Kalata Yopita kwa Aroma 9:1-33

  • Paulo ankamvera chisoni Aisiraeli (1-5)

  • Mbadwa zenizeni za Abulahamu (6-13)

  • Palibe angatsutse zimene Mulungu wasankha (14-26)

    • Ziwiya za mkwiyo ndiponso ziwiya za chifundo (22, 23)

  • Anthu ochepa okha ndi amene adzapulumuke (27-29)

  • Aisiraeli anapunthwa (30-33)

9  Ndikunena zoona mogwirizana ndi Khristu, sindikunama ayi. Ndipo chikumbumtima changa chikundichitira umboni mwa mzimu woyera,  kuti ndikumva chisoni kwambiri ndipo mtima umandipweteka nthawi zonse.  Ndikanakonda kuti ineyo ndisiyanitsidwe ndi Khristu ngati wotembereredwa mʼmalo mwa abale anga, anthu a mtundu wanga,  omwe ndi Aisiraeli. Mulungu anawatenga kuti akhale ana ake+ ndipo anawapatsa ulemerero, mapangano,+ Chilamulo,+ utumiki wopatulika+ komanso malonjezo.+  Iwo ndi ana a makolo athu akale.+ Komanso Khristu anabadwa ngati munthu kuchokera kwa iwo.+ Mulungu, yemwe ndi wamkulu pa zinthu zonse, atamandike mpaka kalekale. Ame.  Komabe sizikutanthauza kuti mawu a Mulungu sanakwaniritsidwe. Chifukwa si onse omwe ndi mbadwa za Aisiraeli amene alidi “Aisiraeli.”+  Ndiponso sikuti onse ndi ana chifukwa choti ndi mbadwa* za Abulahamu.+ Koma Malemba amati, “Mbadwa* zimene ndinakulonjeza zidzachokera mwa Isaki.”+  Izi zikutanthauza kuti si ana akuthupi amene alidi ana a Mulungu,+ koma ana obadwa mogwirizana ndi lonjezo+ ndi amene amatengedwa kuti ndi mbadwa.*  Popeza lonjezo lija linati: “Ndidzabweranso nthawi ngati yomwe ino, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”+ 10  Lonjezolo silinaperekedwe pa nthawi iyi yokha. Linaperekedwanso pamene Rabeka ankayembekezera kubereka ana amapasa a Isaki kholo lathu lija.+ 11  Mapasawo asanabadwe ndiponso asanachite chabwino kapena choipa chilichonse, Mulungu anasonyeza kuti cholinga chake chidzadalira iye amene amaitana, osati zochita za munthu. 12  Choncho anauza Rabeka kuti: “Wamkulu adzakhala kapolo wa wamngʼono.”+ 13  Mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Ndinakonda Yakobo, koma Esau ndinadana naye.”+ 14  Ndiye tinene kuti chiyani pamenepa? Kodi Mulungu alibe chilungamo? Ayi ndithu.+ 15  Chifukwa iye anauza Mose kuti: “Amene ndikufuna kumukomera mtima ndidzamukomera mtima, ndipo amene ndikufuna kumusonyeza chifundo, ndidzamusonyeza chifundo.”+ 16  Choncho sizidalira kufuna kwa munthu kapena khama lake,* koma Mulungu amene ndi wachifundo.+ 17  Ponena za Farao, lemba lina linati: “Ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga komanso kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.”+ 18  Choncho iye amachitira chifundo munthu amene wafuna kumuchitira chifundo, koma amalola anthu ena kuti aumitse mitima yawo.+ 19  Mwina ungandiuze kuti: “Nʼchifukwa chiyani Mulungu akupezerabe anthu zifukwa? Kodi ndani akutsutsa chifuniro chake?” 20  Munthu iwe, ndiwe ndani kuti uziyankhana ndi Mulungu?+ Kodi chinthu choumbidwa chingauze munthu amene anachiumba kuti, “Unandipangiranji chonchi?”+ 21  Kodi simukudziwa kuti woumba mbiya ali ndi ufulu woumba+ chinthu china cha ntchito yolemekezeka, china cha ntchito yonyozeka kuchokera pa dongo limodzi? 22  Ndiye bwanji ngati Mulungu anafuna kusonyeza mkwiyo wake kuti mphamvu zake zidziwike ndipo analekerera moleza mtima kwambiri anthu oyenera kuwonongedwa amene anamukwiyitsa?* 23  Ndiponso bwanji ngati anachita zimenezo kuti asonyeze kukula kwa ulemerero wake kwa anthu oyenera kuwachitira chifundo,*+ omwe anawakonzeratu kuti alandire ulemerero, 24  ndipo anthu ake ndi ifeyo amene anatiitana osati kuchokera kwa Ayuda okha komanso ku mitundu ina?+ 25  Ndi zofanananso ndi zimene ananena mʼbuku la Hoseya kuti: “Anthu amene si anthu anga+ ndidzawatchula kuti ‘anthu anga,’ ndipo mkazi amene sankakondedwa ndidzamutchula kuti ‘wokondedwa.’+ 26  Kumene ankauzidwa kuti, ‘Siinu anthu anga,’ adzauzidwa kuti, ‘Ndinu ana a Mulungu wamoyo.’”+ 27  Komanso, Yesaya analengeza zokhudza Isiraeli kuti: “Ngakhale kuti ana a Isiraeli adzakhala ambiri ngati mchenga wakunyanja, ochepa okha ndi amene adzapulumuke.+ 28  Chifukwa Yehova* adzaweruza milandu padziko lapansi nʼkuimaliza mwamsanga.”+ 29  Ndiponso mogwirizana ndi zimene Yesaya ananeneratu, “Yehova* wa magulu ankhondo akumwamba akanapanda kutisiyira mbadwa,* tikanakhala ngati Sodomu, ndipo tikanafanana ndi Gomora.”+ 30  Ndiye pamenepa tinene kuti chiyani? Ngakhale kuti anthu a mitundu ina sanatsatire chilungamo,+ iwo anapeza chilungamo chimene chimabwera chifukwa cha chikhulupiriro.+ 31  Koma ngakhale kuti Aisiraeli ankatsatira lamulo la chilungamo, sanakwanitse kutsatira lamulolo. 32  Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti ankaganiza kuti angalitsatire mʼzochita zawo, osati mwa chikhulupiriro. Iwo anapunthwa “pamwala wopunthwitsa”+ 33  mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Inetu ndikuika mwala+ wopunthwitsa ndiponso thanthwe lokhumudwitsa mu Ziyoni, koma munthu wokhulupirira mwalawo sadzakhumudwa.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene akuthamanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ziwiya za mkwiyo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ziwiya za chifundo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”