Kalata Yopita kwa Aroma 16:1-27

  • Paulo anauza anthu za Febe yemwe ankatumikira mumpingo (1, 2)

  • Moni wopita kwa Akhristu a ku Roma (3-16)

  • Anachenjeza za kugawikana (17-20)

  • Moni wochokera kwa anzake a Paulo (21-24)

  • Chinsinsi chopatulika tsopano chadziwika (25-27)

16  Ndikufuna kukudziwitsani za mlongo wathu Febe, amene akutumikira mumpingo wa ku Kenkereya.+  Mulandireni mwa Ambuye mmene mumalandirira oyerawo ndiponso kumupatsa thandizo lililonse limene angafunikire.+ Chifukwa iyenso anateteza abale ambiri, kuphatikizapo ineyo.  Mundiperekere moni kwa Purisika ndi Akula,+ antchito anzanga potumikira Khristu Yesu.  Iwo anaika miyoyo yawo pachiswe chifukwa cha ine,+ ndipo si ine ndekha amene ndikuwayamikira, komanso mipingo yonse ya anthu a mitundu ina.  Ndikuperekanso moni ku mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwawo.+ Moni kwa wokondedwa wanga Epeneto, amene ndi chipatso choyambirira cha Khristu ku Asia.  Moni kwa Mariya, amene wachita zinthu zambiri pokuthandizani.  Moni kwa Anduroniko ndi Yuniya, omwe ndi achibale anga+ komanso akaidi anzanga. Amenewa ndi amuna odziwika kwambiri kwa atumwi ndiponso akhala ogwirizana ndi Khristu kwa nthawi yaitali kuposa ineyo.  Mundiperekere moni kwa Ampiliato, wokondedwa wanga mwa Ambuye.  Moni kwa Uribano wantchito mnzathu mwa Khristu ndiponso wokondedwa wanga Sitaku. 10  Moni kwa Apele, wokhulupirika mwa Khristu. Moni kwa anthu a mʼbanja la Arisitobulo. 11  Moni kwa wachibale wanga Herodiona. Moni kwa anthu a mʼbanja la Narikiso omwe ndi otsatira a Ambuye. 12  Moni kwa Turufena ndi Turufosa, azimayi ogwira ntchito mwakhama potumikira Ambuye. Moni kwa Peresida, wokondedwa wathu. Mayi ameneyu wagwira ntchito mwakhama potumikira Ambuye. 13  Moni kwa Rufu, wosankhidwa mwa Ambuye. Moninso kwa mayi ake amenenso ndi mayi anga. 14  Moni kwa Asunkirito, Felego, Heme, Pateroba, Heremase ndiponso abale amene ali nawo limodzi. 15  Moni kwa Filologo ndi Yuliya, Nerea ndi mchemwali wake komanso Olumpa ndi oyera onse amene ali nawo limodzi. 16  Mupatsane moni mwachikondi. Mipingo yonse ya Khristu ikupereka moni. 17  Tsopano ndikukulimbikitsani abale, kuti musamale ndi amene amagawanitsa anthu ndiponso kuchita zinthu zokhumudwitsa ena. Zimenezi ndi zosemphana ndi zimene munaphunzira, choncho muziwapewa.+ 18  Chifukwa anthu oterowo si akapolo a Ambuye wathu Khristu, koma a mimba zawo. Ndipo amagwiritsa ntchito mawu okopa ndiponso achinyengo kuti apusitse anthu oona mtima. 19  Anthu onse akudziwa kuti ndinu omvera ndipo ndikusangalala nanu chifukwa cha zimenezi. Koma ndikufuna kuti mukhale anzeru pa zinthu zabwino koma osadziwa kanthu pa zinthu zoipa.+ 20  Mulungu amene amapereka mtendere aphwanya Satana+ pansi pa mapazi anu posachedwapa. Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu kukhale nanu. 21  Wantchito mnzanga Timoteyo akupereka moni, chimodzimodzinso Lukiyo, Yasoni ndi Sosipato omwe ndi achibale anga.+ 22  Ineyo Teritio, amene ndalemba kalatayi, ndikuti moni mwa Ambuye. 23  Gayo,+ amene ndikukhala kunyumba kwawo amenenso mpingo umasonkhana kunyumba kwawo, akupereka moni. Nayenso Erasito woyangʼanira mzinda, ndi Kwarito mchimwene wake akupereka moni. 24 *⁠—— 25  Mulungu angakulimbitseni pogwiritsa ntchito uthenga wabwino umene ndikulengeza ndiponso uthenga wonena za Yesu Khristu umene ukulalikidwa. Uthengawu ndi wogwirizana ndi zimene zaululidwa zokhudza chinsinsi chopatulika+ chimene chakhala chobisika kwa nthawi yaitali. 26  Koma tsopano chinsinsi chimenechi chaululidwa ndipo anthu a mitundu yonse achidziwa kudzera mʼMalemba aulosi. Zimenezi nʼzogwirizana ndi lamulo la Mulungu wamuyaya. Cholinga chake nʼchakuti anthu a mitundu yonse azimumvera mwa chikhulupiriro. 27  Kwa Mulungu wanzeru yekhayo,+ kukhale ulemerero mpaka kalekale kudzera mwa Yesu Khristu. Ame.

Mawu a M'munsi