Kwa Aefeso 1:1-23

  • Moni (1, 2)

  • Madalitso auzimu (3-7)

  • Kusonkhanitsa zinthu zonse kwa Akhristu (8-14)

    • Kukhazikitsa “dongosolo” pa nthawi imene anaikiratu (10)

    • Anaikidwa chidindo ndi mzimu woyera ngati “chikole chotsimikizira” (13, 14)

  • Paulo anathokoza Mulungu chifukwa cha chikhulupiriro cha Aefeso ndipo anawapempherera (15-23)

1  Ine Paulo, mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, ndine mtumwi wa Khristu Yesu ndipo ndikulembera oyera amene ali ku Efeso,+ amene ndi ophunzira a Khristu Yesu okhulupirika kuti:  Mulungu Atate wathu komanso Ambuye Yesu Khristu akupatseni kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere.  Atamandike Mulungu amene ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, chifukwa watidalitsa ndi dalitso lililonse lauzimu mʼmalo akumwamba mogwirizana ndi Khristu.+  Iye anatisankha kuti tikakhale ogwirizana ndi Khristu dziko lisanakhazikitsidwe nʼcholinga choti tizisonyeza chikondi komanso kuti tikhale oyera ndiponso opanda chilema+ pamaso pa Mulungu.  Chifukwa anatisankhiratu+ kuti adzatitenga nʼkukhala ana ake+ kudzera mwa Yesu Khristu, mogwirizana ndi zimene zinamusangalatsa komanso zimene anafuna.+  Anachita zimenezi kuti iye atamandike chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu+ kwaulemerero kumene anatisonyeza kudzera mwa mwana wake wokondedwa.+  Kudzera mwa mwana wakeyu, tinamasulidwa ndi dipo* la magazi ake,+ inde, takhululukidwa machimo athu,+ mogwirizana ndi kukoma mtima kwake kwakukulu.  Iye anachititsa kuti kukoma mtima kumeneku kukhale kochuluka kwa ife potithandiza kuti tikhale anzeru komanso omvetsa zinthu,*  potiululira chinsinsi chake chopatulika+ chokhudza chifuniro chake. Chinsinsicho nʼchogwirizana ndi zimene zimamusangalatsa ndiponso zimene amafuna, 10  zoti akakhazikitse dongosolo lake pa nthawi imene anaikiratu. Dongosolo limenelo ndi kusonkhanitsa zinthu zonse pamodzi kuti zikhale zogwirizana ndi Khristu, zinthu zakumwamba ndi zinthu zapadziko lapansi.+ Inde, zinthu zonse zidzasonkhanitsidwa kwa Khristu, 11  amene chifukwa chogwirizana naye tinasankhidwa kuti tidzalandire cholowa,+ chifukwa anatisankha kale mwa kufuna kwake, iye amene amachita zinthu zonse mogwirizana ndi chifuniro chake. 12  Anachita zimenezo kuti ifeyo amene ndife oyamba kukhala ndi chiyembekezo mwa Khristu titamande Mulungu chifukwa iye ndi wamkulu. 13  Koma inunso munakhala ndi chiyembekezo mwa iye mutamva mawu a choonadi, omwe ndi uthenga wabwino wonena za chipulumutso chanu. Mutakhulupirira, Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu woyera umene analonjeza kuti akuikeni chidindo+ ndipo anagwiritsa ntchito Khristu kuti achite zimenezi. 14  Mzimu woyerawo uli ngati chikole chotsimikizira kuti tidzalandira zimene Mulungu watilonjeza.+ Mulungu anachita zimenezi nʼcholinga choti apereke dipo+ kuti anthu ake amasulidwe.+ Zimenezi zidzachititsa kuti atamandidwe komanso kupatsidwa ulemerero. 15  Ndiye chifukwa chake inenso, kuyambira pamene ndinamva za chikhulupiriro chimene muli nacho mwa Ambuye Yesu komanso chikondi chimene mumachisonyeza kwa oyera onse, 16  sindinaleke kuyamika Mulungu chifukwa cha inu. Ndikupitirizabe kukupemphererani, 17  kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate waulemerero, akupatseni mzimu wa nzeru kuti mumvetse zimene Iye akuulula pamene mukuphunzira kuti mumudziwe molondola.+ 18  Mulungu watsegula mitima yanu nʼcholinga choti muone komanso mudziwe chiyembekezo chimene wakupatsani ndiponso zinthu zabwino kwambiri zimene walonjeza kwa oyera,+ 19  ndi kutinso mudziwe kukula kwa mphamvu zake zopambana zimene wazisonyeza kwa okhulupirirafe.+ Mphamvu zake zazikuluzo zikuonekera muntchito zake, 20  pamene anazigwiritsa ntchito poukitsa Khristu kwa akufa nʼkumukhazika kudzanja lake lamanja+ mʼmalo akumwamba. 21  Anamuika pamwamba kuposa boma lililonse, ulamuliro uliwonse, anthu amphamvu onse, ambuye onse, ndi aliyense amene ali ndi dzina laulemu,+ osati mu nthawi* ino yokha, komanso imene ikubwerayo. 22  Mulungu anaikanso zinthu zonse pansi pa mapazi ake,+ ndipo anamuika kuti akhale mutu wa zinthu zonse zimene ndi zokhudzana ndi mpingo+ 23  umene ndi thupi lake+ ndipo ndi wodzaza ndi Khristu, amene amadzaza zinthu zonse mokwanira.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “komanso ozindikira.”