Kalata Yopita kwa Aroma 4:1-25
4 Popeza zili choncho, kodi tinene chiyani za kholo lathu Abulahamu?
2 Mwachitsanzo, zikanakhala kuti Abulahamu ankaonedwa kuti ndi wolungama chifukwa cha zimene anachita, akanakhala ndi chifukwa chodzitamira, koma osati pamaso pa Mulungu.
3 Kodi paja Malemba amati chiyani? Amati: “Abulahamu anakhulupirira zimene Yehova* anamuuza, ndipo anaonedwa kuti ndi wolungama.”+
4 Munthu amene wagwira ntchito saona malipiro ake ngati kukoma mtima kwakukulu, koma ngati zimene amayenera kulandira.*
5 Koma Mulungu amene amaona anthu ochimwa kukhala olungama amaona kuti munthu yemwe sanagwire ntchito, koma amamukhulupirira, ndi wolungama.+
6 Davide ananena za munthu wosangalala amene Mulungu amamuona kuti ndi wolungama ngakhale kuti zimene wachita sizikugwirizana kwenikweni ndi Chilamulo. Iye anati:
7 “Osangalala ndi anthu amene akhululukidwa zochita zawo zosamvera malamulo ndipo machimo awo akhululukidwa.*
8 Wosangalala ndi munthu amene Yehova* sadzawerengera tchimo lake.”+
9 Ndiye kodi anthu odulidwa okha ndi amene amakhala osangalala choncho? Kapena osadulidwa nawonso amakhala osangalala?+ Popeza timati: “Abulahamu anaonedwa kuti ndi wolungama chifukwa cha chikhulupiriro chake.”+
10 Koma kodi iye anali wotani pamene anaonedwa kuti ndi wolungama? Kodi anali wodulidwa kapena wosadulidwa? Iyetu anali asanadulidwe.
11 Ndipo Mulungu anapatsa Abulahamu mdulidwe ngati chizindikiro+ chosonyeza kuti Mulungu anamuona kuti ndi wolungama asanadulidwe chifukwa cha chikhulupiriro. Anachita zimenezi kuti adzakhale bambo wa onse osadulidwa amene ali ndi chikhulupiriro,+ kuti anthuwo adzaonedwe kuti ndi olungama.
12 Kuti adzakhalenso bambo wa ana odulidwa, osati odulidwa okhawo, komanso wa amene amayenda moyenera potsatira chikhulupiriro chimene bambo wathu Abulahamu+ anali nacho asanadulidwe.
13 Chifukwa Abulahamu kapena mbadwa* zake sanalonjezedwe kuti adzalandira dziko monga cholowa chawo chifukwa cha Chilamulo ayi.+ Analandira lonjezolo chifukwa chakuti Abulahamu anali ndi chikhulupiriro ndipo Mulungu anamuona kuti ndi wolungama.+
14 Chifukwa ngati anthu amene akutsatirabe Chilamulo ndi amene adzalandire cholowacho, ndiye kuti chikhulupiriro chilibenso ntchito ndipo lonjezo lija lathetsedwa.
15 Zoona zake nʼzakuti, kuphwanya Chilamulo kumachititsa kuti munthu alandire chilango,+ koma pamene palibe lamulo, palibenso kulakwa.+
16 Nʼchifukwa chake iye anapatsidwa lonjezolo chifukwa cha chikhulupiriro, kuti likhale logwirizana ndi kukoma mtima kwakukulu.+ Komanso anapatsidwa lonjezolo kuti likhale lotsimikizika kwa anthu onse omwe ndi mbadwa* zake,+ osati otsatira Chilamulo okha, komanso otsatira chikhulupiriro cha Abulahamu yemwe ndi bambo wa tonsefe.+
17 (Zimenezi nʼzogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Ndakusankha kuti ukhale bambo wa mitundu yambiri.”)+ Izi zinali choncho pamaso pa Mulungu amene Abulahamu ankamukhulupirira, yemwenso amaukitsa akufa ndipo amanena za zinthu zimene palibe ngati kuti zilipo.
18 Abulahamu anali ndi chiyembekezo ndiponso chikhulupiriro chakuti adzakhala bambo wa mitundu yambiri, ngakhale kuti zimenezi zinkaoneka kuti nʼzosatheka. Anakhulupirira zimenezi mogwirizana ndi zimene zinanenedwa kuti: “Umu ndi mmene mbadwa* zako zidzakhalire.”+
19 Ndiponso, ngakhale kuti chikhulupiriro chake sichinafooke, ankaganizira za thupi lake, limene pa nthawiyo linali ngati lakufa (popeza anali ndi zaka pafupifupi 100).+ Ankadziwanso kuti Sara ndi wokalamba kwambiri ndipo sangabereke mwana.+
20 Koma chifukwa cha lonjezo la Mulungu, chikhulupiriro chake sichinagwedezeke ndipo chikhulupiriro chakecho chinamupatsa mphamvu moti anapereka ulemerero kwa Mulungu.
21 Iye sankakayikira kuti zimene Mulungu analonjeza anali ndi mphamvu yozichita.+
22 Choncho “Mulungu anamuona kuti ndi wolungama.”+
23 Komabe, mawu akuti “Mulungu anamuona kuti ndi wolungama” sanalembere iye yekha.+
24 Analemberanso ifeyo. Nafenso timaonedwa kuti ndife olungama chifukwa timakhulupirira Mulungu amene anaukitsa Yesu Ambuye wathu.+
25 Yesu anaperekedwa chifukwa cha machimo athu+ ndipo anaukitsidwa kuti tionedwe olungama.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “ngati ngongole.”
^ Kapena kuti, “aphimbidwa.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”