Kalata Yachiwiri ya Yohane 1:1-13
1 Ine monga munthu wachikulire,* ndikulembera mayi wosankhidwa ndi Mulungu ndiponso ana ake amene ndimawakonda kwambiri. Ndipo si ine ndekha amene ndimawakonda, chifukwa onse amene adziwa choonadi amawakondanso.
2 Timakukondani chifukwa cha choonadi chimene chili mumtima mwathu, ndipo chidzakhalabe mwa ife mpaka muyaya.
3 Mulungu, yemwe ndi Atate wathu wakumwamba, komanso Mwana wake Yesu Khristu, adzatiphunzitsa mfundo zolondola ndiponso kutisonyeza chikondi. Adzatisonyezanso kukoma mtima kwakukulu ndi chifundo komanso adzatipatsa mtendere.
4 Ndikusangalala kwambiri chifukwa ndapeza ena mwa ana anu akuyenda mʼchoonadi+ mogwirizana ndi lamulo limene tinalandira kwa Atate.
5 Chotero ndikukupemphani mayi, kuti tizikondana. (Sindikukulemberani lamulo latsopano, koma lomwe lija limene takhala nalo kuyambira pachiyambi.)+
6 Ndipo chikondi chimatanthauza kupitiriza kuyenda motsatira malamulo ake.+ Monga mmene munamvera kuyambira pachiyambi, lamulo lake ndi lakuti nthawi zonse muzisonyeza chikondi.
7 Komabe samalani chifukwa anthu ambiri opusitsa anzawo ayamba kupezeka mʼdzikoli.+ Anthu amenewa amatsutsa zoti Yesu Khristu anabwera monga munthu.+ Amene amachita zimenezi ndi wopusitsa ena ndiponso wokana Khristu.+
8 Samalani kuti musataye zinthu zimene tinakuthandizani kuti muzipeze nʼcholinga choti mudzalandire madalitso onse amene Mulungu wakukonzerani.+
9 Aliyense amene amachita zosemphana ndi zimene Khristu ankaphunzitsa, ndiye kuti akukana Mulungu.+ Koma Atate ndiponso Mwana, amasangalala ndi munthu amene amachita zinthu mogwirizana ndi zimene iye ankaphunzitsa.+
10 Wina akabwera ndi chiphunzitso chosiyana ndi ichi, musamulandire mʼnyumba zanu+ kapena kumupatsa moni.
11 Aliyense amene wamupatsa moni amakhala ngati akuchita nawo ntchito zake zoipazo.
12 Ngakhale kuti ndili ndi zambiri zoti ndikulembereni, sindikufuna kuzilemba papepala ndi inki. Koma ndikuyembekezera kubwera kwa inu kuti ndidzalankhule nanu pamasomʼpamaso nʼcholinga choti mudzasangalale kwambiri.
13 Ana a mchemwali wanu wosankhidwa ndi Mulungu, akupereka moni.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Ine monga mkulu.”