Amosi 4:1-13

  • Uthenga wotsutsana ndi ngʼombe za ku Basana (1-3)

  • Yehova ananyoza kulambira kwabodza kwa Aisiraeli (4, 5)

  • Aisiraeli anakana kubwerera kwa Mulungu (6-13)

    • “Konzekera kukumana ndi Mulungu wako” (12)

    • ‘Mulungu amafotokozera munthu zimene akuganiza’ (13)

4  “Tamverani mawu awa, inu ngʼombe zazikazi za ku Basana,Amene mumakhala mʼphiri la Samariya,+Inu akazi amene mukuchitira zachinyengo anthu ovutika+ komanso kuphwanya anthu osauka.Ndipo mumauza amuna* anu kuti, ‘Tipatseni chakumwa kuti timwe!’   Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, walumbira mogwirizana ndi kuyera kwake kuti,‘“Taonani! Masiku adzafika pamene iye adzakukolani ndi ngowe zokolera nyama nʼkukunyamulani.Ndipo otsala adzawakola ndi mbedza.   Mudzatulukira pamabowo a mpanda amene muli nawo pafupi.Ndipo mudzaponyedwa kunja, ku Harimoni,” watero Yehova.’   ‘Bwerani ku Beteli anthu inu kuti mudzachite zolakwa,*+Bwerani ku Giligala kuti mudzawonjezere machimo.+ Bweretsani nsembe zanu+ mʼmawa.Ndipo pa tsiku lachitatu, mubweretse chakhumi* chanu.+   Perekani nsembe zoyamikira za mkate wokhala ndi zofufumitsa.+Ndipo lengezani mokweza za nsembe zanu zaufulu! Chifukwa nʼzimene mumakonda kuchita, inu Aisiraeli,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.   ‘Mʼmizinda yanu yonse, ine sindinakupatseni chakudya.Ndipo ndinachititsa kuti mʼnyumba zanu zonse musakhale chakudya.+Koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.   ‘Ine ndinakumanani mvula kutatsala miyezi itatu kuti mukolole.+Ndinagwetsa mvula mumzinda wina koma mumzinda wina sindinagwetse. Mvula inagwa mʼmunda umodziKoma mʼmunda wina, mmene simunagwe mvula, munauma.   Anthu amʼmizinda iwiri kapena itatu anayenda movutikira kupita mumzinda wina kuti akamwe madzi,+Ndipo ludzu lawo silinathe,Koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova.   ‘Ndinawononga mbewu zanu ndi mphepo yotentha komanso matenda a chuku.+ Munachulukitsa minda yanu ya mpesa ndi ya mbewu zina.Koma dzombe linawononga mitengo yanu ya mkuyu ndi ya maolivi,+Ndipo inu simunabwererebe kwa ine,’+ watero Yehova. 10  ‘Ndinakutumizirani mliri ngati wa ku Iguputo.+ Ndinapha anyamata anu ndi lupanga+ ndipo mahatchi anu analandidwa.+ Ndinachititsa kuti fungo lonunkha lamʼmisasa yanu lifike mʼmphuno mwanu,+Koma inu simunabwerere kwa ine,’ watero Yehova. 11  ‘Ndinakubweretserani chiwonongekoNgati chimene Mulungu anabweretsa ku Sodomu ndi Gomora.+ Ndipo inu munali ngati chikuni cholanditsidwa pamoto.Koma simunabwerere kwa ine,’+ watero Yehova. 12  Ndidzakuchitiranso zimenezo, iwe Isiraeli. Ndipo chifukwa chakuti ndidzakuchitira zimenezi,Konzekera kukumana ndi Mulungu wako, iwe Isiraeli. 13  Taona! Iye ndi amene anapanga mapiri+ ndipo analenganso mphepo,+Amafotokozera munthu zimene akuganiza,Amachititsa kuwala kwa mʼbandakucha kukhala mdima,+Ndiponso amaponda malo okwezeka a dziko lapansi.”+Dzina lake ndi Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ambuye.”
Kapena kuti, “mudzandigalukire.”
Kapena kuti “gawo limodzi mwa magawo 10.”