Amosi 5:1-27

  • Isiraeli anali ngati namwali wakugwa (1-3)

  • Funafunani Mulungu kuti mukhale ndi moyo (4-17)

    • Muzidana ndi zoipa nʼkumakonda zabwino (15)

  • Tsiku la Yehova ndi tsiku lamdima (18-27)

    • Nsembe za Aisiraeli zinakanidwa (22)

5  “Tamverani mawu awa amene ndikukuuzani monga nyimbo ya pamaliro, inu amʼnyumba ya Isiraeli:   ‘Namwali, Isiraeli, wagwa.Iye sangathenso kuimirira. Aliyense wamuthawa nʼkumusiya mʼdziko lake.Ndipo palibe womudzutsa.’  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa wanena kuti, ‘Mzinda umene unkapita kunkhondo ndi anthu 1,000, udzatsala ndi anthu 100.Ndipo mzinda umene unkapita kunkhondo ndi anthu 100, udzatsala ndi anthu 10. Zimenezi ndi zimene zidzachitikire nyumba ya Isiraeli.’+  Yehova wauza anthu a mʼnyumba ya Isiraeli kuti: ‘Ndifufuzeni kuti mupitirize kukhala ndi moyo.+   Musakhale ndi mtima wofuna kupita ku Beteli.+Ndipo musapite ku Giligala+ kapena ku Beere-seba.+Chifukwa ndithu Giligala adzapita ku ukapolo.+Ndipo Beteli adzawonongedwa.*   Funafunani Yehova kuti mupitirize kukhala ndi moyo.+Kuti asakuyakireni ngati moto panyumba ya Yosefe.Nʼkuwotcheratu Beteli popanda wozimitsa motowo.   Mumasandutsa chilungamo kukhala chitsamba chowawa.Ndipo mumataya pansi chilungamocho.+   Amene anapanga gulu la nyenyezi la Kima ndi gulu la nyenyezi la Kesili,+Amene amachititsa mdima wandiweyani kukhala kuwala kwa mʼmamawa,Amene amachititsa masana kukhala ngati mdima wausiku,+Amenenso amasonkhanitsa madzi amʼnyanjaNʼkuwakhuthulira pansi,+Dzina lake ndi Yehova.   Iye adzawononga mwamsanga munthu wamphamvu.Ndiponso adzawononga malo amene ali ndi mpanda wolimba. 10  Anthuwo amadana ndi munthu wowadzudzula pageti la mzinda,Komanso amanyansidwa ndi munthu wolankhula chilungamo.+ 11  Chifukwa chakuti mumalamula anthu osauka kuti akulipireni akabwereka munda,Ndipo mumatenga zokolola zawo ngati msonkho,+Simudzapitiriza kukhala mʼnyumba zamiyala yosema zimene mwamanga.+Ndiponso simudzamwa vinyo wochokera mʼminda yanu ya mpesa yabwino kwambiri.+ 12  Chifukwa ndikudziwa kuchuluka kwa zochita zanu zondigalukira,Ndiponso kukula kwa machimo anu.Mumachitira nkhanza munthu wolungama,Mumalandira ziphuphu,Komanso mumaphwanya ufulu wa anthu osauka pageti la mzinda.+ 13  Choncho anthu ozindikira adzakhala chete pa nthawi imeneyo,Chifukwa idzakhala nthawi yoopsa.+ 14  Yesetsani kuchita zabwino osati zoipa,+Kuti mupitirize kukhala ndi moyo.+ Mukatero Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba adzakhala nanu.Ngati mmene mwanenera kuti ali nanu.+ 15  Muzidana ndi choipa ndipo muzikonda chabwino.+Pageti la mzinda pazichitika chilungamo.+ Mwina Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwambaAdzakomera mtima mbadwa za Yosefe zotsala.’+ 16  Choncho Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, Yehova wanena kuti: ‘Padzamveka kulira mʼmabwalo onse a mizinda yanu,Ndipo mʼmisewu yanu yonse anthu azidzati: “Mayo ine! Mayo ine!” Adzaitana alimi kuti alire,Ndiponso akatswiri odziwa kulira maliro kuti alire mokweza.’ 17  ‘Padzakhala kulira mokweza mʼminda yonse ya mpesa,+Chifukwa ine ndidzadutsa pakati panu,’ watero Yehova. 18  ‘Tsoka kwa anthu amene akulakalaka tsiku la Yehova!+ Kodi chidzakuchitikireni nʼchiyani pa tsiku la Yehova?+ Limeneli lidzakhala tsiku lamdima, osati kuwala.+ 19  Zidzakhala ngati munthu amene akuthawa mkango wakumana ndi chimbalangondo,Ndipo pamene akulowa mʼnyumba nʼkugwira khoma, njoka ikumuluma. 20  Tsiku la Yehova lidzakhala lakuda, osati lowala,Lidzakhala lamdima, osati kuwala. 21  Ine ndimadana ndi zikondwerero zanu ndipo sindigwirizana nazo,+Komanso sindisangalala ndi fungo la nsembe zanu zoperekedwa pamisonkhano yanu yapadera. 22  Ngakhale mutapereka nsembe zathunthu zopsereza ndiponso nsembe zoperekedwa ngati mphatso,Ine sindidzasangalala ndi nsembe zanuzo.+Ndipo sindidzakondwera ndi nsembe zanu zamgwirizano zanyama zonenepa.+ 23  Siyani kuimba nyimbo zaphokoso,Ndipo sindikufuna kumva nyimbo zanu zoimbidwa ndi zoimbira za zingwe.+ 24  Chilungamo chiyende ngati madzi.+Ndiponso ngati mtsinje wosaphwa nthawi zonse. 25  Inu amʼnyumba ya Isiraeli,Kodi pamene munali mʼchipululu muja kwa zaka 40, munandipatsa nsembe zanyama ndi zopereka zina?+ 26  Koma inu mudzanyamula Sakuti mfumu yanu ndi Kaiwani,*Mafano amene munapanga a mulungu wanu wa nyenyezi. 27  Ndipo ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kwambiri ndi ku Damasiko,’+ watero Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, amene dzina lake ndi Yehova.”+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “adzakhala malo ochitikira zinthu zamatsenga.”
Nʼkutheka kuti milungu iwiri yonseyi ikunena za pulaneti yotchedwa Saturn, imene ankailambira ngati mulungu.