Kalata Yopita kwa Aroma 11:1-36

  • Si Aisiraeli onse amene anakanidwa (1-16)

  • Fanizo la mtengo wa maolivi (17-32)

  • Nzeru za Yehova nʼzozama (33-36)

11  Ndiye ndifunse kuti, kodi Mulungu anakana anthu ake?+ Ayi ndithu. Paja inenso ndine mmodzi wa Aisiraeli, mbadwa* ya Abulahamu, wa fuko la Benjamini.  Mulungu sanakane anthu ake amene anali oyambirira kuwavomereza.+ Kodi simukudziwa zimene lemba lina limanena zokhudza Eliya, pamene anachonderera Mulungu motsutsa Aisiraeli? Limati:  “Yehova,* iwo apha aneneri anu ndipo agwetsa maguwa anu ansembe moti ine ndatsala ndekhandekha. Tsopano ayambanso kundifunafuna kuti andiphe.”+  Koma kodi Mulungu anamuuza kuti chiyani? Anamuuza kuti: “Ine ndasiya anthu 7,000 amene mawondo awo sanagwadirepo Baala.”+  Choncho, pa nthawi inonso alipo ena ochepa amene anasankhidwa+ mwa kukoma mtima kwakukulu.  Ndiyetu ngati anasankhidwa mwa kukoma mtima kwakukulu,+ sanasankhidwe chifukwa cha ntchito zawo ayi.+ Zitati zitero, kukoma mtima kumeneko sikungakhalenso kukoma mtima kwakukulu.  Ndiye zili bwanji pamenepa? Chimene Aisiraeli akuchifunitsitsa sanachipeze, koma anthu osankhidwa ndi amene anachipeza.+ Enawo anaumitsa mitima yawo+  ngati mmene Malemba amanenera kuti: “Mulungu wawapatsa mzimu wa tulo tofa nato,+ maso osaona ndi makutu osamva, mpaka lero.”+  Ndiponso Davide anati: “Tebulo lawo likhale khwekhwe, msampha, chopunthwitsa ndi chilango kwa iwo. 10  Maso awo achite mdima kuti asaone, ndipo weramitsani misana yawo nthawi zonse.”+ 11  Ndiyeno ndifunse kuti, kodi anapunthwa mpaka kugweratu? Ayi. Koma chifukwa cha kulakwa kwawo anthu a mitundu ina apeza chipulumutso, ndipo zimenezi zachititsa kuti olakwawo achite nsanje.+ 12  Kulakwa kwawo kwabweretsa chuma mʼdziko ndipo kuchepa kwawo kukutanthauza chuma kwa anthu a mitundu ina.+ Choncho padzakhala madalitso ambiri chiwerengero chawo chikadzakwanira. 13  Tsopano ndikulankhula ndi inu anthu a mitundu ina. Popeza ndine mtumwi wotumidwa kwa anthu a mitundu ina,+ ndimalemekeza utumiki wanga,+ 14  kuti mwina ndingapangitse anthu a mtundu wanga kuchita nsanje nʼkupulumutsapo ena a iwo. 15  Chifukwatu ngati dziko lagwirizanitsidwa ndi Mulungu chifukwa chakuti iwo anatayidwa,+ ndiye kuti akadzalandiridwa zidzakhala ngati awaukitsa. 16  Ndiponso, ngati mbali ya mtanda wa mkate imene yaperekedwa nsembe ngati chipatso choyambirira ili yoyera, ndiye kuti mtanda wonse ndi woyeranso. Ndipo ngati muzu uli woyera, ndiye kuti nthambinso ndi zoyera. 17  Ngati nthambi zina zinadulidwa, ndipo iwe ngakhale kuti ndiwe nthambi ya mtengo wa maolivi wamʼtchire, unalumikizidwa pakati pa nthambi zotsala ndipo unayamba kupeza zonse zofunika kuchokera ku muzu wamtengo wa maoliviwo, 18  usayambe kukulira mtima nthambi zimene zinadulidwazo. Koma ngati ukuzikulira mtima+ kumbukira kuti si iwe amene ukunyamula muzu, koma muzu ndi umene ukukunyamula iweyo. 19  Mwina ukunena kuti: “Anadula nthambi zina kuti alumikizepo ineyo.”+ 20  Zimenezo nʼzoona. Iwo anadulidwa chifukwa analibe chikhulupiriro,+ koma iweyo udakali wolumikizidwa kumtengowo chifukwa cha chikhulupiriro.+ Chotsa maganizo odzikuzawo, koma khala ndi mantha. 21  Chifukwa ngati Mulungu sanalekerere nthambi zachilengedwe, sadzakulekereranso iweyo. 22  Uziganizira kukoma mtima komanso kusalekerera kwa Mulungu.+ Amene anagwa anasonyezedwa kusalekerera,+ koma iweyo unasonyezedwa kukoma mtima kwa Mulungu. Bola ukhalebe woyenera kusonyezedwa kukoma mtima kwake. Apo ayi, iwenso udzadulidwa. 23  Iwonso ngati angayambe kukhala ndi chikhulupiriro, adzalumikizidwa kumtengowo,+ chifukwa Mulungu akhoza kuwalumikizanso. 24  Ngati iweyo unadulidwa kumtengo wa maolivi umene mwachilengedwe umamera mʼtchire, ndipo mosemphana ndi chilengedwe unalumikizidwa kumtengo wa maolivi wolimidwa, kodi si chapafupi kulumikiza nthambizi kumtengo wawo umene zinadulidwako? 25  Chifukwa sindikufuna kuti mukhale osadziwa abale za chinsinsi chopatulika chimenechi,+ kuopera kuti mungadzione ngati anzeru. Chinsinsicho nʼchakuti ena mu Isiraeli aumitsa mitima yawo mpaka chiwerengero chonse cha anthu ochokera mʼmitundu ina chitakwanira. 26  Aisiraeli onse adzapulumutsidwa mwa njira imeneyi+ mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Mpulumutsi adzachokera mʼZiyoni+ ndipo adzachotsera Yakobo zochita zonse zosalemekeza Mulungu. 27  Limeneli ndi pangano limene ndidzachite nawo+ ndikadzawachotsera machimo awo.”+ 28  Nʼzoona kuti iwo ndi adani a uthenga wabwino ndipo zimenezi zakuthandizani inuyo. Koma Mulungu anawasankha ndipo amawakonda chifukwa cha makolo awo akale.+ 29  Mulungu sadzanongʼoneza bondo chifukwa cha mphatso zake ndiponso chifukwa chakuti anawaitana. 30  Inuyo munali osamvera Mulungu,+ koma tsopano mwasonyezedwa chifundo+ chifukwa cha kusamvera kwawo.+ 31  Iwowa tsopano ndi osamvera ndipo Mulungu wakusonyezani chifundo. Koma akhoza kuwasonyezanso chifundo ngati mmene anachitira ndi inuyo. 32  Mulungu walola onse kuti akhale akaidi a kusamvera+ kuti onsewo awasonyeze chifundo.+ 33  Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake nʼzozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri. Ziweruzo zake ndi zovuta kuzimvetsa, ndipo ndani angatulukire njira zake? 34  “Ndani akudziwa maganizo a Yehova,* kapena ndani angakhale mlangizi wake?”+ 35  Kapenanso “ndani anayambirira kumupatsa kanthu, kuti amubwezere?”+ 36  Chifukwa zinthu zonse zimachokera kwa iye, ndi iyeyo amene anazipanga ndiponso ndi zake. Ulemerero ukhale wake mpaka kalekale. Ame.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”