Amosi 7:1-17

  • Masomphenya osonyeza kuti mapeto a Aisiraeli ali pafupi (1-9)

    • Dzombe (1-3), moto (4-6), chingwe choyezera (7-9)

  • Amosi anauzidwa kuti asiye kunenera (10-17)

7  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anandionetsa masomphenya awa: Ndinamuona akutumiza dzombe, mbewu zomaliza zitayamba kumera.* Zimenezi zinali mbewu zimene ankadzala, akamaliza kumweta udzu wopita kwa mfumu.  Dzombelo litamaliza kudya zomera zonse zamʼdziko, ine ndinati: “Inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, chonde khululukani.+ Kodi Yakobo apulumuka bwanji popeza ndi wofooka?”+  Choncho Yehova anaiganiziranso nkhaniyi+ ndipo Yehova anati, “Zimenezi sizidzachitika.”  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anandionetsanso masomphenya awa: Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, analamula kuti dziko lilangidwe ndi moto. Motowo unaumitsa madzi akuya ndiponso unawononga kachigawo ka dziko.  Ndiyeno ine ndinati: “Inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, chonde musatero.+ Kodi Yakobo apulumuka bwanji popeza ndi wofooka?”+  Choncho Yehova anaiganiziranso nkhaniyi+ ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, anati, “Zimenezinso sizidzachitika.”  Iye anandionetsanso masomphenya awa: Yehova anaima pamwamba pa khoma limene linamangidwa pogwiritsa ntchito chingwe chowongolera, ndipo anali ndi chingwe chowongolera mʼmanja mwake.  Ndiyeno Yehova anandifunsa kuti: “Kodi ukuona chiyani Amosi?” Ndinamuyankha kuti: “Ndikuona chingwe chowongolera.” Ndiyeno Yehova anati: “Ndikuika chingwe chowongolera pakati pa anthu anga Aisiraeli, ndipo sindidzawakhululukiranso.+  Malo okwezeka a Isaki+ adzawonongedwa, ndipo malo opatulika a Isiraeli adzasakazidwa.+ Ine ndidzabwera kudzawononga nyumba ya Yerobowamu ndi lupanga.”+ 10  Ndiyeno Amaziya wansembe wa ku Beteli,+ anatumiza uthenga kwa Yerobowamu+ mfumu ya Isiraeli wakuti: “Amosi akukukonzerani chiwembu mkati mwenimweni mwa Isiraeli,+ ndipo anthu atopa nawo mawu ake.+ 11  Amosi akunena kuti, ‘Yerobowamu adzaphedwa ndi lupanga ndipo ndithu Isiraeli adzagwidwa mʼdziko lake nʼkutengedwa kupita ku ukapolo.’”+ 12  Ndiyeno Amaziya anauza Amosi kuti: “Iwe wamasomphenya, choka, pita kudziko la Yuda. Uzikapeza chakudya* chako kumeneko ndiponso uzikanenera.+ 13  Koma usapitirize kunenera ku Beteli kuno,+ chifukwa ndi malo opatulika a mfumu+ ndiponso nyumba ya ufumuwu.” 14  Amosi anayankha Amaziya kuti: “Ine sindinali mneneri kapena mwana wa mneneri, koma ndinali mʼbusa+ ndiponso wosamalira* nkhuyu. 15  Koma Yehova ananditenga kumene ndinkaweta nkhosa ndipo Yehova anandiuza kuti, ‘Pita ukanenere kwa anthu anga Aisiraeli.’+ 16  Tsopano imva zimene Yehova wanena, ‘Ukunena kuti: “Usanenere zinthu zoipa zokhudza Isiraeli,+ ndipo usanene mawu alionse+ oipa okhudza nyumba ya Isaki.” 17  Ndiyetu Yehova wanena kuti: “Mkazi wako adzakhala hule mumzindawu. Ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa ndi lupanga. Anthu adzagawana dziko lako mochita kuyeza ndi chingwe, ndipo iweyo udzafera mʼdziko lodetsedwa. Isiraeli adzagwidwa ndithu mʼdziko lake nʼkutengedwa kupita ku ukapolo.”’”+

Mawu a M'munsi

Umenewu unali mwezi wa January ndi February.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Uzikadya mkate.”
Kapena kuti, “woboola.”