Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira 15:1-8

  • Angelo 7 amene anali ndi miliri 7 (1-8)

    • Nyimbo ya Mose komanso ya Mwanawankhosa (3, 4)

15  Ndinaona chizindikiro china kumwamba, chachikulu ndi chodabwitsa. Chizindikiro chimenechi chinali angelo 7+ amene anali ndi miliri 7. Miliri imeneyi ndi yomaliza chifukwa ikamatha, mkwiyo wa Mulungu udzakhalanso utatha.+  Kenako ndinaona chinachake chooneka ngati nyanja yagalasi+ yosakanikirana ndi moto. Ndipo amene anagonjetsa+ chilombo chija, chifaniziro chake+ ndi nambala ya dzina lake+ anali ataima pambali pa nyanja yagalasiyo, atanyamula azeze a Mulungu.  Iwo ankaimba nyimbo ya Mose+ kapolo wa Mulungu ndi nyimbo ya Mwanawankhosa+ yakuti: “Ntchito zanu nʼzazikulu ndi zodabwitsa,+ inu Yehova* Mulungu Wamphamvuyonse.+ Njira zanu ndi zolungama komanso zoona,+ inu Mfumu yamuyaya.+  Popeza inu nokha Yehova* ndinu wokhulupirika, ndi ndani amene sadzakuopani komanso kulemekeza dzina lanu?+ Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzalambira pamaso panu,+ chifukwa iwo adziwa malamulo anu olungama.”  Zimenezi zitatha, ndinaona malo opatulika amʼchihema cha umboni+ atatsegulidwa kumwamba.+  Ndipo angelo 7 amene anali ndi miliri 7+ aja anatuluka kumalo opatulikawo, atavala zovala zoyera ndi zowala komanso atamanga malamba agolide pazifuwa zawo.  Ndiyeno mmodzi wa angelo 4 aja anapereka kwa angelo 7 amenewo mbale zagolide 7 zodzaza ndi mkwiyo wa Mulungu,+ amene adzakhala ndi moyo mpaka kalekale.  Mʼmalo opatulikawo munadzaza utsi chifukwa cha ulemerero wa Mulungu+ ndiponso chifukwa cha mphamvu zake. Palibe amene anatha kulowa mʼmalo opatulikawo mpaka miliri 7+ ya angelo 7 aja itatha.

Mawu a M'munsi