Terofimo+ ndinamusiya akudwala ku Mileto. 21  Uyesetse kuti ufike kuno nyengo yozizira isanayambe. Ebulo, Pude, Lino, Kalaudiya komanso abale onse akupereka moni. 22  Ambuye akhale nawe chifukwa cha mzimu umene umasonyeza. Kukoma mtima kwake kwakukulu kukhale nanu.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “yolalikira uthenga wabwino.”
Kapena kuti, “za mʼnthawi ino.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.