Kwa Agalatiya 1:1-24

  • Moni (1-5)

  • Palibe uthenga wina wabwino (6-9)

  • Uthenga wabwino umene Paulo ankalalikira ndi wochokera kwa Mulungu (10-12)

  • Kutembenuka kwa Paulo komanso zimene ankachita poyamba (13-24)

1  Ine Paulo, ndine mtumwi, osati wochokera kwa anthu kapena woikidwa kudzera mwa munthu, koma kudzera mwa Yesu Khristu+ komanso kudzera mwa Mulungu Atate+ amene anamuukitsa kwa akufa.  Ineyo limodzi ndi abale onse amene ali ndi ine tikupereka moni ku mipingo ya ku Galatiya:  Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu.  Iye anadzipereka chifukwa cha machimo athu,+ kuti atipulumutse ku dziko loipali,*+ mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu amene ndi Atate wathu.+  Ulemerero ukhale kwa Mulunguyo mpaka muyaya. Ame.  Ine ndikudabwa kuti mwapatuka mwamsanga* kuchoka kwa Mulungu amene anakuitanani kudzera mu kukoma mtima kwakukulu kwa Khristu ndipo mwayamba kumvetsera uthenga wabwino wamtundu wina.+  Koma umenewo sikuti ndi uthenga wabwino, kungoti pali anthu ena amene akukusokonezani+ ndipo akufuna kupotoza uthenga wabwino wonena za Khristu.  Komabe, ngati ifeyo kapena mngelo wochokera kumwamba angalengeze nkhani ina kwa inu nʼkumanena kuti akulengeza uthenga wabwino, koma nkhaniyo nʼkukhala yosiyana ndi uthenga wabwino umene tinaulengeza kwa inu, ameneyo akhale wotembereredwa.  Monga mmene tanenera kale, ndikunenanso kuti, Aliyense amene akulengeza nkhani ina kwa inu nʼkumati ndi uthenga wabwino, koma yosiyana ndi imene munalandira, ameneyo akhale wotembereredwa. 10  Ndiye kodi panopa ndikufuna kuti ndizikondedwa ndi anthu kapena Mulungu? Kapena kodi ndikungofuna kusangalatsa anthu? Ndikanakhala kuti ndikusangalatsabe anthu, sindikanakhala kapolo wa Khristu. 11  Chifukwa ndikufuna kuti mudziwe abale, kuti uthenga wabwino umene ndinalengeza kwa inu sunachokere kwa anthu.+ 12  Uthengawu sindinaulandire kwa munthu ndipo sindinachite kuphunzitsidwa, koma Yesu Khristu ndi amene anandiululira uthenga umenewu. 13  Munamva ndithu zimene ndinkachita ndili mʼChiyuda,+ kuti ndinkazunza kwambiri mpingo wa Mulungu ndipo ndinapitiriza kuuwononga.+ 14  Ndinkachita bwino kwambiri mʼchipembedzo cha Chiyuda kuposa anzanga ambiri a fuko langa, omwe anali amsinkhu wanga, chifukwa ndinali wodzipereka kwambiri pa miyambo ya makolo anga.+ 15  Koma pamene Mulungu, amene anandichititsa kuti ndibadwe komanso kundiitana kudzera mu kukoma mtima kwake kwakukulu,+ anaona kuti nʼzabwino kuti 16  aulule za Mwana wake kudzera mwa ine, nʼcholinga choti ndilengeze kwa anthu a mitundu ina+ uthenga wabwino wonena za iye, sindinapite kukakambirana ndi munthu aliyense* nthawi yomweyo. 17  Sindinapitenso ku Yerusalemu kwa amene anakhala atumwi ine ndisanakhale, koma ndinapita ku Arabiya, kenako ndinabwereranso ku Damasiko.+ 18  Ndiye pambuyo pa zaka zitatu, ndinapita ku Yerusalemu+ kukacheza kwa Kefa*+ ndipo ndinakhala naye masiku 15. 19  Koma atumwi ena onse sindinawaone kupatulapo Yakobo,+ mchimwene wa Ambuye. 20  Zimene ndikukulemberanizi, ndikukutsimikizirani pamaso pa Mulungu kuti sindikunama. 21  Kenako ndinalowa mʼmadera a Siriya ndi Kilikiya.+ 22  Koma anthu a mʼmipingo ya ku Yudeya yomwe inali yogwirizana ndi Khristu, sankandidziwa bwinobwino. 23  Iwo ankangomva kuti: “Munthu amene kale ankatizunza uja+ komanso kuwononga mipingo* tsopano akulengeza uthenga wabwino.”+ 24  Choncho anthuwo anayamba kulemekeza Mulungu chifukwa cha ine.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ku nthawi yoipayi.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “mwapatutsidwa mwamsanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi anthu a thupi la nyama ndi magazi.”
Amene ankadziwikanso kuti Petulo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “chikhulupiriro.”