Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira 11:1-19

  • Mboni ziwiri (1-13)

    • Zinanenera kwa masiku 1,260 zitavala ziguduli (3)

    • Zinaphedwa koma sizinaikidwe mʼmanda (7-10)

    • Zinakhalanso ndi moyo patatha masiku atatu ndi hafu (11, 12)

  • Tsoka lachiwiri lapita, tsoka lachitatu likubwera (14)

  • Lipenga la 7 (15-19)

    • Ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake (15)

    • Amene akuwononga dziko lapansi adzawonongedwa (18)

11  Ndiyeno ndinapatsidwa bango lokhala ngati ndodo*+ ndipo ndinauzidwa kuti: “Pita ukayeze nyumba yopatulika yapakachisi wa Mulungu, guwa lansembe ndi amene akulambira mmenemo.  Koma bwalo limene lili kunja kwa nyumba yopatulika yapakachisi ulisiye, usaliyeze chifukwa laperekedwa kwa anthu a mitundu ina. Ndipo iwo adzapondaponda mzinda woyera+ kwa miyezi 42.+  Ndiyeno ndidzachititsa kuti mboni zanga ziwiri zinenere kwa masiku 1,260, zitavala ziguduli.”  Mboni zimenezi zikuimiridwa ndi mitengo iwiri ya maolivi+ komanso zoikapo nyale ziwiri+ ndipo zaimirira pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.+  Ngati wina aliyense akufuna kuzivulaza, moto umatuluka mʼkamwa mwawo nʼkupsereza adani awo. Ngati wina angafune kuzivulaza, ayenera kuphedwa mwanjira imeneyi.  Mboni zimenezi zili ndi mphamvu yotseka kumwamba+ kuti mvula isagwe+ mʼmasiku onse amene zikunenera. Zilinso ndi mphamvu yosandutsa madzi kuti akhale magazi+ komanso yobweretsa mliri wamtundu uliwonse padziko lapansi maulendo ambirimbiri mmene zikufunira.  Zikamaliza kuchitira umboni wawo, chilombo chimene chatuluka muphompho chidzachita nazo nkhondo ndipo chidzagonjetsa mbonizo nʼkuzipha.+  Mitembo yawo idzagona pamsewu waukulu wamumzinda waukulu, umene mophiphiritsa ukutchedwa Sodomu ndi Iguputo, kumenenso Ambuye wawo anaphedwa powapachika pamtengo.  Mitundu ya anthu yambiri, mafuko, zilankhulo ndi mayiko, adzayangʼanitsitsa mitembo yawo masiku atatu ndi hafu+ ndipo sadzalola kuti mitemboyo iikidwe mʼmanda. 10  Amene akukhala padziko lapansi adzasangalala ndi kukondwera chifukwa cha imfa yawoyo. Iwo adzatumizirana mphatso chifukwa aneneri awiriwa anazunza amene akukhala padziko lapansi. 11  Masiku atatu ndi hafu aja atatha, mzimu wa moyo wochokera kwa Mulungu unalowa mwa mboni zija.+ Ndiyeno mbonizo zinaimirira ndipo amene anaziona anagwidwa ndi mantha aakulu. 12  Kenako mbonizo zinamva mawu ofuula kuchokera kumwamba akuziuza kuti: “Bwerani kuno.” Ndipo zinakwera kumwamba mumtambo adani awo akuona. 13  Mu ola limenelo, kunachitika chivomerezi chachikulu ndipo gawo limodzi mwa magawo 10 a mzindawo linagwa. Anthu 7,000 anaphedwa ndi chivomerezicho ndipo ena onse anachita mantha nʼkupereka ulemerero kwa Mulungu wakumwamba. 14  Tsoka lachiwiri+ lapita. Koma tsoka lachitatu likubwera mofulumira. 15  Mngelo wa 7 analiza lipenga lake.+ Ndiyeno kumwamba kunamveka mawu osiyanasiyana akunena mokweza kuti: “Ufumu wa dziko wakhala Ufumu wa Ambuye wathu+ ndi wa Khristu wake+ ndipo iye adzalamulira monga mfumu mpaka kalekale.”+ 16  Ndipo akulu 24+ amene anali atakhala pamipando yawo yachifumu pamaso pa Mulungu aja, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi ndipo analambira Mulungu. 17  Iwo ankanena kuti: “Tikukuthokozani inu Yehova,* Mulungu Wamphamvuyonse, inu amene mulipo+ ndi amene munalipo, chifukwa mwatenga mphamvu zanu zazikulu nʼkuyamba kulamulira monga mfumu.+ 18  Koma mitundu ya anthu inakwiya ndipo inunso munasonyeza mkwiyo wanu. Ndiye nthawi yoikidwiratu inafika yoti akufa aweruzidwe nʼkupereka mphoto+ kwa akapolo anu aneneri+ komanso kwa oyera ndi amene akuopa dzina lanu, olemekezeka ndi onyozeka omwe. Komanso nthawi yoti muwononge amene akuwononga dziko lapansi.”+ 19  Nyumba yopatulika yapakachisi wa Mulungu kumwamba inatsegulidwa ndipo likasa la pangano lake linaonekera lili mʼnyumba yake yopatulika yapakachisi.+ Ndiyeno kunachitika mphezi, kunamveka mawu, kunagunda mabingu, kunachita chivomerezi ndipo kunagwa matalala ambiri.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ndodo yoyezera.”