Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira 10:1-11

  • Mngelo wamphamvu amene anali ndi mpukutu waungʼono (1-7)

    • “Nthawi yodikira yatha” (6)

    • Chinsinsi chopatulika chidzakwaniritsidwa (7)

  • Yohane anadya mpukutu waungʼono (8-11)

10  Kenako ndinaona mngelo wina wamphamvu akutsika kuchokera kumwamba ndipo anali atavala mtambo.* Kumutu kwake kunali utawaleza ndipo nkhope yake inali ngati dzuwa.+ Miyendo yake inali* ngati zipilala zamoto. 2  Mʼdzanja lake, anali ndi mpukutu waungʼono wotambasula. Iye anaponda panyanja ndi phazi lake lakumanja koma ndi phazi lake lakumanzere anaponda pamtunda. 3  Kenako anafuula ndi mawu okweza ngati kubangula kwa mkango.+ Atafuula choncho, panamveka mawu a mabingu 7.+ 4  Ndiye mabingu 7 aja atalankhula, ndinkafuna kulemba. Koma ndinamva mawu ochokera kumwamba+ akuti: “Usunge mwachinsinsi* zimene mabingu 7 amenewa alankhula ndipo usazilembe.” 5  Mngelo amene ndinamuona ataimirira panyanja ndi pamtunda uja, anakweza dzanja lake lamanja kumwamba. 6  Iye analumbira mʼdzina la Mulungu amene adzakhale ndi moyo mpaka kalekale,+ amene analenga kumwamba ndi zinthu zonse zimene zili kumeneko, dziko lapansi ndi zinthu zonse zimene zili mmenemo komanso nyanja ndi zinthu zonse zimene zili mmenemo.+ Analumbira kuti: “Nthawi yodikira yatha. 7  Masiku oti mngelo wa 7+ alize lipenga akadzatsala pangʼono kukwana,+ chinsinsi chopatulika+ chimene Mulungu analengeza kwa akapolo ake aneneri,+ monga uthenga wabwino, chidzakwaniritsidwa ndithu.” 8  Kenako ndinamva mawu kuchokera kumwamba+ akulankhulanso ndi ine kuti: “Pita, katenge mpukutu wotambasula umene uli mʼdzanja la mngelo amene waima panyanja ndi pamtunda uja.”+ 9  Choncho ndinapita kwa mngeloyo nʼkumuuza kuti andipatse mpukutu waungʼonowo. Iye anandiuza kuti: “Tenga mpukutuwu udye.+ Ukupweteketsa mʼmimba, koma mʼkamwa mwako ukhala wokoma ngati uchi.” 10  Ndinatengadi mpukutu waungʼonowo mʼdzanja la mngeloyo nʼkuudya.+ Mʼkamwa mwanga unkakoma ngati uchi,+ koma nditaudya mʼmimba mwanga munayamba kupweteka. 11  Ndiye ndinauzidwa kuti: “Uyenera kuneneranso zokhudza mitundu ya anthu, mayiko, zilankhulo ndi mafumu ambiri.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “anali atakutidwa ndi mtambo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mapazi ake anali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Utsekere.”