Amosi 2:1-16

  • Ziweruzo chifukwa chogalukira mobwerezabwereza (1-16)

2  “Yehova wanena kuti,‘“Popeza Mowabu anandigalukira mobwerezabwereza,*+ sindidzamusinthira chigamulo changa.Chifukwa anatentha mafupa a mfumu ya Edomu kuti apeze laimu.   Choncho ndidzatumiza moto ku Mowabu,Ndipo udzawotcheratu nsanja zolimba za Kerioti.+Mowabu adzafa pakati pa phokoso,Pakati pa mfuu yankhondo ndiponso kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa.+   Ndidzachotsa wolamulira* pakati pake,Komanso ndidzapha akalonga ake onse limodzi ndi iyeyo,”+ watero Yehova.’   Yehova wanena kuti,‘Popeza Yuda anandigalukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa.Chifukwa chakuti anakana malamulo* a Yehova,Ndiponso chifukwa sanatsatire malangizo ake.+Koma anasocheretsedwa ndi mabodza amene makolo awo ankatsatira.+   Choncho ndidzatumiza moto ku YudaNdipo udzawotcheratu nsanja zolimba za Yerusalemu.’+   Yehova wanena kuti,‘Popeza Isiraeli anandigalukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa.Chifukwa chakuti anagulitsa munthu wolungama kuti apeze siliva,Komanso munthu wosauka kuti apeze nsapato.+   Amapondaponda mitu ya anthu wamba pafumbi,+Ndipo amatsekereza njira ya anthu ofatsa.+ Bambo ndi mwana wake wamwamuna akugona ndi mtsikana mmodzi,Ndipo akuipitsa dzina langa loyera.   Zovala zimene alanda anthu ena monga chikole,+ amaziyala pafupi ndi guwa lililonse lansembe+ nʼkugonapo.Ndipo vinyo amene amakamwera kunyumba* za milungu yawo, amagula ndi ndalama zimene alipiritsa anthu.’   ‘Koma ine ndi amene ndinapha Aamori iwo akuona.+Aamoriwo anali aatali ngati mitengo ya mkungudza komanso amphamvu ngati mitengo ikuluikulu.Ndinawononga zipatso zawo mʼmwamba ndiponso mizu yawo pansi.+ 10  Ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo,+Ndipo ndinakuyendetsani mʼchipululu zaka 40,+Kuti mukatenge dziko la Aamori. 11  Ndinachititsa ana anu ena kukhala aneneri.+Ndipo anyamata anu ena ndinawachititsa kukhala Anaziri.+ Si choncho kodi, inu Aisiraeli?’ watero Yehova. 12  ‘Koma inu munkapatsa Anaziri vinyo kuti amwe,+Ndipo aneneri munawalamula kuti: “Musamanenere.”+ 13  Choncho ine ndidzakupondani pamalo anu,Ngati mmene ngolo imene yanyamula mitolo ya tirigu imapondera zinthu. 14  Munthu waliwiro adzasowa kothawira,+Palibe munthu wamphamvu amene adzalimbe,Komanso palibe msilikali amene adzapulumuke. 15  Munthu wokhala ndi uta sadzaima,Munthu waliwiro kwambiri sadzatha kuthawaNdipo wokwera pahatchi* sadzapulumuka. 16  Ngakhale msilikali wolimba mtima kwambiriAdzathawa ali maliseche pa tsiku limenelo,’+ watero Yehova.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Chifukwa chondigalukira katatu ndiponso ka 4.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “woweruza.”
Kapena kuti, “malangizo.”
Kapena kuti, “ku akachisi.”
Ena amati “hosi.”