Kwa Aefeso 6:1-24

  • Malangizo opita kwa makolo ndi ana (1-4)

  • Malangizo opita kwa akapolo ndi ambuye (5-9)

  • Zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu (10-20)

  • Moni womaliza (21-24)

6  Ana inu, muzimvera makolo anu+ mogwirizana ndi zimene Ambuye amafuna, chifukwa kuchita zimenezi nʼkoyenera.  “Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu.”+ Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. Lonjezo lake ndi lakuti:  “Kuti zinthu zikuyendereni bwino, ndiponso kuti mukhale ndi moyo wautali padziko lapansi.”  Inu abambo, musamapsetse mtima ana anu,+ koma pitirizani kuwalera powapatsa malangizo*+ komanso kuwaphunzitsa mogwirizana ndi zimene Yehova* amanena.+  Akapolo inu, muzimvera anthu amene ndi ambuye anu.+ Muziwaopa ndi kuwalemekeza kuchokera pansi pa mtima, ngati mmene mumachitira ndi Khristu.  Musamachite zimenezi pokhapokha pamene anthu akukuonani pongofuna kuwasangalatsa,*+ koma ngati akapolo a Khristu amene akuchita chifuniro cha Mulungu ndi mtima wonse.+  Muzitumikira ambuye anu modzipereka, ngati mukutumikira Yehova*+ osati anthu,  chifukwa mukudziwa kuti pa chabwino chilichonse chimene munthu angachite, Yehova* adzamupatsa mphoto,+ kaya munthuyo ndi kapolo kapena mfulu.  Inu ambuye, muzichitiranso akapolo anu chimodzimodzi. Musamawaopseze chifukwa mukudziwa kuti Ambuye wa nonsenu, wa iwowo ndi wa inuyo, ali kumwamba+ ndipo alibe tsankho. 10  Pomaliza ndikuti, pitirizani kupeza mphamvu+ kuchokera kwa Ambuye chifukwa mphamvu zake nʼzazikulu. 11  Valani zida zonse zankhondo+ zochokera kwa Mulungu kuti musagonje polimbana ndi zochita zachinyengo* za Mdyerekezi, 12  chifukwa sitikulimbana+ ndi anthu athupi la magazi ndi nyama, koma tikulimbana ndi ziwanda+ zimene zili kumwamba, zomwe ndi maboma komanso maulamuliro amene akulamulira dziko limene lili mumdimali. 13  Pa chifukwa chimenechi, nyamulani zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu+ kuti patsiku loipa musadzagonje, ndiponso kuti mutachita zonse bwinobwino, mudzathe kulimba. 14  Choncho khalani olimba, mutamanga kwambiri choonadi mʼchiuno mwanu ngati lamba,+ mutavala chodzitetezera pachifuwa chachilungamo,+ 15  komanso mutavala nsapato kumapazi anu pokonzekera kulengeza uthenga wabwino wamtendere.+ 16  Koposa zonsezi, nyamulani chishango chachikulu chachikhulupiriro,+ chimene mudzathe kuzimitsira mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.+ 17  Komanso valani chipewa cha chipulumutso+ ndipo nyamulani lupanga la mzimu, lomwe ndi mawu a Mulungu.+ 18  Pamene mukuchita zimenezi, muzipemphera pa chochitika chilichonse mu mzimu,+ pogwiritsa ntchito pemphero+ ndi pembedzero la mtundu uliwonse. Kuti muchite zimenezi khalani maso ndipo nthawi zonse muzipemphera mopembedzera mʼmalo mwa oyera onse. 19  Muzindipemphereranso ineyo kuti ndikayamba kulankhula ndizipeza mawu oyenerera nʼcholinga choti ndizitha kulankhula molimba mtima ndikamalalikira zokhudza chinsinsi chopatulika cha uthenga wabwino,+ 20  umene ndine kazembe+ wake womangidwa ndi unyolo ndiponso kuti ndilankhule za uthengawo molimba mtima ngati mmene ndikuyenera kuchitira. 21  Tsopano, kuti mudziwenso mmene zinthu zikuyendera pa moyo wanga ndi mmene ine ndilili, Tukiko,+ mʼbale wokondedwa ndiponso mtumiki wokhulupirika wa Ambuye, adzakufotokozerani zonse.+ 22  Ndamutumiza kwa inu ndi cholinga chimenechi, kuti mudziwe za moyo wathu ndiponso kuti atonthoze mitima yanu. 23  Mtendere ndi chikondi ndiponso chikhulupiriro zochokera kwa Mulungu Atate ndi kwa Ambuye Yesu Khristu, zikhale pa abalenu. 24  Kukoma mtima kwakukulu kukhale pa onse amene ali ndi chikondi chenicheni pa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Mawu a M'munsi

Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mwachiphamaso pofuna kusangalatsa anthu.”
Kapena kuti, “ndi ziwembu.”