Kalata Yopita kwa Aheberi 3:1-19

  • Yesu ndi wamkulu kuposa Mose (1-6)

    • Zinthu zonse zinapangidwa ndi Mulungu (4)

  • Chenjezo lakuti tisakhale opanda chikhulupiriro (7-19)

    • “Lero mukamva mawu a Mulungu” (7, 15)

3  Choncho, abale athu oyera, amene muli mʼgulu la anthu oitanidwa kumwamba,+ ganizirani za Yesu, mtumwi ndi mkulu wa ansembe amene tikumuvomereza.+  Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene anamuika kukhala mtumwi ndi mkulu wa ansembe,+ ngati mmenenso Mose analili wokhulupirika mʼnyumba yonse ya Mulungu.+  Yesu akuyenera kupatsidwa ulemerero waukulu+ kuposa Mose, chifukwa womanga nyumba amakhala wolemekezeka kuposa nyumbayo.  Nʼzoona kuti nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.  Mose anali mtumiki wokhulupirika mʼnyumba yonse ya Mulungu ndipo utumiki wakewo unali umboni wa zinthu zimene zidzanenedwe mʼtsogolo.  Koma Khristu anali mwana ndipo ankayangʼanira nyumba ya Mulungu mokhulupirika.+ Ife tikhalabe nyumba ya Mulunguyo+ tikapitiriza kukhala ndi ufulu wa kulankhula komanso kugwira mwamphamvu chiyembekezo chimene timachinyadira mpaka mapeto.  Choncho mogwirizana ndi zimene mzimu woyera ukunena+ kuti: “Lero mukamva mawu a Mulungu,  musaumitse mitima yanu ngati mmene zinakhalira pamene makolo anu anandipsetsa mtima kwambiri, ngati mmene zinalili pa tsiku limene anandiyesa mʼchipululu.+  Mʼchipululumo, makolo anu anandiyesa ngakhale kuti anali ataona ntchito zanga kwa zaka 40.+ 10  Nʼchifukwa chake ndinanyansidwa ndi mʼbadwo umenewo, ndipo ndinati, ‘Mitima yawo imasochera nthawi zonse ndipo njira zanga sakuzidziwa.’ 11  Choncho ndinalumbira nditakwiya kuti, ‘Sadzalowa mumpumulo wanga.’”+ 12  Chenjerani abale kuti pakati panu, wina asachoke kwa Mulungu wamoyo nʼkukhala ndi mtima woipa wopanda chikhulupiriro.+ 13  Mʼmalomwake, pitirizani kulimbikitsana tsiku ndi tsiku, nthawi iliyonse imene mukuti “Lero,”+ kuti chinyengo champhamvu cha uchimo chisaumitse mtima wa aliyense wa inu. 14  Chifukwa timachita nawo zimene Khristu akuchita, ngati zinthu zimene tinkadalira poyamba tazigwira mwamphamvu mpaka mapeto.+ 15  Paja Malemba amati: “Lero mukamva mawu a Mulungu, musaumitse mitima yanu ngati mmene zinakhalira pamene makolo anu anandipsetsa mtima kwambiri.”+ 16  Kodi paja ndi ndani amene anamva koma nʼkupsetsa mtima Mulungu? Kodi si anthu onse amene anatuluka mʼdziko la Iguputo motsogoleredwa ndi Mose?+ 17  Komanso, kodi Mulungu ananyansidwa ndi ndani kwa zaka 40?+ Kodi si anthu amene anachimwa aja, amene anafera mʼchipululu?+ 18  Nanga kodi analumbirira ndani kuti sadzalowa mumpumulo wake? Kodi si omwe aja amene sanamumvere? 19  Choncho, tikuona kuti sakanatha kulowa mumpumulowo chifukwa anali opanda chikhulupiriro.+

Mawu a M'munsi