Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira 13:1-18

  • Chilombo cha mitu 7 chinatuluka mʼnyanja (1-10)

  • Chilombo cha nyanga ziwiri chinatuluka pansi (11-13)

  • Chifaniziro cha chilombo cha mitu 7 (14, 15)

  • Chizindikiro komanso nambala ya chilombo (16-18)

13  Ndiyeno chinjokacho chinangoima pamchenga wamʼmbali mwa nyanja. Kenako ndinaona chilombo+ chikutuluka mʼnyanja.+ Chinali ndi nyanga 10 ndi mitu 7. Panyanga yake iliyonse panali chisoti chachifumu. Koma pamitu yake panali mayina onyoza Mulungu.  Chilombo chimene ndinaonacho chinali ngati kambuku koma mapazi ake anali ngati a chimbalangondo ndipo pakamwa pake panali ngati pa mkango. Chinjoka chija+ chinapatsa chilombocho mphamvu yake, mpando wake wachifumu komanso ulamuliro waukulu.+  Ndinaona kuti mutu wake umodzi unkaoneka kuti unali utavulazidwa kwambiri. Koma balalo linapola+ ngakhale kuti chikanatha kufa nalo ndipo dziko lonse lapansi linatsatira chilombocho chifukwa chochita nacho chidwi.  Iwo analambira chinjoka chija chifukwa chinapereka ulamuliro kwa chilombo. Ndipo analambira chilombocho ndi mawu akuti: “Ndi ndani ali ngati chilombo ndipo ndi ndani angamenyane nacho?”  Chilombocho chinapatsidwa pakamwa polankhula zinthu zodzitukumula ndi zonyoza Mulungu. Chinapatsidwanso mphamvu yochita zimene chikufuna kwa miyezi 42.+  Chilombocho chinatsegula pakamwa pake nʼkumanyoza+ Mulungu. Chinkanyoza dzina lake, malo ake okhala komanso amene akukhala kumwamba.+  Chinaloledwa kumenyana ndi oyerawo nʼkuwagonjetsa.+ Chinapatsidwanso ulamuliro pa anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse, chilankhulo chilichonse ndi dziko lililonse.  Anthu amene akukhala padziko lapansi adzachilambira. Kuchokera pamene dziko linakhazikitsidwa, anthu amenewa mayina awo sanalembedwe mumpukutu wa moyo+ wa Mwanawankhosa amene anaphedwa.+  Aliyense amene ali ndi makutu amve.+ 10  Ngati wina akuyenera kutengedwa kupita ku ukapolo, adzapitadi ku ukapoloko. Aliyense wopha munthu ndi lupanga, nayenso adzaphedwa ndi lupanga.*+ Apa mʼpamene oyera+ akufunika kupirira+ ndiponso kukhala ndi chikhulupiriro.+ 11  Kenako ndinaona chilombo china chikutuluka pansi pa dziko lapansi. Chinali ndi nyanga ziwiri ngati mwana wa nkhosa, koma chinayamba kulankhula ngati chinjoka.+ 12  Chilombocho chinalamulira ndi mphamvu zofanana ndi za chilombo choyambacho,+ chilombo choyambacho chikuona. Chinachititsa kuti dziko lapansi ndi amene akukhala mmenemo alambire chilombo choyamba chija, chimene bala lake limene chinayenera kufa nalo, linapola.+ 13  Chinachitanso zizindikiro zazikulu, moti chinapangitsa kuti moto ugwere padziko lapansi kuchokera kumwamba, anthu akuona. 14  Chilombocho chinasocheretsa anthu amene akukhala padziko lapansi chifukwa cha zizindikiro zimene chinaloledwa kuchita pamaso pa chilombo choyamba chija. Chinauzanso amene akukhala padziko lapansi kuti apange chifaniziro+ cha chilombo chimene chinali ndi bala la lupanga chija, koma sichinafe.+ 15  Ndipo chinaloledwa kupereka mpweya* kwa chifaniziro cha chilombo chija, kuti chifaniziro cha chilombocho chithe kulankhula komanso kuchititsa kuti onse amene akukana kulambira chifaniziro cha chilombocho aphedwe. 16  Chilombocho chinakakamiza anthu onse, olemekezeka ndi onyozeka, olemera ndi osauka, mfulu ndi akapolo, kuti aikidwe chizindikiro padzanja lawo lamanja kapena pachipumi pawo.+ 17  Chinachita zimenezi kuti aliyense asathe kugula kapena kugulitsa, kupatulapo ngati ali ndi chizindikirocho, dzina+ la chilombo kapena nambala ya dzina lake.+ 18  Apa mʼpamene pakufunika nzeru: Amene ali ndi nzeru awerengere nambala ya chilombocho, chifukwa ndi nambala ya munthu. Nambala yake ndi 666.+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “Ngati wina akuyenera kuphedwa ndi lupanga, aphedwe ndi lupanga.”
Kapena kuti, “mzimu.”