Kwa Aefeso 2:1-22

  • Anapangitsa kuti akhale amoyo mogwirizana ndi Khristu (1-10)

  • Anagwetsa khoma lomwe linkawalekanitsa (11-22)

2  Kuwonjezera pamenepo, Mulungu anapangitsa kuti mukhale amoyo ngakhale kuti munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu komanso machimo anu.+  Pa nthawi ina munkachita zimenezi mogwirizana ndi nthawi* za mʼdzikoli,+ pomvera wolamulira wa mpweya+ umene umalamulira zochita za anthu. Mpweya umenewu, kapena kuti kaganizidwe+ kameneka, tsopano kakugwira ntchito mwa ana osamvera.  Inde, pa nthawi ina pamene tinkakhala pakati pawo, tinkachita zinthu motsatira zilakolako za thupi lathu.+ Tinkachita zofuna za thupi ndi maganizo athu,+ ndipo mwachibadwa tinali ana oyenera kulandira mkwiyo wa Mulungu+ mofanana ndi ena onse.  Koma popeza kuti Mulungu ndi wachifundo chochuluka,+ komanso chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatisonyeza,+  anapangitsa kuti tikhale amoyo limodzi ndi Khristu, ngakhale kuti tinali akufa chifukwa cha machimo athu,+ ndipotu inu mwapulumutsidwa chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu.  Kuwonjezera pamenepo, Mulungu anatichititsa kuti tikhale ndi moyo ndipo anatipatsa malo oti tikakhale kumwamba chifukwa anatigwirizanitsa ndi Khristu Yesu.+  Anachita zimenezi kuti mu nthawi* zimene zikubwera, iye adzatisonyeze chuma chopambana cha kukoma mtima kwake kwakukulu. Mulungu adzachita zimenezi potisonyeza chifundo chifukwa ndife ophunzira a Khristu Yesu.  Inu amene muli ndi chikhulupiriro, mwapulumutsidwa chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kumeneku.+ Sikuti zimenezi zinatheka chifukwa cha khama lanu, koma ndi mphatso ya Mulungu.  Ayi, sikuti zinatheka chifukwa cha ntchito,+ kuti munthu asakhale ndi chifukwa chodzitamandira. 10  Ndife ntchito ya manja a Mulungu. Iye ndi amene anatilenga+ ndipo ndife ogwirizana ndi Khristu Yesu+ kuti tichite ntchito zabwino, zimene Mulungu anakonzeratu kuti tiyendemo. 11  Choncho muzikumbukira kuti nthawi ina, inu amene munali anthu a mitundu ina, anthu odulidwa ankakutchulani kuti anthu osadulidwa. Mdulidwe umenewu umachitika pathupi ndi manja a anthu. 12  Pa nthawi imene ija, Khristu simunkamudziwa, munali otalikirana ndi mtundu wa Isiraeli komanso simunali nawo mʼmapangano a lonjezo.+ Munalibe chiyembekezo ndipo Mulungu simunkamudziwa mʼdzikoli.+ 13  Koma tsopano mogwirizana ndi Khristu Yesu, inu amene pa nthawi ina munali kutali, mwabwera pafupi chifukwa cha magazi a Khristu. 14  Chifukwa iye amene anaphatikiza magulu awiri aja kukhala gulu limodzi+ nʼkugwetsa khoma lomwe linkawalekanitsa limene linali pakati pawo,+ watibweretsera mtendere.+ 15  Ndi thupi lake, anathetsa chinthu choyambitsa chidani, chomwe ndi Chilamulo chimene chinali ndi malamulo komanso malangizo. Anachithetsa kuti magulu awiri omwe ndi ogwirizana ndi iye, akhale munthu mmodzi watsopano+ komanso kuti akhazikitse mtendere. 16  Ndiponso kuti kudzera mwa mtengo wozunzikirapo,*+ agwirizanitse magulu awiri a anthuwo kwa Mulungu ndipo anthuwo akhale thupi limodzi, chifukwa anali atapheratu chidanicho+ kudzera mu imfa yake. 17  Choncho iye anabwera ndipo analengeza uthenga wabwino wa mtendere kwa inu amene munali kutali. Analengezanso za mtendere kwa amene anali pafupi, 18  chifukwa kudzera mwa iye, magulu onse awiriwa angathe kufika kwa Atate mosavuta kudzera mwa mzimu umodzi. 19  Choncho, si inunso anthu osadziwika kapena alendo,+ koma mofanana ndi oyerawo inunso ndinu nzika+ ndipo ndinu a mʼbanja la Mulungu.+ 20  Mwamangidwa pamaziko a atumwi ndi aneneri+ ndipo Khristu Yesu ndi mwala wapakona wa mazikowo.+ 21  Mogwirizana ndi iye, nyumba yonse, popeza ndi yolumikizana bwino,+ ikukula nʼkukhala kachisi woyera wa Yehova.*+ 22  Mogwirizana ndi iye, inunso limodzi ndi anthu ena mukumangidwa pamodzi kuti mukhale malo oti Mulungu akhalemo mwa mzimu.+