Amosi 6:1-14

  • Tsoka kwa anthu okhala mosatekeseka (1-14)

    • Mabedi aminyanga ya njovu; makapu a vinyo (4, 6)

6  “Tsoka kwa anthu amene akukhala mosatekeseka ku Ziyoni,Ndiponso anthu amene akuona kuti ndi otetezeka mʼphiri la Samariya.+Anthu olemekezeka a mtundu wotchuka kuposa mitundu ina,Amene nyumba yonse ya Isiraeli imapita kwa iwowo.   Pitani mukaone ku Kaline. Mukakachoka kumeneko mukapite ku Hamati Wamkulu,+Kenako mukapite ku Gati wa Afilisiti. Kodi mizinda imeneyi imaposa maufumu anu awiriwa?*Kapena kodi malo awo ndi aakulu kuposa malo anu?   Kodi inu simukufuna kuganizira za tsiku latsoka?+Kodi mukufuna kuti chiwawa chikhale paliponse?+   Mumagona pamabedi aminyanga ya njovu+ ndi kudziwongola pamipando yokhala ngati bedi,+Ndiponso mukudya nkhosa zamphongo komanso ana a ngʼombe* onenepa.+   Mumapeka nyimbo zoti muziimba ndi zeze,*+Ndipo mofanana ndi Davide, mumapanga zipangizo zoimbira.+   Mumamwera vinyo mʼmakapu akuluakulu,+Ndipo mumadzola mafuta apamwamba kwambiri. Komanso simukukhudzidwa* ndi tsoka lomwe linagwera Yosefe.+   Anthu amenewa adzakhala oyambirira kupita ku ukapolo,+Ndipo phwando laphokoso la anthu ogona modziwongola pamipando yokhala ngati bedi lidzatha.   Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, wanena kuti: ‘Ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndalumbira pa dzina langaʼ+ kuti,‘Ndimanyasidwa ndi kunyada kwa Yakobo,+Ndimadana ndi nsanja zake zolimba,+Ndipo ndidzapereka mzindawu ndi zinthu zake zonse kwa adani ake.+  Ngati anthu 10 angatsale mʼnyumba imodzi, nawonso adzafa. 10  Wachibale* adzabwera kudzawatulutsa nʼkuyamba kuwawotcha mmodzimmodzi. Adzatulutsa mafupa awo mʼnyumbamo, ndiyeno adzafunsa aliyense amene ali mʼzipinda zamkati kuti, “Kodi muli anthu enanso mmenemo?” Ndipo adzayankha kuti, “Mulibe!” Kenako adzamuuza kuti, “Khala chete! Chifukwa ino si nthawi yotchula dzina la Yehova.”’ 11  Chifukwa Yehova ndi amene walamula,+Iye adzagwetsa nyumba zikuluzikulu moti zidzasanduka mulu wadothi.Ndipo nyumba zingʼonozingʼono zidzasanduka zibuma.+ 12  Kodi mahatchi angathamange pathanthwe?Kapena kodi munthu angalime pathanthwe ndi ngʼombe? Chifukwa mwasintha chilungamo kukhala chomera chapoizoni,Ndipo mwasandutsa chipatso cha chilungamo kukhala chinthu chowawa.+ 13  Mumasangalala ndi zinthu zopanda pake.Ndipo mukunena kuti: ‘Tapeza mphamvu patokha.’*+ 14  Tsopano Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti ‘Inu amʼnyumba ya Isiraeli, ine ndikubweretserani mtundu wa anthu.+Ndipo udzakuponderezani kuyambira ku Lebo-hamati*+ mpaka kuchigwa* cha Araba.’”

Mawu a M'munsi

Ayenera kuti akutanthauza ufumu wa Yuda ndi wa Isiraeli.
Kapena kuti, “ana a ngʼombe amphongo.”
Kapena kuti, “zipangizo za zingwe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “simukudwala.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mchimwene wa bambo ake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Tadzitengera nyanga.”
Kapena kuti, “polowera ku Hamati.”