Kalata Yopita kwa Aheberi 12:1-29

  • Yesu, Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu (1-3)

    • Gulu lalikulu la mboni (1)

  • Osapeputsa chilango cha Yehova (4-11)

  • Muziwongola njira zimene mapazi anu akuyendamo (12-17)

  • Kufika ku Yerusalemu wakumwamba (18-29)

12  Choncho, popeza tazunguliridwa ndi gulu lalikulu chonchi la mboni,* tiyeninso titaye cholemera chilichonse ndi tchimo limene limatikola mosavuta.+ Ndipo tithamange mopirira mpikisano umene talowawu.+  Tichite zimenezi pamene tikuyangʼanitsitsa Mtumiki Wamkulu ndi Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu, Yesu.+ Chifukwa chodziwa kuti adzasangalala mʼtsogolo, anapirira mtengo wozunzikirapo.* Iye sanasamale kuti zochititsa manyazi zimuchitikira ndipo panopa wakhala kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.+  Choncho ganizirani mozama za munthu amene anapirira malankhulidwe onyoza amenewo a anthu ochimwa,+ amene polankhula zimenezo ankangodzivulaza okha. Ganizirani za munthu ameneyu kuti musatope nʼkutaya mtima.+  Polimbana ndi tchimoli, sikuti mwamenya nkhondo mpaka kufika potaya magazi anu.  Ndipo mwaiwaliratu malangizo okudandaulirani ngati amene bambo amauza ana ake kuti: “Mwana wanga, usapeputse chilango* cha Yehova,* kapena kutaya mtima pamene iye akukudzudzula.  Chifukwa Yehova* amalanga aliyense amene iye amamukonda, ndipo amakwapula aliyense amene iye amamuona kuti ndi mwana wake.”+  Muyenera kupirira kuti muphunzitsidwe.* Mulungu akuchita nanu zinthu ngati ana ake.+ Ndi mwana wanji amene bambo ake samupatsa chilango?+  Koma ngati simunalandire chilango chimene tonsefe tiyenera kulandira, ndiye kuti ndinu ana a munthu wina, osati ana ake enieni.  Bambo athu otibereka ankatilanga ndipo tinkawalemekeza. Ndiye kuli bwanji Atate wa moyo wathu wauzimu? Kodi sitiyenera kuwagonjera koposa pamenepo kuti tikhale ndi moyo?+ 10  Chifukwa bambo athu otiberekawo, anatilanga kwa nthawi yochepa mogwirizana ndi zimene ankaziona kuti nʼzoyenera, koma Mulungu amatilanga kuti zinthu zitiyendere bwino ndiponso kuti tikhale oyera ngati iyeyo.+ 11  Nʼzoona kuti palibe chilango chimene chimakhala chosangalatsa pa nthawi yomwe ukuchilandira, koma chimakhala chowawa. Komabe pambuyo pake, kwa anthu amene aphunzirapo kanthu pa chilangocho, chimabala chipatso chamtendere, chomwe ndi chilungamo. 12  Choncho limbitsani manja ofooka komanso mawondo olobodoka,+ 13  ndipo pitirizani kuwongola njira zimene mapazi anu akuyendamo+ kuti chiwalo chimene chavulala chisaguluke, koma chichiritsidwe. 14  Muziyesetsa kukhala mwamtendere ndi anthu onse,+ komanso kukhala oyera+ chifukwa ngati munthu si woyera, sadzaona Ambuye. 15  Muonetsetse kuti wina asalephere kulandira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, kuti pasatuluke muzu wapoizoni nʼkuyambitsa mavuto komanso kuchititsa kuti ambiri aipitsidwe.+ 16  Muonetsetsenso kuti pakati panu pasakhale wachiwerewere* kapena aliyense wosayamikira zinthu zopatulika ngati Esau, amene anapereka udindo wake monga woyamba kubadwa pousinthanitsa ndi chakudya chodya kamodzi kokha.+ 17  Mukudziwa kuti pambuyo pake, pamene ankafuna kulandira madalitso,* anamukanira. Ngakhale kuti anayesetsa ndi mtima wonse kwinaku akulira,+ kuti bambo ake asinthe maganizo, sizinatheke. 18  Inu simunafike paphiri limene mungathe kulikhudza,+ loyaka moto,+ lokhala ndi mtambo wakuda, mdima wandiweyani, lowombedwa ndi mphepo yamkuntho+ 19  komanso limene panamveka kulira kwa lipenga+ ndi mawu a winawake+ ndipo anthu atawamva, anapempha kuti asawauzenso mawu ena.+ 20  Chifukwa anachita mantha kwambiri ndi lamulo lakuti: “Ngakhalenso nyama iliyonse imene ingakhudze phirilo, iponyedwe miyala.”+ 21  Komanso, zimene anaona kumeneko zinali zoopsa kwambiri moti Mose anati: “Ndikuchita mantha ndipo ndikunjenjemera.”+ 22  Koma mwafika kuphiri la Ziyoni+ ndi mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba,+ kumene kuli angelo ambirimbiri,* 23  pamsonkhano wawo waukulu.+ Kumenenso kuli mpingo wa woyamba kubadwayo, mpingo wa iwo amene mayina awo alembedwa kumwamba. Kumeneko kulinso Mulungu, Woweruza wa onse.+ Kulinso olungama amene akukhala ndi moyo mogwirizana ndi mphamvu ya mzimu woyera+ omwe athandizidwa kukhala angwiro.+ 24  Kulinso Yesu, mkhalapakati+ wa pangano latsopano,+ ndiponso magazi amene awazidwa, omwe amalankhula mʼnjira yabwino kwambiri kuposa magazi a Abele.+ 25  Samalani kuti musasiye* kumumvera amene akulankhulayo. Chifukwa ngati omwe anakana kumvera amene anapereka chenjezo la Mulungu padziko lapansi sanapulumuke, ndiye kuli bwanji ifeyo? Nafenso sitidzapulumuka tikapanda kumvera amene amalankhula ali kumwamba.+ 26  Pa nthawiyo, mawu ake anagwedeza dziko lapansi,+ koma tsopano walonjeza kuti: “Ndidzagwedezanso kumwamba, osati dziko lapansi lokha.”+ 27  Mawu akuti “ndidzagwedezanso,” akusonyeza kuti zinthu zimene adzazigwedezezo zidzachotsedwa ndipo zinthu zimenezi sizinapangidwe ndi Mulungu. Adzazichotsa kuti zomwe sizikugwedezeka zitsale. 28  Choncho, popeza kuti tidzalandira Ufumu umene sungagwedezeke, tiyeni tikhalebe okhulupirika kuti Mulungu apitirize kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu, kuti tizichita utumiki wopatulika mʼnjira yovomerezeka, moopa Mulungu komanso mwaulemu kwambiri. 29  Chifukwa Mulungu wathu ali ngati moto wowononga.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi mtambo waukulu wa mboni.”
Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “chilango” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.
Kapena kuti, “chikhale chilango chanu.”
Kapena kuti, “kulandira madalitso ngati cholowa.”
Kapena kuti, “masauzande masauzande.”
Kapena kuti, “musapeze zifukwa zokanira; musanyalanyaze.”